Salimo 97:1-12

  • Yehova ndi wokwezeka kuposa milungu ina yonse

    • “Yehova wakhala Mfumu!” (1)

    • Muzikonda Yehova nʼkumadana ndi zoipa (10)

    • Kuwala kwaunikira olungama (11)

97  Yehova wakhala Mfumu!+ Dziko lapansi lisangalale.+ Zilumba zambiri zikondwere.+   Mitambo ndi mdima wandiweyani zamuzungulira.+Maziko a mpando wake wachifumu ndi chilungamo komanso chiweruzo cholungama.+   Moto umachoka kwa iye+Nʼkupsereza adani ake omuzungulira.+   Kungʼanima kwa mphezi zake kumaunika dziko.Dziko lapansi limaona zimenezi ndipo limanjenjemera.+   Mapiri amasungunuka ngati phula pamaso pa Yehova,+Pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.   Kumwamba kumalengeza za chilungamo chake,Ndipo mitundu yonse ya anthu imaona ulemerero wake.+   Onse amene akutumikira chifaniziro chilichonse achite manyazi,+Amene amadzitama chifukwa cha milungu yawo yopanda pake.+ Muweramireni,* inu milungu yonse.+   Ziyoni wamva ndipo akusangalala,+Matauni* a ku Yuda akukondweraChifukwa cha zigamulo zanu, inu Yehova.+   Chifukwa inu Yehova, ndinu Wamʼmwambamwamba woyenera kulamulira dziko lonse lapansi.Ndinu wokwezeka kwambiri kuposa milungu ina yonse.+ 10  Inu amene mumakonda Yehova, muzidana ndi zoipa.+ Iye amateteza moyo wa anthu ake okhulupirika.+Amawapulumutsa mʼmanja mwa* oipa.+ 11  Kuwala kwaunikira olungama+Ndipo owongoka mtima akusangalala. 12  Sangalalani chifukwa cha Yehova, olungama inu,Ndipo yamikirani dzina lake loyera.*

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Mulambireni.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana aakazi.”
Kapena kuti, “ku mphamvu za.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chikumbutso chake choyera.”