Salimo 87:1-7

  • Ziyoni ndi mzinda wa Mulungu woona

    • Amene anabadwira mu Ziyoni (4-6)

Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+ 87  Maziko a mzinda wa Mulungu ali mʼmapiri opatulika.+   Yehova amakonda kwambiri mageti a Ziyoni+Kuposa matenti onse a Yakobo.   Iwe mzinda wa Mulungu woona, anthu akunena za ulemerero wako.+ (Selah)   Ndidzaika Rahabi* ndi Babulo mʼgulu la amene+ akundidziwa.Filisitiya, Turo ndi Kusi alinso mʼgulu la amene akundidziwa. Ine ndidzati: “Amenewa anabadwira mʼZiyoni.”   Ponena za Ziyoni anthu adzati: “Aliyense anabadwira mmenemo.” Ndipo Wamʼmwambamwamba adzakhazikitsa mzinda umenewo ndi kuulimbitsa.   Powerenga mitundu ya anthu, Yehova adzalengeza kuti: “Amenewa anabadwira mu Ziyoni.” (Selah)   Oimba+ komanso ovina magule amene amavina mozungulira+ adzanena kuti: “Akasupe anga onse ali mwa iwe.”*+

Mawu a M'munsi

Zikuoneka kuti dzina lakuti “Rahabi” likuimira dziko la Iguputo.
Kapena kuti, “Zinthu zanga zonse zimachokera kwa iwe.”