Salimo 81:1-16

  • Anawalimbikitsa kuti akhale omvera

    • Musalambire milungu yachilendo (9)

    • ‘Zikanakhala bwino mukanamvera’ (13)

Kwa wotsogolera nyimbo, pa Gititi.* Salimo la Asafu.+ 81  Fuulani mosangalala kwa Mulungu amene ndi mphamvu yathu.+ Fuulirani Mulungu wa Yakobo mosangalala chifukwa wapambana.   Yambani kuimba nyimbo ndipo tengani maseche,Zeze womveka mosangalatsa pamodzi ndi choimbira cha zingwe.   Pa tsiku limene mwezi watsopano waoneka,+ imbani lipenga la nyanga ya nkhosa,Pa tsiku limene mwezi wathunthu waoneka, imbani lipenga la nyanga ya nkhosa, limene limaimbidwa pa tsiku la chikondwerero.+   Chifukwa limeneli ndi lamulo kwa Isiraeli,Komanso chigamulo cha Mulungu wa Yakobo.+   Mulungu anaika chigamulocho kuti chikhale chikumbutso kwa Yosefe+Pamene ankapita kukapereka chilango mʼdziko la Iguputo.+ Ndinamva mawu amene sindinathe kuwazindikira akuti:*   “Ndinachotsa katundu wolemera paphewa lake.+Manja ake anamasuka moti sankanyamulanso dengu.   Pamene unkakumana ndi mavuto unaitana, ndipo ine ndinakupulumutsa.+Ndinakuyankha ndi mabingu ochokera mumtambo.*+ Ndinakuyesa pamadzi a ku Meriba.*+ (Selah)   Imvani anthu anga, ndipo ine ndipereka umboni wokutsutsani. Inu Aisiraeli, zikanakhala bwino ngati mukanandimvera.+   Pakati panu sipadzakhala mulungu wachilendo,Ndipo simudzagwadira mulungu wachilendo.+ 10  Ine Yehova, ndine Mulungu wanu,Amene ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo.+ Tsegulani kwambiri pakamwa panu ndipo ndidzaikamo chakudya.+ 11  Koma anthu anga sanamvere mawu anga,Isiraeli sanafune kundigonjera.+ 12  Choncho ndinawasiya kuti apitirize kuchita zofuna za mtima wawo wosamverawo.Iwo anachita zimene ankaganiza kuti nʼzoyenera.*+ 13  Zikanakhala bwino ngati anthu anga akanandimvera,+Zikanakhala bwino ngati Isiraeli akanayenda mʼnjira zanga.+ 14  Ndikanagonjetsa adani awo mofulumira,Ndikanalanga adani awo ndi dzanja langa.+ 15  Amene amadana ndi Yehova adzachita mantha pamaso pake,Ndipo zimene zidzawachitikire* zidzakhalapo mpaka kalekale. 16  Koma iye adzakudyetsani tirigu wabwino kwambiri,*+Ndipo adzakupatsani uchi wochokera pathanthwe kuti mudye nʼkukhuta.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “chilankhulo chimene sindinathe kuchizindikira kuti.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmalo obisika a mabingu.”
Kutanthauza, “Kukangana.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Anayenda mʼmalangizo awo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nthawi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzakudyetsani mafuta a tirigu.”