Salimo 74:1-23

  • Pemphero lopempha kuti Mulungu akumbukire anthu ake

    • Anakumbukira zimene Mulungu anachita kuti awapulumutse (12-17)

    • “Kumbukirani mmene adani akunyozera” (18)

Masikili.* Salimo la Asafu.+ 74  Inu Mulungu, nʼchifukwa chiyani mwatikana mpaka kalekale?+ Nʼchifukwa chiyani mkwiyo wanu ukuyakira* nkhosa zimene mukuweta?+   Kumbukirani anthu* amene munawatenga kalekale kuti akhale anu,+Fuko limene munaliwombola kuti likhale cholowa chanu.+ Kumbukirani phiri la Ziyoni kumene inu mumakhala.+   Pitani kumalo amene akhala owonongeka kuyambira kalekale.+ Mdani wawononga chilichonse mʼmalo opatulika.+   Adani anu afuula mosangalala mʼmalo anu olambiriramo.*+ Aikamo mbendera zawo kuti zikhale zizindikiro.   Anali ngati anthu amene akugwetsa mitengo ndi nkhwangwa mʼnkhalango yowirira.   Anagumula zinthu zojambula mochita kugoba zamʼmakoma a malo opatulika+ ndi nkhwangwa komanso ndodo zachitsulo.   Anawotcha malo anu opatulika.+ Anaipitsa chihema chokhala ndi dzina lanu nʼkuchigwetsera pansi.   Iwo limodzi ndi ana awo ananena mumtima mwawo kuti: “Malo onse amene anthu amalambirirako Mulungu mʼdzikoli, ayenera kutenthedwa.”   Kulibe zizindikiro zathu zoti tizione.Kulibenso mneneri wina aliyense amene watsala,Ndipo pakati pathu palibe amene akudziwa kuti zimenezi zikhala chonchi kwa nthawi yayitali bwanji. 10  Inu Mulungu, kodi mdani adzapitiriza kunyoza mpaka liti?+ Kodi mdani adzachitira mwano dzina lanu mpaka kalekale?+ 11  Nʼchifukwa chiyani mwabweza dzanja lanu, dzanja lanu lamanja?+ Lichotseni pachifuwa panu ndipo muwawononge. 12  Koma Mulungu ndi Mfumu yanga kuyambira kalekale,Iye ndi amene amapulumutsa anthu padziko lapansi.+ 13  Inu munavundula nyanja ndi mphamvu zanu.+Munaphwanya mitu ya zilombo zamʼnyanja. 14  Inu munaphwanya mitu ya Leviyatani.*Munamupereka kwa anthu kuti akhale chakudya kwa anthu amene amakhala mʼzipululu. 15  Inu munangʼamba nthaka nʼkupanga akasupe ndi mitsinje.+Munaumitsa mitsinje imene inkakhala ndi madzi nthawi zonse.+ 16  Masana ndi anu, usikunso ndi wanu. Munapanga kuwala* komanso dzuwa.+ 17  Munaika malire onse a dziko lapansi.+Munapanga nyengo yachilimwe ndi nyengo yachisanu.+ 18  Inu Yehova, kumbukirani mmene adani akunyozera,Mmene anthu opusa akuchitira mwano dzina lanu.+ 19  Musapereke moyo wa njiwa yanu kwa zilombo zakuthengo. Musaiwale kwamuyaya moyo wa anthu anu ovutika. 20  Kumbukirani pangano lanu,Chifukwa anthu achiwawa amabisalira anzawo mʼmalo amdima apadziko lapansi. 21  Musalole kuti munthu woponderezedwa abwerere mokhumudwa.+Anthu onyozeka komanso osauka atamande dzina lanu.+ 22  Nyamukani inu Mulungu, ndipo mudziteteze pa mlandu wanu. Kumbukirani mmene munthu wopusa wakunyozerani tsiku lonse.+ 23  Musaiwale zimene adani anu akunena. Phokoso la anthu amene amakutsutsani likukwera kumwamba nthawi zonse.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ukufukira utsi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “msonkhano wanu.”
Kapena kuti, “mʼmalo anu ochitiramo misonkhano.”
Kapena kuti, “zounikira.”