Salimo 62:1-12

  • Chipulumutso chenicheni chimachokera kwa Mulungu

    • “Ndikuyembekezera Mulungu modekha” (1, 5)

    • ‘Mukhuthulireni Mulungu zonse zamumtima mwanu’ (8)

    • Anthu ali ngati mpweya (9)

    • Musamadalire chuma (10)

Kwa wotsogolera nyimbo. Aimbe nyimboyi pa Yedutuni.* Nyimbo ya Davide. 62  Ndithudi, ndikuyembekezera* Mulungu modekha. Chipulumutso changa chimachokera kwa iye.+   Iye ndi thanthwe langa komanso ndi amene amandipulumutsa, malo anga othawirako otetezeka.*+Sindidzagwedezeka kwambiri.+   Kodi mudzamenya munthu kuti mumuphe mpaka liti?+ Nonsenu ndinu oopsa ngati khoma lopendekeka, khoma lamiyala limene latsala pangʼono kugwa.   Iwo amakambirana kuti amuchotse pa udindo wake wapamwamba.*Bodza limawasangalatsa. Iwo amadalitsa ndi pakamwa pawo, koma mumtima mwawo amakhala akutemberera.+ (Selah)   Ndithudi, ndikuyembekezera Mulungu modekha*+Chifukwa chiyembekezo changa chimachokera kwa iye.+   Ndithudi, iye ndi thanthwe langa komanso amene amandipulumutsa, malo anga othawirako otetezeka.Sindidzagwedezeka.+   Chipulumutso ndi ulemerero wanga zimachokera kwa Mulungu. Mulungu ndi thanthwe langa lolimba ndi malo anga othawirako.+   Muzimudalira nthawi zonse, anthu inu. Mukhuthulireni zonse zamumtima mwanu.+ Mulungu ndi malo athu othawirako.+ (Selah)   Ana a anthu ali ngati mpweya,Ana a anthu ndi malo othawirako osadalirika.+ Onse pamodzi akaikidwa pasikelo amapepuka kuposa mpweya.+ 10  Musadalire chizolowezi chobera ena mwachinyengo,Kapena kudalira uchifwamba. Ngati chuma chanu chachuluka, mtima wanu usakhale pachumacho.+ 11  Kawiri konse ndamva Mulungu akunena kuti: Mphamvu ndi za Mulungu.+ 12  Komanso chikondi chokhulupirika ndi chanu, inu Yehova,+Chifukwa inu mumabwezera aliyense mogwirizana ndi zochita zake.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “moyo wanga ukuyembekezera.”
Kapena kuti, “malo okwezeka achitetezo.”
Kapena kuti, “pa ulemelero wake.”
Kapena kuti, “yembekezera Mulungu modekha, iwe moyo wanga.”