Salimo 66:1-20

  • Ntchito zochititsa mantha za Mulungu

    • ‘Bwerani mudzaone ntchito za Mulungu’ (5)

    • “Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa inu” (13)

    • Mulungu amamva mapemphero (18-20)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo. 66  Dziko lonse lapansi lifuule mosangalala ndipo litamande Mulungu.+   Imbani nyimbo zotamanda dzina lake laulemerero. Mʼpatseni ulemerero ndipo mumutamande.+   Muuzeni Mulungu kuti: “Ntchito zanu ndi zochititsadi mantha!+ Chifukwa cha mphamvu zanu zazikulu,Adani anu adzabwera kwa inu mwamantha.+   Anthu onse padziko lapansi adzakugwadirani.+Adzaimba nyimbo zokutamandani,Adzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”+ (Selah)   Bwerani mudzaone ntchito za Mulungu. Zimene wachitira ana a anthu ndi zochititsa mantha.+   Anasandutsa nyanja kukhala malo ouma,+Anthu anawoloka mtsinje poyenda ndi mapazi awo.+ Pamenepo tinasangalala chifukwa cha zimene Mulungu anatichitira.+   Iye akulamulira ndi mphamvu zake mpaka kalekale.+ Maso ake akuyangʼanitsitsa mitundu ya anthu.+ Anthu osamvera asadzikweze.+ (Selah)   Tamandani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthu,+Mutamandeni mofuula.   Iye amatithandiza kuti tikhalebe ndi moyo,+Salola kuti mapazi athu apunthwe.*+ 10  Chifukwa inu Mulungu mwatifufuza.+Mwatiyenga ngati mmene amayengera siliva. 11  Mwatikola ndi ukonde wanu wosakira nyama,Mwatisenzetsa katundu wolemera kwambiri.* 12  Munalola kuti munthu wamba atipondeponde.*Tinadutsa pamoto ndi pamadzi,Kenako munatibweretsa pamalo ampumulo. 13  Ndidzalowa mʼnyumba yanu ndi nsembe zopsereza zathunthu.+Ine ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa inu+ 14  Amene milomo yanga inalonjeza,+Ndiponso amene pakamwa panga pananena pa nthawi imene ndinali pamavuto aakulu. 15  Ndidzapereka kwa inu nsembe zopsereza za nyama zonenepa,Ndidzapereka nsembe nkhosa zamphongo. Ndidzapereka ngʼombe zamphongo pamodzi ndi mbuzi zamphongo. (Selah) 16  Bwerani mudzamve, inu nonse amene mumaopa Mulungu,Ndipo ine ndidzakuuzani zimene wandichitira.+ 17  Ndinamuitana ndi pakamwa panga,Ndipo ndinamutamanda ndi lilime langa. 18  Ngati mumtima mwanga ndikanakhala ndi maganizo aliwonse oti ndichitire munthu zoipa,Yehova sakanandimvetsera.+ 19  Koma Mulungu anamva.+Anamvetsera pemphero langa mwatcheru.+ 20  Atamandike Mulungu, amene sananyalanyaze pemphero langaKapena kulephera kundisonyeza chikondi chake chokhulupirika.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “tiyende dzandidzandi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼchiuno mwathu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “atipondeponde ndi mahatchi awo.”