Salimo 98:1-9

  • Yehova ndi Mpulumutsi komanso Woweruza wolungama

    • Chipulumutso cha Yehova chadziwika (2, 3)

Nyimbo. 98  Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,+Chifukwa wachita zinthu zodabwitsa.+ Dzanja lake lamanja, mkono wake woyera, wabweretsa chipulumutso.*+   Yehova wachititsa kuti chipulumutso chake chidziwike.+Wachititsa kuti anthu a mitundu yonse aone chilungamo chake.+   Iye wakumbukira chikondi chake chokhulupirika komanso kukhulupirika kumene analonjeza nyumba ya Isiraeli.+ Anthu onse padziko lapansi aona mmene Mulungu wathu wapulumutsira anthu ake.*+   Dziko lonse lapansi lifuulire Yehova mosangalala chifukwa wapambana. Kondwerani ndipo fuulani mosangalala komanso imbani nyimbo zomutamanda.+   Imbirani Yehova nyimbo zomutamanda pogwiritsa ntchito zeze,Mutamandeni ndi nyimbo zosangalatsa pogwiritsa ntchito zeze.   Fuulani mosangalala pamaso pa Mfumu Yehova,Poimba malipenga komanso lipenga la nyanga ya nkhosa chifukwa wapambana.+   Nyanja ichite mkokomo ndi zonse zimene zili mmenemo,Chimodzimodzinso dziko lapansi komanso amene akukhala mmenemo.   Mitsinje iwombe mʼmanja,Mapiri afuule pamodzi mosangalala+   Pamaso pa Yehova chifukwa iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi. Adzaweruza anthu okhala padziko lapansi mwachilungamo+Ndipo adzaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “zamuchititsa kuti apambane.”
Kapena kuti, “aona kupambana kwa Mulungu wathu.”