Salimo 77:1-20
Kwa wotsogolera nyimbo. Aimbe nyimboyi pa Yedutuni.* Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+
77 Ndidzafuulira Mulungu,Ndithu, ndidzafuulira Mulungu, ndipo iye adzandimvetsera.+
2 Pa tsiku limene ndakumana ndi mavuto ndimafunafuna Yehova.+
Usiku ndimakweza manja anga kwa iye ndipo sindisiya.*
Palibe chimene chimanditonthoza.
3 Ndikakumbukira Mulungu ndimabuula.+Ndimavutika kwambiri mumtima ndipo mphamvu zanga zimatha.*+ (Selah)
4 Mumatsegula zikope zanga.Ndavutika mumtima, moti sindingathe kulankhula.
5 Ndikuganizira masiku akale,+Ndikuganizira zaka zakale kwambiri.
6 Usiku ndimakumbukira nyimbo yanga.*+Ndimaganiza mumtima mwanga,+Ndipo ndimafufuza mwakhama.
7 Kodi Yehova adzatitaya mpaka kalekale?+
Kodi sadzatisonyezanso kukoma mtima kwake?+
8 Kodi chikondi chake chokhulupirika chatha mpaka kalekale?
Kodi malonjezo ake sadzakwaniritsidwa ku mibadwomibadwo?
9 Kodi Mulungu waiwala kusonyeza kukoma mtima kwake,+Kapena kodi mkwiyo wake wachititsa kuti chifundo chake chithe? (Selah)
10 Kodi ndizingonena kuti: “Zimene zikundivutitsa* ndi zakuti:+
Wamʼmwambamwamba wasiya kutithandiza”?
11 Ndidzakumbukira ntchito za Ya,Ndidzakumbukira zochita zanu zodabwitsa zakale.
12 Ndidzaganizira mozama za ntchito zanu zonse,Ndipo ndiziganizira mwakuya zochita zanu.+
13 Inu Mulungu, njira zanu ndi zoyera.
Kodi pali mulungu winanso wamkulu amene angafanane ndi inu Mulungu?+
14 Inu ndinu Mulungu woona amene mumachita zinthu zodabwitsa.+
Mwasonyeza ku mitundu ya anthu kuti ndinu wamphamvu.+
15 Ndi mphamvu zanu* mwapulumutsa* anthu anu,+Ana aamuna a Yakobo ndi a Yosefe. (Selah)
16 Madzi anakuonani, inu Mulungu,Madzi anakuonani ndipo anavutika.+
Ndipo madzi akuya anayamba kuvutika kwambiri.
17 Mitambo inagwetsa madzi.
Mʼmitambo yakuda munamveka mabingu,Ndipo mphezi zanu zinawala paliponse ngati mivi.+
18 Phokoso la bingu lanu+ linali ngati la mawilo a galeta.Kungʼanima kwa mphezi kunaunika padziko lapansi.+Dziko lapansi linanjenjemera komanso kugwedezeka.+
19 Msewu wanu unadutsa panyanja,+Ndipo njira yanu inadutsa pamadzi ambiri.Koma palibe amene anatha kuzindikira mmene mapazi anu anaponda.
20 Munatsogolera anthu anu ngati nkhosa,+Kudzera mwa Mose ndi Aroni.+
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “sindichita dzanzi.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mzimu wanga umakomoka.”
^ Kapena kuti, “nyimbo yoimbidwa ndi zingwe.”
^ Kapena kuti, “zikundilasa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “dzanja lanu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mwawombola.”