Salimo 78:1-72

  • Mulungu ankasamalira Aisiraeli koma iwo analibe chikhulupiriro

    • Mudzauze mʼbadwo wamʼtsogolo (2-8)

    • “Sanakhulupirire Mulungu” (22)

    • “Tirigu wochokera kumwamba” (24)

    • “Ankachititsa kuti Woyera wa Isiraeli amve chisoni” (41)

    • Kuchoka ku Iguputo kupita ku Dziko Lolonjezedwa (43-55)

    • ‘Iwo anapitiriza kuyesa Mulungu’ (56)

Masikili.* Salimo la Asafu.+ 78  Inu anthu anga, mvetserani chilamulo changa.*Tcherani khutu ku mawu apakamwa panga.   Ndidzatsegula pakamwa panga nʼkunena mwambi. Ndidzanena mawu ophiphiritsa akalekale.+   Zinthu zimene tinamva ndipo tikuzidziwa,Zimene makolo athu anatifotokozera,+   Sitidzazibisa kwa ana awo.Tidzafotokozera mʼbadwo wamʼtsogolo+Tidzawafotokozera zinthu zotamandika zimene Yehova anachita komanso mphamvu zake,+Zinthu zodabwitsa zimene wachita.+   Mulungu anaika chikumbutso pakati pa ana a Yakobo,Ndipo anaika chilamulo mu Isiraeli.Iye analamula makolo athuKuti auze ana awo zinthu zimenezi,+   Kuti mʼbadwo wotsatira,Ana amene adzabadwe mʼtsogolo, adzadziwe zimenezi.+ Nawonso adzazifotokoze kwa ana awo.+   Zikadzatero anawo azidzadalira Mulungu. Sadzaiwala ntchito za Mulungu+Koma azidzasunga malamulo ake.+   Akadzachita zimenezi sadzakhala ngati makolo awo,Mʼbadwo wosamva komanso wopanduka,+Mʼbadwo umene mtima wawo unali wosakhazikika*+Komanso wosakhulupirika kwa Mulungu.   Anthu a fuko la Efuraimu anali ndi mauta,Koma anathawa pa tsiku lankhondo. 10  Iwo sanasunge pangano la Mulungu,+Ndipo anakana kutsatira chilamulo chake.+ 11  Iwo anaiwalanso zimene anachita,+Ntchito zake zodabwitsa zimene anawaonetsa.+ 12  Mulungu anachita zodabwitsa pamaso pa makolo awo,+Mʼdziko la Iguputo, mʼdera la Zowani.+ 13  Iye anagawa nyanja kuti iwo awoloke,Ndipo anaimitsa madzi nʼkukhala ngati khoma.+ 14  Iye ankawatsogolera ndi mtambo masanaNdipo usiku wonse ankawatsogolera ndi kuwala kwa moto.+ 15  Iye anangʼamba miyala mʼchipululu,Anawalola kumwa madziwo mpaka ludzu kutha ngati kuti akumwa madzi amʼnyanja.+ 16  Iye anatulutsa madzi ochuluka pathanthwe,Ndipo anachititsa madzi ambiri kuti ayende ngati mitsinje.+ 17  Koma iwo anapitiriza kumuchimwiraPopandukira Wamʼmwambamwamba mʼchipululu.+ 18  Iwo anayesa Mulungu mʼmitima yawo+Pomuumiriza kuti awapatse chakudya chimene ankalakalaka. 19  Choncho iwo analankhula mawu amwano kwa MulunguKuti: “Kodi Mulungu angathe kutipatsa chakudya mʼchipululu muno?”+ 20  Iye anamenya thanthweMoti panatuluka madzi ambiri ndipo mitsinje inasefukira.+ Koma iwo anati: “Kodi angathenso kutipatsa chakudya,Kapena kodi angapatse anthu ake nyama?”+ 21  Yehova atamva zimene ankanenazo anakwiya kwambiri.+Moto+ unayakira Yakobo,Ndipo mkwiyo wake unayakira Isiraeli+ 22  Chifukwa chakuti sanakhulupirire Mulungu.+Sanakhulupirire kuti iye angathe kuwapulumutsa. 23  Choncho Mulungu analamula mitambo yamumlengalenga,Ndipo anatsegula zitseko zakumwamba. 24  Iye anapitiriza kuwagwetsera mana ngati mvula kuti adye.Anawapatsa tirigu wochokera kumwamba.