Salimo 99:1-9

  • Yehova ndi Mfumu yoyera

    • Wakhala pampando wachifumu pamwamba pa akerubi (1)

    • Mulungu amene amakhululuka komanso kupereka chilango (8)

99  Yehova wakhala Mfumu.+ Mitundu ya anthu injenjemere. Iye wakhala pampando wachifumu pamwamba* pa akerubi.+ Dziko lapansi ligwedezeke.   Yehova ndi wamkulu mu Ziyoni,Ndipo iye ali pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.+   Iwo atamande dzina lanu lalikulu,+Chifukwa ndi lochititsa mantha komanso loyera.   Iye ndi mfumu yamphamvu imene imakonda chilungamo.+ Nthawi zonse mumaonetsetsa kuti chilungamo chachitika. Mwabweretsa chiweruzo cholungama komanso chilungamo+ pakati pa ana a Yakobo.   Kwezani Yehova Mulungu wathu+ ndipo mugwadireni* pachopondapo mapazi ake.+Iye ndi woyera.+   Mose ndi Aroni anali mʼgulu la ansembe ake,+Ndipo Samueli anali mʼgulu la anthu amene ankaitana pa dzina lake.+ Iwo ankaitana Yehova,Ndipo iye ankawayankha.+   Mulungu ankalankhula nawo kuchokera mʼchipilala cha mtambo.+ Iwo anasunga zikumbutso zake ndi malamulo amene anawapatsa.+   Inu Yehova Mulungu wathu munawayankha.+ Inu ndi Mulungu amene munawakhululukira,+Koma munawalanga chifukwa cha machimo awo.+   Kwezani Yehova Mulungu wathu+Ndipo mugwadireni* paphiri lake loyera,+Chifukwa Yehova Mulungu wathu ndi woyera.+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “pakati.”
Kapena kuti, “mulambireni.”
Kapena kuti, “mulambireni.”