Salimo 89:1-52

  • Imbani za chikondi chokhulupirika cha Yehova

    • Anachita pangano ndi Davide (3)

    • Mbadwa za Davide zidzakhalapo mpaka kalekale (4)

    • Wodzozedwa wa Mulungu amanena kuti Mulungu ndi “Bambo” ake (26)

    • Nʼzotsimikizirika kuti pangano la Davide lidzakwaniritsidwa (34-37)

    • Munthu sangapulumutse moyo wake ku mphamvu ya Manda (48)

Masikili.* Salimo la Etani+ wa mʼbanja la Zera. 89  Ndidzaimba mpaka kalekale za mmene Yehova wasonyezera chikondi chake chokhulupirika. Ndidzalengeza ndi pakamwa panga za kukhulupirika kwanu ku mibadwo yonse.   Chifukwa ndanena kuti: “Chikondi chanu chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale,+Ndipo kukhulupirika kwanu kudzakhala kumwamba mpaka kalekale.”   Mulungu anati: “Ndachita pangano ndi wosankhidwa wanga.+Ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga kuti:+   ‘Ndidzachititsa kuti mbadwa* zako zikhalepo mpaka kalekale,+Ndipo ndidzachititsa kuti ufumu* wako ukhalepo ku mibadwo yonse.’”+ (Selah)   Inu Yehova, kumwamba kudzakutamandani chifukwa cha ntchito zanu zodabwitsa,Mpingo wa oyera anu udzakutamandani chifukwa ndinu wokhulupirika.   Ndi ndani kumwamba amene angafanane ndi Yehova?+ Ndi ndani pakati pa ana a Mulungu+ amene ndi wofanana ndi Yehova?   Mulungu ndi wochititsa mantha komanso wolemekezeka pakati pa gulu lake la oyera.*+Iye ndi wamkulu komanso wochititsa mantha kwa onse amene amuzungulira.+   Inu Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba,Ndi ndani ali ndi mphamvu ngati inu Ya?+ Ndinu wokhulupirika pa chilichonse.+   Nyanja ikadzaza mumailamulira.+Mafunde ake akawinduka, inuyo mumawachititsa kuti akhale bata.+ 10  Mwaphwanya Rahabi*+ ngati munthu amene waphedwa.+ Mwabalalitsa adani anu ndi dzanja lanu lamphamvu.+ 11  Kumwamba ndi kwanu, dziko lapansi ndi lanunso.+Nthaka ya dziko lapansi ndiponso zinthu zimene zili mmenemo+ munazipanga ndinu. 12  Munapanga kumpoto ndi kumʼmwera.Mapiri a Tabori+ ndi Herimoni+ amatamanda dzina lanu mosangalala. 13  Mkono wanu ndi wamphamvu,+Dzanja lanu ndi lamphamvu,+Dzanja lanu lamanja lapambana.+ 14  Mukamalamulira, nthawi zonse mumachita zinthu mwachilungamo komanso molungama.+Nthawi zonse mumasonyeza kukhulupirika komanso chikondi chokhulupirika.+ 15  Osangalala ndi anthu amene amakutamandani ndi mawu osangalala.+ Iwo amayenda mʼkuwala kwa nkhope yanu, inu Yehova. 16  Chifukwa cha dzina lanu, iwo amasangalala tsiku lonse,Ndipo amalemekezedwa chifukwa cha chilungamo chanu. 17  Mumachititsa kuti anthu anu akhale amphamvu komanso kuti alemekezedwe,+Ndipo mphamvu* zathu zikuwonjezeka, chifukwa chakuti mukusangalala nafe.+ 18  Chifukwa chishango chathu ndi chochokera kwa Yehova,Ndipo mfumu yathu ndi yochokera kwa Woyera wa Isiraeli.+ 19  Pa nthawi imeneyo munalankhula mʼmasomphenya kwa okhulupirika anu ndipo munati: “Ndapereka nyonga kwa wamphamvu.+Ndakweza wosankhidwa mwapadera pakati pa anthu.+ 20  Ndapeza Davide mtumiki wanga,+Ndipo ndamudzoza ndi mafuta anga opatulika.+ 21  Dzanja langa lidzamuthandiza,+Ndipo mkono wanga udzamulimbitsa. 22  Palibe mdani amene adzamukakamize kuti apereke msonkho,Ndipo palibe munthu woipa amene adzamupondereze.+ 23  Ndidzaphwanya adani ake kuti akhale zidutswazidutswa iye akuona.+Ndipo ndidzapha amene amadana naye.+ 24  Kukhulupirika kwanga komanso chikondi changa chokhulupirika zili pa iye,+Ndipo ndidzachititsa kuti akhale ndi mphamvu* chifukwa cha dzina langa. 25  Ndidzaika ulamuliro wake* panyanjaNdipo ndidzamʼpatsa ulamuliro pamitsinje.+ 26  Iye adzafuula kwa ine kuti: ‘Inu ndinu Bambo anga,Mulungu wanga komanso Thanthwe la chipulumutso changa.’