Salimo 91:1-16

  • Kutetezedwa mʼmalo obisika a Mulungu

    • Kupulumutsidwa mumsampha wa wosaka mbalame (3)

    • Kuthawira pansi pa mapiko a Mulungu (4)

    • Kukhala otetezeka ngakhale anthu masauzande atagwa (7)

    • Adzalamula angelo kuti akuteteze (11)

91  Aliyense amene akukhala mʼmalo obisika a Wamʼmwambamwamba+Adzakhala mumthunzi wa Wamphamvuyonse.+   Ndidzauza Yehova kuti: “Inu ndinu malo anga othawirako komanso malo anga achitetezo,+Mulungu wanga amene ndimamukhulupirira.”+   Chifukwa iye adzakupulumutsa mumsampha wa wosaka mbalame,Komanso ku mliri wowononga.   Adzakuphimba ndi mapiko ake,Ndipo udzathawira pansi pa mapiko ake.*+ Kukhulupirika kwake+ kudzakhala chishango chako chachikulu+ komanso khoma lokuteteza.   Usiku sudzaopa choopsa chilichonse,+Kapena muvi woponyedwa masana,+   Sudzaopa mliri umene umafalikira mumdima,Kapena chiwonongeko chimene chimachitika masana.   Anthu 1,000 adzagwa pambali pako,Ndipo anthu 10,000 adzagwa kudzanja lako lamanja.Koma palibe choipa chilichonse chimene chidzakuchitikire.+   Maso ako adzaona zimenezi zikuchitika,Pamene anthu oipa akulandira chilango.*   Popeza wanena kuti: “Yehova ndi malo anga othawirako,” Wapanga Wamʼmwambamwamba kuti akhale malo ako okhalamo.+ 10  Palibe tsoka limene lidzakugwere,+Ndipo palibe mliri umene udzayandikire tenti yako. 11  Chifukwa adzalamula angelo ake+ zokhudza iwe,Kuti akuteteze mʼnjira zako zonse.+ 12  Iwo adzakunyamula mʼmanja mwawo,+Kuti phazi lako lisawombe mwala.+ 13  Udzapondaponda mkango wamphamvu ndi njoka ya mamba,Ndipo udzapondaponda mkango wamphamvu kwambiri komanso chinjoka chachikulu.+ 14  Mulungu ananena kuti: “Popeza amandikonda,* ine ndidzamupulumutsa.+ Ndidzamuteteza chifukwa akudziwa* dzina langa.+ 15  Adzandiitana ndipo ndidzamuyankha.+ Ndidzakhala naye pa nthawi ya mavuto.+ Ndidzamupulumutsa komanso kumupatsa ulemerero. 16  Ndidzamupatsa moyo wautali,+Ndipo ndidzamuchititsa kuti aone mmene ndidzamupulumutsire.”*+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Adzakutchinga ndi mapiko ake kuti adani asakuyandikire.”
Kapena kuti, “Pamene akubwezera anthu oipa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wadzigwirizanitsa ndi ine.”
Kapena kuti, “akuvomereza.”
Kapena kuti, “aone chipulumutso chochokera kwa ine.”