Salimo 67:1-7

  • Kuchokera kumalekezero a dziko lapansi anthu adzaopa Mulungu

    • Njira za Mulungu zidzadziwika (2)

    • ‘Mitundu yonse ya anthu itamande Mulungu’ (3, 5)

    • “Mulungu adzatidalitsa” (6, 7)

Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Nyimbo ndi Salimo. 67  Mulungu adzatikomera mtima ndi kutidalitsa.Iye adzasonyeza kuti akusangalala nafe+ (Selah)   Kuti njira zanu zidziwike padziko lonse lapansi,+Kuti mitundu yonse ya anthu idziwe kuti ndinu Mpulumutsi.+   Inu Mulungu, mitundu ya anthu ikutamandeni,Ndithu mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.   Mitundu ya anthu isangalale ndi kufuula mokondwera,+Chifukwa inu mudzaweruza anthu mwachilungamo.+ Mudzatsogolera mitundu ya anthu padziko lapansi. (Selah)   Inu Mulungu, mitundu ya anthu ikutamandeni,Ndithu mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.   Dziko lapansi lidzapereka zipatso zake.+Mulungu, ndithu Mulungu wathu, adzatidalitsa.+   Mulungu adzatidalitsa,Ndipo anthu onse apadziko lapansi adzamuopa.*+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “adzamulemekeza.”