Salimo 8:1-9

  • Ulemerero wa Mulungu komanso ulemu wa munthu

    • “Dzina lanu ndi lalikulu!” (1, 9)

    • “Munthu ndi ndani kuti muzimuganizira?” (4)

    • Munthu munamuveka ulemerero ngati chisoti chachifumu (5)

Kwa wotsogolera nyimbo, pa Gititi.* Nyimbo ya Davide. 8  Inu Yehova Ambuye wathu, dzina lanu ndi lalikulu padziko lonse lapansi,Mwachititsa kuti ulemerero wanu ukhale pamwamba kuposa kumwamba!+   Kudzera mʼmawu otamanda ochokera mʼkamwa mwa ana ndi mwa makanda+Mwasonyeza mphamvu zanu chifukwa cha adani anu,Kuti adani anu komanso amene akufuna kukubwezerani zoipa akhale chete.   Ndikayangʼana kumwamba, ntchito ya zala zanu,Mwezi ndi nyenyezi zimene munapanga,+   Ndimaganiza kuti, munthu ndi ndani kuti muzimuganizira,Ndipo mwana wa munthu ndi ndani kuti muzimusamalira?+   Munamutsitsa pangʼono poyerekeza ndi angelo,*Ndipo munamuveka ulemerero ndi ulemu ngati chisoti chachifumu.   Munamupatsa mphamvu kuti alamulire ntchito za manja anu.+Mwaika zinthu zonse pansi pa mapazi ake:   Nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe zonse,Komanso nyama zakutchire,*+   Mbalame zamumlengalenga komanso nsomba zamʼnyanja,Chilichonse chimene chimasambira mʼnyanja.   Inu Yehova Ambuye wathu, dzina lanu ndi lalikulu padziko lonse lapansi!

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ena okhala ngati Mulungu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “zilombo zakutchire.”