Salimo 64:1-10

  • Nditetezeni ku ziwembu zobisika

    • “Mulungu adzawalasa” (7)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. 64  Inu Mulungu, imvani mawu anga pamene ndikukuchondererani.+ Tetezani moyo wanga ku zinthu zoopsa zimene mdani akuchita.   Ndibiseni ku ziwembu zachinsinsi za anthu oipa,+Kwa gulu la anthu ochita zoipa.   Iwo amanola lilime lawo ngati lupanga.Amakonzekera kuponya mawu awo opweteka ngati mivi,   Kuti alase munthu wosalakwa atamubisalira.Amamulasa modzidzimutsa ndiponso mopanda mantha.   Amaumirira kuti akwaniritse zolinga zawo zoipa,*Amakambirana zimene angachite kuti abise misampha yawo. Iwo amanena kuti: “Angaione ndani?”+   Amafufuza njira zatsopano zochitira zinthu zoipa.Mwachinsinsi amakonza njira zochitira ziwembu zawo mochenjera.+Zimene munthu aliyense akuganiza mumtima mwake, nʼzovuta kuzimvetsa.   Koma Mulungu adzawalasa ndi muvi.+Adzavulazidwa ndi muvi modzidzimutsa.   Adzawonongedwa chifukwa cha zolankhula za lilime lawo lomwe,+Onse amene adzaone zimenezi adzapukusa mitu yawo.   Ndiyeno anthu onse adzachita mantha,Ndipo adzalengeza zimene Mulungu wachita,Iwo adzamvetsa bwino zimene iye amachita.+ 10  Wolungama adzasangalala chifukwa cha Yehova ndipo adzathawira kwa iye.+Onse owongoka mtima adzasangalala kwambiri.*

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Amalimbikitsana kuti achite zoipa.”
Kapena kuti, “adzadzitamandira.”