+ 27  Ndipo ndidzamuika kuti akhale ngati mwana woyamba kubadwa,+Ndiponso mfumu yaikulu pa mafumu onse apadziko lapansi.+ 28  Ndidzapitiriza kumusonyeza chikondi changa chokhulupirika mpaka kalekale,+Ndipo pangano limene ndinachita naye silidzaphwanyidwa.+ 29  Ndidzachititsa kuti mbadwa* zake zidzakhalepo kwamuyaya,Ndipo ndidzachititsa kuti mpando wake wachifumu udzakhalepo mpaka kalekale ngati kumwamba.+ 30  Ana ake akadzasiya chilamulo changa,Ndipo akadzaleka kutsatira zigamulo* zanga, 31  Akadzaphwanya mfundo zangaKomanso osasunga malamulo anga, 32  Ine ndidzawalanga ndi ndodo chifukwa cha kusamvera* kwawo,+Ndipo ndidzawakwapula chifukwa cha zolakwa zawo. 33  Koma sindidzasiya kumusonyeza chikondi changa chokhulupirika,+Kapena kulephera kukwaniritsa lonjezo langa.* 34  Sindidzaphwanya pangano langa+Kapena kusintha mawu otuluka pakamwa panga.+ 35  Ndalumbira kamodzi kokha pa kuyera kwanga.Davide sindidzamunamiza.+ 36  Mbadwa* zake zidzakhalapo mpaka kalekale,+Ndipo mpando wake wachifumu udzakhala pamaso panga kwamuyaya ngati dzuwa.+ 37  Udzakhalapo mpaka kalekale ngati mweziUdzakhala ngati mboni yokhulupirika yamumlengalenga.” (Selah) 38  Koma inu mwataya wodzozedwa wanu ndipo mwamukana,+Komanso mwamukwiyira kwambiri. 39  Mwakana monyansidwa pangano la mtumiki wanu.Mwanyoza chisoti chake chachifumu pochiponyera pansi. 40  Mwagwetsa mipanda yake yonse yamiyala.*Mizinda yake ya mipanda yolimba mwaisandutsa mabwinja. 41  Anthu onse amene amadutsa njira imeneyo alanda zinthu zake.Iye akunyozedwa ndi anthu oyandikana naye.+ 42  Mwachititsa kuti adani ake apambane.*+Mwachititsa kuti adani ake onse asangalale. 43  Mwachititsanso kuti lupanga lake likhale lopanda ntchito,Ndipo mwachititsa kuti iye asapambane pa nkhondo. 44  Mwathetsa ulemerero wake,Ndipo mpando wake wachifumu mwauponyera pansi. 45  Mwafupikitsa masiku a unyamata wake.Ndipo mwamuveka manyazi. (Selah) 46  Inu Yehova, kodi mudzadzibisa mpaka liti? Mpaka kalekale?+ Kodi mkwiyo wanu udzapitiriza kuyaka ngati moto? 47  Kumbukirani kuti moyo wanga ndi waufupi.+ Kodi anthu munawalenga popanda cholinga? 48  Kodi pali munthu aliyense amene angapitirize kukhala ndi moyo ndipo sadzafa?+ Kodi angathe kupulumutsa moyo wake ku mphamvu ya Manda?* (Selah) 49  Inu Yehova, kodi zochita zanu zakale zosonyeza chikondi chanu chokhulupirika zili kuti,Zimene munalumbira kwa Davide chifukwa cha kukhulupirika kwanu?+ 50  Inu Yehova, kumbukirani mmene atumiki anu anyozedwera.Kumbukirani mmene ndapiririra* kunyozedwa kochokera ku mitundu yonse ya anthu. 51  Inu Yehova, kumbukirani mmene adani anu alankhulira monyoza.Mmene anyozera paliponse pamene mapazi a wodzozedwa wanu aponda. 52  Yehova atamandike mpaka kalekale. Ame! Ame!+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mpando wachifumu.”
Kapena kuti, “pakati pa msonkhano wake wa oyera.”
Zikuoneka kuti dzina lakuti “Rahabi” likuimira dziko la Iguputo kapena Farao.
Mʼchilankhulo choyambirira, “nyanga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nyanga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “dzanja lake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Kapena kuti, “ziweruzo.”
Kapena kuti, “kupanduka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Kapena kulephera kusonyeza kukhulupirika kwanga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mbewu.”
Kapena kuti, “malo ake obisala amiyala.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mwakweza dzanja lamanja la adani ake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼdzanja la Manda,” amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mmene ndanyamulira pachifuwa panga.”