Salimo 63:1-11

  • Kulakalaka Mulungu

    • “Chikondi chanu chokhulupirika nʼchabwino kuposa moyo” (3)

    • “Ndakhutira ndi gawo labwino” (5)

    • Ndimaganizira mozama za Mulungu usiku (6)

    • ‘Ndimakhala pafupi kwambiri ndi Mulungu’ (8)

Nyimbo ya Davide, pamene anali mʼchipululu cha Yuda.+ 63  Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ine ndikukufunafunani.+ Ine ndikulakalaka inu.*+ Ndalefuka* chifukwa cholakalaka inuMʼdziko louma komanso lopanda madzi, kumene sikumera chilichonse.+   Choncho ndakuonani mʼmalo oyera.Ndaona mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.+   Chifukwa chikondi chanu chokhulupirika nʼchabwino kuposa moyo,+Milomo yanga idzakulemekezani.+   Choncho ndidzakutamandani moyo wanga wonse.Ndidzapemphera mʼdzina lanu nditakweza manja anga.   Ndakhutira* ndi gawo labwino komanso losangalatsa kwambiri,*Choncho milomo yanga idzakutamandani pofuula mosangalala.+   Ndimakukumbukirani ndili pabedi langa,Ndimaganizira mozama za inu usiku wonse.*+   Chifukwa inu mumandithandiza,+Ndipo ndimafuula mosangalala mumthunzi wa mapiko anu.+   Ndimakhala* nanu pafupi kwambiri.Dzanja lanu lamanja limandigwira mwamphamvu.+   Koma amene akufuna kuwononga moyo wanga*Adzatsikira kumanda. 10  Adzaphedwa ndi lupanga,Adzakhala chakudya cha nkhandwe. 11  Koma mfumu idzasangalala ndi zimene Mulungu adzaichitire. Munthu aliyense wolumbira mʼdzina la Mulungu adzasangalala kwambiri,*Chifukwa pakamwa pa anthu olankhula zabodza padzatsekedwa.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Moyo wanga ukulakalaka inu.”
Kapena kuti, “Thupi langa lalefuka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi mafuta komanso kunenepa.”
Kapena kuti, “Moyo wanga wakhutira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pa maulonda a usiku.”
Kapena kuti, “Moyo wanga umakhala.”
Kapena kuti, “akufuna kundipha.”
Kapena kuti, “adzadzitamandira.”