Wolembedwa ndi Mateyu 1:1-25

  • Mzere wa makolo a Yesu Khristu (1-17)

  • Kubadwa kwa Yesu (18-25)

1  Buku la mzere wa makolo a Yesu Khristu,* mwana wa Davide,+ mwana wa Abulahamu:+   Abulahamu anabereka Isaki.+Isaki anabereka Yakobo.+Yakobo anabereka Yuda+ ndi azichimwene ake.   Yuda anabereka Perezi ndi Zera,+ ndipo mayi awo anali Tamara.Perezi anabereka Hezironi.+Hezironi anabereka Ramu.+   Ramu anabereka Aminadabu.Aminadabu anabereka Naasoni.+Naasoni anabereka Salimoni.   Salimoni anabereka Boazi, ndipo mayi ake anali Rahabi.+Boazi anabereka Obedi, ndipo mayi ake anali Rute.+Obedi anabereka Jese.+   Jese anabereka Mfumu Davide.+ Davide anabereka Solomo,+ yemwe mayi ake anali mkazi wa Uriya.   Solomo anabereka Rehobowamu.+Rehobowamu anabereka Abiya.Abiya anabereka Asa.+   Asa anabereka Yehosafati.+Yehosafati anabereka Yehoramu.+Yehoramu anabereka Uziya.   Uziya anabereka Yotamu.+Yotamu anabereka Ahazi.+Ahazi anabereka Hezekiya.+ 10  Hezekiya anabereka Manase.+Manase anabereka Amoni.+Amoni anabereka Yosiya.+ 11  Yosiya+ anabereka Yekoniya+ ndi azichimwene ake pa nthawi imene Ayuda anatengedwa kupita ku Babulo.+ 12  Ayuda atatengedwa kupita ku Babulo, Yekoniya anabereka Salatiyeli.Salatiyeli anabereka Zerubabele.+ 13  Zerubabele anabereka Abiyudi.Abiyudi anabereka Eliyakimu.Eliyakimu anabereka Azoro. 14  Azoro anabereka Zadoki.Zadoki anabereka Akimu.Akimu anabereka Eliyudi. 15  Eliyudi anabereka Eleazara.Eleazara anabereka Matani.Matani anabereka Yakobo. 16  Yakobo anabereka Yosefe mwamuna wake wa Mariya, amene anabereka Yesu,+ wotchedwa Khristu.+ 17  Choncho mibadwo yonse kuchokera pa Abulahamu kukafika pa Davide inalipo mibadwo 14. Kuchokera pa Davide kukafika nthawi imene Ayuda anatengedwa kupita ku Babulo panali mibadwo 14. Kuchokera pa nthawi imene Ayudawo anatengedwa kupita ku Babulo kukafika pa Khristu, panali mibadwo 14. 18  Zimene zinachitika kuti Yesu Khristu abadwe ndi izi: Pa nthawi imene mayi ake Mariya anali atalonjezedwa ndi Yosefe kuti adzamukwatira, Mariyayo anapezeka kuti ndi woyembekezera mwa mzimu woyera*+ asanakwatirane. 19  Koma chifukwa chakuti mwamuna wake Yosefe anali munthu wolungama ndipo sanafune kumuchititsa manyazi kwa anthu, anaganiza zomusiya mwachinsinsi.*+ 20  Koma ataganizira mozama za nkhani imeneyi, mngelo wa Yehova* anamuonekera mʼmaloto nʼkumuuza kuti: “Yosefe, mwana wa Davide, usaope kutenga Mariya mkazi wako nʼkupita naye kunyumba, popeza iye ndi woyembekezera chifukwa cha mphamvu ya mzimu woyera.+ 21  Iye adzabereka mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina lakuti Yesu,*+ chifukwa adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.”+ 22  Zonsezi zinachitikadi kuti zimene Yehova* ananena kudzera mwa mneneri wake zikwaniritsidwe. Iye anati: 23  “Tamverani! Namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabereka mwana wamwamuna. Mwanayo adzamʼpatsa dzina lakuti Emanueli,”+ limene akalimasulira limatanthauza kuti “Mulungu Ali Nafe.”+ 24  Ndiyeno Yosefe anadzuka nʼkuchita mogwirizana ndi zimene mngelo wa Yehova* anamuuza. Anatenga mkazi wake nʼkupita naye kunyumba. 25  Koma sanagone naye mpaka anabereka mwana wamwamuna.+ Mwanayo anamupatsa dzina lakuti Yesu.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Mesiya; Wodzozedwa.”
Kapena kuti, “mphamvu ya Mulungu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anaganiza zothetsa ukwati mwachinsinsi.” Pa mwambo wachiyuda, kuti lonjezo loti anthu adzakwatirana lithe, ankatsatira dongosolo lothetsera ukwati.
Awa ndi malo oyamba mwa malo 237 mʼMalemba a Chigiriki pamene dzina la Mulungu lakuti Yehova likupezeka mʼBaibuloli. Onani Zakumapeto A5.
MʼChiheberi dzinali amati Yesuwa kapena kuti Yoswa ndipo limatanthauza kuti “Yehova Ndi Chipulumutso.”