Salimo 7:1-17

  • Yehova ndi Woweruza wolungama

    • “Ndiweruzeni inu Yehova” (8)

Nyimbo yoimba polira imene Davide anaimbira Yehova, yokhudza mawu a Kusi wa fuko la Benjamini. 7  Inu Yehova Mulungu wanga, ine ndathawira kwa inu.+ Ndipulumutseni kwa anthu onse amene akundizunza ndipo mundilanditse.+   Mukapanda kutero andikhadzulakhadzula ngati mmene mkango umachitira,+Nʼkunditenga popanda wondipulumutsa.   Inu Yehova Mulungu wanga, ngati ndalakwitsa chilichonse,Ngati ndachita zinthu mopanda chilungamo,   Ngati ndachita zoipa kwa munthu amene akundichitira zabwino,+Kapena ngati mdani wanga ndamulanda zinthu zake popanda chifukwa,*   Mdani wanga andithamangitse nʼkundipeza,Andigwetsere pansi nʼkundipondaponda mpaka kufaNdipo andisiye nditagona pafumbi mwamanyazi. (Selah)   Nyamukani mutakwiya, inu Yehova.Imirirani ndi kukhaulitsa adani anga amene andikwiyira.+Dzukani nʼkundithandiza, ndipo mulamule kuti chilungamo chichitike.+   Mitundu ya anthu ikuzungulireni,Ndipo inu muwaweruze muli kumwambako.   Yehova adzapereka chigamulo kwa mitundu ya anthu.+ Ndiweruzeni inu Yehova, mogwirizana ndi chilungamo changaKomanso mogwirizana ndi kukhulupirika kwanga.+   Chonde, thetsani zinthu zoipa zimene anthu oipa akuchita. Koma muchititse kuti wolungama akhale wolimba,+Chifukwa inu ndinu Mulungu wolungama+ amene amayeza mitima+ komanso mmene munthu akumvera mumtima.*+ 10  Mulungu ndi chishango changa,+ Mpulumutsi wa anthu owongoka mtima.+ 11  Mulungu ndi Woweruza wolungama,+Ndipo Mulungu amapereka zigamulo kwa* oipa tsiku lililonse. 12  Ngati munthu sakulapa,+ Mulungu amanola lupanga lake,+Amakunga uta wake nʼkukonzekera kulasa.+ 13  Iye amakhala wokonzeka kugwiritsa ntchito zida zake zoopsa,Amakhala wokonzeka kugwiritsa ntchito mivi yake yoyaka moto.+ 14  Taonani munthu amene ali ndi pakati pa zinthu zoipa,Watenga pakati pa mavuto ndipo adzabereka mabodza.+ 15  Iye wakumba dzenje ndipo walizamitsa,Koma adzagwera mʼdzenje limene wakumba yekhalo.+ 16  Mavuto amene akuwayambitsawo adzabwerera pamutu pake,+Zinthu zachiwawa zimene akuchita zidzagwera paliwombo pake. 17  Ndidzatamanda Yehova chifukwa cha chilungamo chake.+Ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina la Yehova+ Wamʼmwambamwamba.+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “Ngati ndamulanditsa wondisautsa popanda chifukwa.”
Kapena kuti, “amayeza mitima ndi impso.”
Kapena kuti, “amadzudzula mwamphamvu.”