Salimo 88:1-18

  • Pemphero lopempha kuti atetezedwe ku imfa

    • “Moyo wanga wayandikira ku Manda” (3)

    • ‘Mʼmawa uliwonse ndimapemphera kwa inu’ (13)

Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+ Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe potsatira kaimbidwe ka Mahalati* ndipo iimbidwe molandizana. Masikili* ya Hemani+ wa mʼbanja la Zera. 88  Inu Yehova, Mulungu amene amandipulumutsa,+Masana ndimafuulira inu,Ndipo usiku ndimabwera pamaso panu.+   Pemphero langa lifike kwa inu.+Tcherani khutu lanu kuti mumve* kuchonderera kwanga kopempha thandizo.+   Chifukwa moyo wanga wadzaza ndi masoka,+Ndipo moyo wanga wayandikira ku Manda.*+   Anandiika kale mʼgulu la anthu amene akutsikira kudzenje.*+Ndakhala munthu wovutika,*+   Amene wasiyidwa pakati pa anthu akufaNgati anthu ophedwa amene agona mʼmanda,Amene simukuwakumbukiransoKomanso amene sakuthandizidwa ndi inu.*   Mwandiika mʼdzenje lakuya kwambiri,Mʼmalo amdima, mʼphompho lalikulu.   Mkwiyo wanu ukundilemera kwambiri,+Ndipo ndikumva ngati mukundipanikiza ndi mafunde anu amphamvu. (Selah)   Anzanga mwawathamangitsira kutali ndi ine.+Mwandipangitsa kuti ndikhale chinthu chonyansa kwa iwo. Ndakodwa ndipo sindingathe kuthawa.   Diso langa lachita mdima chifukwa cha kuvutika kwanga.+ Ndimaitana inu Yehova tsiku lonse.+Ndimapemphera kwa inu nditakweza manja anga. 10  Kodi mungachitire zinthu zodabwitsa anthu akufa? Kodi anthu akufa amene sangathe kuchita kanthu angadzuke nʼkukutamandani?+ (Selah) 11  Kodi chikondi chanu chokhulupirika chingalengezedwe kumanda?Kodi kukhulupirika kwanu kungalengezedwe mʼmalo a chiwonongeko?* 12  Kodi ntchito zanu zodabwitsa zingadziwike mu mdima?Kapena kodi chilungamo chanu chidzadziwika mʼdziko la anthu oiwalika?+ 13  Koma ine ndimafuulirabe kwa inu Yehova kuti mundithandize,+Mʼmawa uliwonse pemphero langa limafika kwa inu.+ 14  Inu Yehova, nʼchifukwa chiyani mukundikana?+ Nʼchifukwa chiyani mukundibisira nkhope yanu?+ 15  Kuyambira ndili mnyamata,Ndakhala ndikuzunzika komanso kutsala pangʼono kufa.+Ndafooka kwambiri chifukwa cha zinthu zoopsa zimene mwalola kuti ndikumane nazo. 16  Ndafooka chifukwa cha mkwiyo wanu woyaka moto.+Zinthu zochititsa mantha zochokera kwa inu zandiwononga. 17  Zinthu zimene mumachita zandizungulira ngati madzi tsiku lonse.Zanditsekera kuzungulira mbali zonse. 18  Anzanga komanso anthu oyandikana nawo mwawathamangitsira kutali ndi ine.+Malo amdima akhala mnzanga wapamtima.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Weramani ndipo mumvetsere.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “kumanda.”
Kapena kuti, “ngati munthu wopanda mphamvu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi dzanja lanu.”
Kapena kuti, “ku Abadoni.”