Salimo 90:1-17

  • Mulungu wamuyaya komanso munthu amene amakhala nthawi yochepa

    • Zaka 1,000 zili ngati dzulo (4)

    • Munthu amangokhala ndi moyo zaka 70 kapena 80 (10)

    • “Tiphunzitseni mmene tingagwiritsire ntchito bwino moyo wathu” (12)

Pemphero la Mose, munthu wa Mulungu woona.+ 90  Inu Yehova, mwakhala malo athu okhalamo+ ku mibadwo yonse.   Mapiri asanabadwe,Kapena musanakhazikitse dziko lapansi komanso nthaka,+Inu ndinu Mulungu kuyambira kalekale mpaka kalekale.+   Mumabwezera munthu kufumbi,Mumanena kuti: “Bwererani kufumbi, inu ana a anthu.”+   Chifukwa kwa inu zaka 1,000 zili ngati dzulo lapitali,+Zili ngati ulonda umodzi wa usiku.   Mumawawononga+ ndipo amatha ngati tulo.Mʼmawa amakhala ngati msipu umene waphukira.+   Mʼmawa umaphuka ndipo umabiriwira,Koma madzulo umafota kenako nʼkuuma.+   Chifukwa ife tawonongedwa ndi mkwiyo wanu,+Ndipo tikuchita mantha kwambiri ndi ukali wanu.   Mumaika zolakwa zathu patsogolo panu,*+Zinsinsi zathu zaululika chifukwa cha kuwala kwa nkhope yanu.+   Moyo wathu ukutha chifukwa cha mkwiyo wanu.Timafa msanga ngati mpweya umene umatha mofulumira. 10  Masiku a moyo wathu amangokwana zaka 70Kapena 80+ ngati munthu ali ndi mphamvu zambiri.* Koma zimakhala zodzaza ndi mavuto komanso chisoni.Zimatha mofulumira ndipo moyo wathu umachoka.+ 11  Ndi ndani angadziwe kuchuluka kwa mphamvu za mkwiyo wanu? Ukali wanu ndi waukulu mofanana ndi mantha amene tikuyenera kukusonyezani.+ 12  Tiphunzitseni mmene tingagwiritsire ntchito bwino moyo wathu*+Kuti tikhale ndi mtima wanzeru. 13  Bwererani, inu Yehova!+ Kodi zinthu zikhala chonchi mpaka liti?+ Timvereni chisoni ife atumiki anu.+ 14  Mʼmawa, muzitisonyeza chikondi chanu chokhulupirika,+Kuti tizifuula mokondwera komanso kukhala mosangalala+ masiku onse a moyo wathu. 15  Tichititseni kuti tisangalale kwa masiku ofanana ndi masiku amene mwatisautsa,+Kwa zaka zofanana ndi zaka zimene takumana ndi masoka.+ 16  Atumiki anu aone ntchito zanu,Ndipo ana awo aone ulemerero wanu.+ 17  Yehova Mulungu wathu atikomere mtima.Chititsani kuti ntchito ya manja anthu iyende bwino.* Inde, chititsani kuti ntchito ya manja athu iyende bwino.*+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Mukudziwa zolakwa zathu.”
Kapena kuti, “zapadera.”
Kapena kuti, “mmene tingawerengere masiku athu.”
Kapena kuti, “Khazikitsani ntchito ya manja athu.”
Kapena kuti, “khazikitsani ntchito ya manja athu.”