Salimo 79:1-13

  • Pemphero la pa nthawi imene anthu a mitundu ina anaukira anthu a Mulungu

    • ‘Anthu akutinyoza’ (4)

    • ‘Tithandizeni chifukwa cha dzina lanu’ (9)

    • “Bwezerani anthu oyandikana nafe maulendo 7” (12)

Nyimbo ya Asafu.+ 79  Inu Mulungu, anthu a mitundu ina alowa mʼdziko limene ndi cholowa chanu.+Aipitsa kachisi wanu woyera.+Yerusalemu amusandutsa bwinja.+   Apereka mitembo ya atumiki anu kwa mbalame kuti chikhale chakudya chawoNdipo matupi a anthu anu okhulupirika awapereka kwa zilombo zakutchire.+   Atsanula magazi awo ngati madzi kuzungulira Yerusalemu,Ndipo palibe aliyense amene watsala kuti awaike mʼmanda.+   Anthu oyandikana nafe akutinyoza,+Anthu otizungulira akutiseka komanso kutikuwiza.   Inu Yehova, kodi mukhala wokwiya mpaka liti? Kwamuyaya?+ Kodi mkwiyo wanu ukhala ukuyaka ngati moto mpaka liti?+   Tsanulirani mkwiyo wanu pa mitundu ya anthu amene sakukudziwaniKomanso pa maufumu amene saitana pa dzina lanu.+   Chifukwa iwo awononga mbadwa zonse za YakoboNdipo dziko lawo alisandutsa bwinja.+   Musatiimbe mlandu chifukwa cha zolakwa za makolo athu.+ Tisonyezeni chifundo chanu mofulumira,+Chifukwa zativuta kwambiri.   Tithandizeni inu Mulungu amene mumatipulumutsa,+Chifukwa cha dzina lanu laulemerero.Tipulumutseni komanso mutikhululukire* machimo athu chifukwa cha dzina lanu.+ 10  Musalole kuti anthu a mitundu ina azinena kuti: “Mulungu wawo ali kuti?”+ Anthu a mitundu ina adziwe ife tikuonaKuti mwabwezera magazi a atumiki anu amene anakhetsedwa.+ 11  Imvani kuusa moyo kwa mkaidi.+ Gwiritsani ntchito mphamvu zanu zazikulu* kupulumutsa anthu amene aweruzidwa kuti aphedwe.*+ 12  Bwezerani anthu oyandikana nafe maulendo 7+Chifukwa choti akunyozani, inu Yehova.+ 13  Mukatero, ife anthu anu komanso nkhosa zimene mukuweta,+Tidzakuyamikani mpaka kalekale.Ndipo tidzalengeza kuti inu ndi woyenera kutamandidwa ku mibadwomibadwo.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “muphimbe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “dzanja lanu lalikulu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kupulumutsa ana aamuna a imfa.”