Salimo 76:1-12

  • Mulungu wagonjetsa adani a Ziyoni

    • Mulungu amapulumutsa anthu ofatsa (9)

    • Adani onyada adzachititsidwa manyazi (12)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+ 76  Mulungu ndi wodziwika mu Yuda.+Dzina lake ndi lalikulu mu Isiraeli.+   Tenti yake ili ku Salemu,+Malo ake okhala ali ku Ziyoni.+   Kumeneko anathyola mivi yoyaka moto,Anathyolanso chishango, lupanga ndi zida zankhondo.+ (Selah)   Inu mumawala kwambiri.*Ndinu waulemerero kuposa mapiri amene muli nyama zodya zinzake.   Anthu olimba mtima alandidwa zinthu zawo.+ Iwo agona tulo,Asilikali onse analibe mphamvu.+   Chifukwa cha kudzudzula kwanu, inu Mulungu wa Yakobo,Hatchi komanso wokwera galeta, onse agona tulo tofa nato.+   Inu nokha ndinu wochititsa mantha.+ Ndi ndani angapirire mkwiyo wanu waukulu?+   Munapereka chiweruzo muli kumwamba.+Dziko lapansi linachita mantha ndipo linakhala chete+   Pamene Mulungu ananyamuka kuti apereke chiweruzo,Kuti apulumutse anthu onse ofatsa apadziko lapansi.+ (Selah) 10  Chifukwa mkwiyo wa munthu udzachititsa kuti mutamandidwe.+Mudzadzikongoletsa ndi mkwiyo wawo wotsala. 11  Chitani malonjezo anu kwa Yehova Mulungu wanu ndipo muwakwaniritse+Anthu onse amene amuzungulira abweretse mphatso zawo mwamantha.+ 12  Mulungu adzachititsa manyazi atsogoleri onyada.Iye amachititsa kuti mafumu apadziko lapansi akhale ndi mantha.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Mwazunguliridwa ndi kuwala.”