+ 25  Anthu anadya chakudya cha amphamvu.*+Iye anawapatsa chakudya chokwanira.+ 26  Anachititsa kuti mphepo yakumʼmawa iwombe mumlengalenga,Komanso ndi mphamvu zake, anachititsa kuti mphepo yakumʼmwera iwombe.+ 27  Iye anawagwetsera nyama yochuluka ngati fumbi,Anawagwetsera mbalame zochuluka ngati mchenga wamʼmbali mwa nyanja. 28  Anawagwetsera zimenezi mumsasa wawo,Kuzungulira matenti awo onse.* 29  Iwo anadya nʼkukhuta kwambiri.Iye anawapatsa zimene ankalakalaka.+ 30  Koma nkhuli yawo isanathe,Chakudya chawo chidakali mʼkamwa, 31  Mkwiyo wa Mulungu unawayakira.+ Iye anapha amuna amphamvu pakati pawo.+Anapha anyamata a mu Isiraeli. 32  Ngakhale zinali choncho, iwo anapitiriza kumuchimwira,+Ndipo sanakhulupirire ntchito zake zodabwitsa.+ 33  Choncho anathetsa masiku a moyo wawo ngati mpweya,+Ndipo anawabweretsera masoka amene anachititsa kuti afe mwadzidzidzi. 34  Nthawi zonse akayamba kuwapha, iwo ankamufunafuna.+Iwo ankabwerera nʼkuyamba kufunafuna Mulungu, 35  Chifukwa choti ankakumbukira kuti Mulungu anali Thanthwe lawo,+Ndiponso kuti Mulungu Wamʼmwambamwamba anali Wowawombola.*+ 36  Koma iwo ankafuna kumupusitsa ndi pakamwa pawoKomanso kumunamiza ndi lilime lawo. 37  Mtima wawo sunali wokhulupirika kwa iye.+Ndipo iwo sanali okhulupirika ku pangano lake.+ 38  Koma ankawamvera chifundo.+Ankawakhululukira* machimo awo ndipo sankawawononga.+ Nthawi zambiri ankabweza mkwiyo wake+Mʼmalo moonetsa ukali wake wonse. 39  Iye ankakumbukira kuti iwo ndi anthu athupi la nyama,+Ali ngati mphepo imene imadutsa ndipo sibwereranso.* 40  Nthawi zambiri iwo ankamupandukira mʼchipululu,+Ndipo ankamukhumudwitsa mʼchipululumo!+ 41  Ankayesa Mulungu mobwerezabwereza,+Ndipo ankachititsa kuti Woyera wa Isiraeli amve chisoni.* 42  Iwo sanakumbukire mphamvu za* Mulungu,Tsiku limene anawapulumutsa* kwa mdani wawo,+ 43  Sanakumbukire mmene anasonyezera zizindikiro zake ku Iguputo,+Komanso zinthu zodabwitsa zimene anachita mʼdera la Zowani, 44  Sanakumbukirenso mmene anasandutsira madzi amʼngalande zotuluka mumtsinje wa Nailo kukhala magazi,+Moti sanathe kumwa madziwo. 45  Mulungu anawatumizira ntchentche zoluma kuti ziwasowetse mtendere,+Komanso achule kuti awawononge.+ 46  Anapereka zokolola zawo kwa dzombe lowononga,Anapereka zipatso za ntchito yawo kwa dzombe lochuluka.+ 47  Anawononga mitengo yawo ya mpesa+Komanso mitengo yawo ya mkuyu ndi matalala. 48  Anapha nyama zawo zonyamula katundu pogwiritsa ntchito matalala,+Ndiponso ziweto zawo ndi mphezi. 49  Anawasonyeza mkwiyo wake woyaka moto,Komanso ukali wake ndipo anawabweretsera mavuto,Anawatumizira magulu a angelo kuti awabweretsere tsoka. 50  Mkwiyo wake anaulambulira njira. Sanawapulumutse ku imfa,Ndipo anawagwetsera mliri.* 51  Pamapeto pake anapha ana onse oyamba kubadwa a ku Iguputo,+Amene ndi chiyambi cha mphamvu zawo zobereka mʼmatenti a Hamu. 52  Kenako anatulutsa anthu ake mʼdzikolo ngati gulu la nkhosa,+Ndipo anawatsogolera mʼchipululu ngati nkhosa. 