Salimo 9:1-20

  • Kulengeza ntchito zodabwitsa za Mulungu

    • Yehova ndi malo othawirako otetezeka (9)

    • Anthu odziwa dzina la Mulungu adzamukhulupirira (10)

Kwa wotsogolera nyimbo, pa Mutilabeni.* Nyimbo ya Davide. א [Aleph] 9  Ndidzakutamandani inu Yehova ndi mtima wanga wonse.Ndidzafotokoza za ntchito zanu zonse zodabwitsa.+   Ndidzakondwera ndi kusangalala chifukwa cha inu,Ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu, inu Wamʼmwambamwamba.+ ב [Beth]   Adani anga akathawa,+Adzapunthwa nʼkuwonongedwa pamaso panu.   Chifukwa mumanditeteza kuti mlandu wanga uweruzidwe mwachilungamo.Mwakhala pampando wanu wachifumu ndipo mukuweruza mwachilungamo.+ ג [Gimel]   Mwadzudzula mitundu ya anthu+ ndipo mwawononga anthu oipa,Nʼkufufuta dzina lawo kwamuyaya.   Mdani wawonongedwa mpaka kalekale.Mwawononganso mizinda yawo,Ndipo sadzakumbukiridwanso.+ ה [He]   Koma Yehova ndi mfumu mpaka kalekale.+Iye akupitiriza kulamulira ndipo nthawi zonse amaweruza mwachilungamo.+   Iye adzaweruza anthu okhala padziko lapansi mwachilungamo.+Adzapereka zigamulo zolungama pa milandu ya mitundu ya anthu.+ ו [Waw]   Yehova adzakhala malo otetezeka* komwe anthu oponderezedwa angathawireko,+Malo otetezeka othawirako pa nthawi ya mavuto.+ 10  Anthu odziwa dzina lanu adzakukhulupirirani.+Simudzasiya anthu amene amakufunafunani, inu Yehova.+ ז [Zayin] 11  Imbani nyimbo zotamanda Yehova, amene akukhala mu Ziyoni.Dziwitsani mitundu ya anthu za ntchito zake.+ 12  Mulungu adzakumbukira anthu ovutika ndipo adzabwezera anthu amene anawapha.+Iye sadzaiwala kulira kwa anthu ovutikawo.+ ח [Heth] 13  Ndikomereni mtima inu Yehova. Inu amene mukundichotsa pakhomo la imfa,+Onani mmene anthu amene akudana nane akundizunzira, 14  Kuti ndilengeze ntchito zanu zotamandika pamageti a mwana wamkazi wa Ziyoni,*+Komanso kuti ndisangalale chifukwa mwandipulumutsa.+ ט [Teth] 15  Mitundu ya anthu yagwera mʼdzenje limene anakumba okha.Phazi lawo lakodwa mu ukonde umene anatchera okha.+ 16  Yehova amadziwika ndi ziweruzo zimene amapereka.+ Woipa wakodwa mumsampha umene watchera yekha.+ Higayoni.* (Selah) י [Yod] 17  Anthu oipa adzapita ku Manda,*Anthu a mitundu yonse amene aiwala Mulungu adzapita kumeneko. 18  Koma Mulungu sadzaiwala anthu osauka,+Ndiponso chiyembekezo cha anthu ofatsa sichidzatha.+ כ [Kaph] 19  Nyamukani, inu Yehova! Musalole kuti munthu apambane. Mitundu ya anthu iweruzidwe pamaso panu.+ 20  Achititseni mantha, inu Yehova,+Chititsani kuti mitundu ya anthu idziwe kuti iwo ndi anthu basi. (Selah)

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “malo okwezeka achitetezo.”
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.