53  Anawatsogolera ndi kuwateteza,Ndipo sanachite mantha.+Nyanja inamiza adani awo.+ 54  Kenako anawalowetsa mʼdziko lake lopatulika,+Mʼdera lamapiri ili limene dzanja lake lamanja linatenga.+ 55  Iye anathamangitsa mitundu ya anthu kuichotsa pamaso pawo.+Iye anawagawira dzikolo kuti likhale cholowa chawo pochita kuwayezera ndi chingwe.+Anachititsa mafuko a Isiraeli kuti akhale mʼnyumba zawozawo.+ 56  Koma iwo anapitiriza kuyesa Mulungu Wamʼmwambamwamba komanso kumupandukira.+Sanamvere zikumbutso zake.+ 57  Iwo anasiyanso Mulungu ndipo ankachita zinthu mwachinyengo ngati makolo awo.+ Anali osadalirika ngati uta wosakunga kwambiri.+ 58  Anapitiriza kumukhumudwitsa ndi malo awo okwezeka,+Ndipo anamukwiyitsa* ndi zifaniziro zawo zogoba.+ 59  Mulungu anamva ndipo anakwiya kwambiri,+Choncho anawakaniratu Aisiraeli. 60  Pamapeto pake anasiya chihema cha ku Silo,+Tenti imene ankakhalamo pakati pa anthu.+ 61  Analola kuti adani atenge chizindikiro cha mphamvu zake,Analola kuti ulemerero wake ukhale mʼmanja mwa adani.+ 62  Iye anapereka anthu ake ku lupanga,+Ndipo anakwiyira cholowa chake. 63  Moto unapsereza anyamata ake,Ndipo anamwali ake sanawaimbire nyimbo zapaukwati.* 64  Ansembe ake anaphedwa ndi lupanga,+Ndipo akazi awo amasiye sanalire.+ 65  Kenako Yehova anadzuka ngati kuti anali mtulo,+Ngati mmene amadzukira munthu wamphamvu+ pambuyo pomwa vinyo wambiri. 66  Iye anathamangitsa adani ake nʼkuwabweza,+Anachititsa kuti adaniwo akhale onyozeka mpaka kalekale. 67  Iye anakana tenti ya Yosefe,Ndipo sanasankhe fuko la Efuraimu. 68  Koma anasankha fuko la Yuda,+Phiri la Ziyoni limene amalikonda.+ 69  Anachititsa kuti malo ake opatulika akhalepo mpaka kalekale ngati kumwamba,*+Ngati dziko lapansi limene analikhazikitsa mpaka kalekale.+ 70  Anasankha Davide+ mtumiki wake,Ndipo anamuchotsa kumakola a nkhosa,+ 71  Kumene ankaweta nkhosa zoyamwitsa,Anamuika kuti akhale mʼbusa wa ana a Yakobo, omwe ndi anthu ake,+Ndi Isiraeli, amene ndi cholowa chake.+ 72  Iye anawaweta ndi mtima wokhulupirika,+Ndipo anawatsogolera mwaluso.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “malangizo anga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wosakonzeka.”
Kapena kuti, “cha angelo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mumsasa wake; mʼmatenti ake.” Kutanthauza a Mulungu kapena a Isiraeli.
Kapena kuti, “Wowabwezerera.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ankaphimba.”
Kapena kuti, “Moyo wawo umapita ndipo subwereranso.”
Kapena kuti, “Ndipo anapweteketsa mtima Woyera wa Isiraeli.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “dzanja la.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anawawombola.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anapereka moyo wawo ku mliri.”
Kapena kuti, “anamuchititsa nsanje.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo anamwali ake sanatamandidwe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Anamanga malo ake opatulika ngati malo okwezeka.”