Wolembedwa ndi Mateyu 11:1-30

  • Yohane Mʼbatizi analemekezedwa (1-15)

  • Anadzudzula mʼbadwo wosamvera (16-24)

  • Yesu anatamanda Atate wake chifukwa chokomera mtima anthu wamba (25-27)

  • Goli la Yesu limatsitsimula (28-30)

11  Yesu atamaliza kupereka malangizo kwa ophunzira ake 12 aja, anachoka kumeneko nʼkupita kukaphunzitsa ndi kukalalikira kumizinda ina.+  Koma Yohane ali mʼndende,+ anamva zimene Khristu ankachita ndipo anatuma ophunzira ake+  kukamufunsa kuti: “Kodi Mesiya amene tikumuyembekezera uja ndi inu kapena tiyembekezere wina?”+  Poyankha Yesu anawauza kuti: “Pitani mukauze Yohane zimene mukumva ndi kuona:+  Amene anali ndi vuto losaona akuona,+ olumala akuyenda, akhate+ akuyeretsedwa ndipo amene anali ndi vuto losamva akumva. Akufa akuukitsidwa ndipo osauka akuuzidwa uthenga wabwino.+  Wosangalala ndi amene sapeza chokhumudwitsa mwa ine.”+  Pamene ophunzira a Yohane ankabwerera, Yesu anayamba kuuza gulu la anthu za Yohane kuti: “Kodi munapita mʼchipululu kukaona chiyani?+ Kodi munapita kukaona bango logwedezeka ndi mphepo?+  Nanga munapita kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zapamwamba kapena? Ayi, paja amene amavala zovala zapamwamba amapezeka mʼnyumba za mafumu.  Nangano nʼchifukwa chiyani munapita makamaka? Kukaona mneneri kapena? Inde, ndikukuuzani, Yohane ndi mneneri komanso ndi wofunika kwambiri kuposa aneneri.+ 10  Malemba amanena za iyeyu kuti: ‘Taona! Ine ndikutumiza mthenga wanga kuti atsogole kukakukonzera njira!’+ 11  Ndithu ndikukuuzani, pa anthu onse,* palibe wamkulu kuposa Yohane Mʼbatizi. Koma munthu amene ali wocheperapo mu Ufumu wakumwamba ndi wamkulu kuposa iyeyu.+ 12  Kuyambira mʼmasiku a Yohane Mʼbatizi mpaka pano anthu akuyesetsa mwakhama kuti apeze mwayi wolowa mu Ufumu wakumwamba, ndipo amene akuyesetsa mwakhama akuupeza.+ 13  Chifukwa zonse zimene aneneri analemba komanso Chilamulo, zinalosera mpaka nthawi ya Yohane.+ 14  Kaya mukhulupirira kapena ayi, Yohane ndi ‘Eliya amene aneneri ananena kuti adzabwera.’+ 15  Amene ali ndi makutu amve. 16  Kodi mʼbadwo uwu ndiuyerekezere ndi ndani?+ Uli ngati ana aangʼono amene akhala pansi mʼmisika nʼkumafuulira anzawo amene amasewera nawo 17  kuti: ‘Tinakuimbirani chitoliro, koma simunavine. Tinalira mofuula, koma inu simunadzigugude pachifuwa chifukwa cha chisoni.’ 18  Mofanana ndi zimenezi, Yohane anabwera ndipo sankadya kapena kumwa. Koma anthu ankanena kuti, ‘Ali ndi chiwanda.’ 19  Kunabwera Mwana wa munthu ndipo akudya ndi kumwa+ koma anthu akunena kuti, ‘Taonani! Munthu wosusuka ndi wokonda kwambiri vinyo, bwenzi la okhometsa msonkho ndi ochimwa.’+ Mulimonsemo, nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama* chifukwa cha ntchito zake.”*+ 20  Kenako anayamba kudzudzula mizinda imene anachitamo ntchito zambiri zamphamvu chifukwa sinalape. Iye anati: 21  “Tsoka kwa iwe Korazini! Tsoka kwa iwe Betsaida! Chifukwa ntchito zamphamvu zimene zinachitika mwa iwe zikanachitika ku Turo ndi ku Sidoni, anthu akanakhala atalapa kalekale, atavala ziguduli nʼkukhala paphulusa.+ 22  Koma ndikukuuzani kuti chilango chanu chidzakhala chopweteka kwambiri kuposa cha Turo ndi Sidoni pa Tsiku la Chiweruzo.+ 23  Iwenso Kaperenao,+ kodi mwina udzakwezedwa kumwamba? Ayi, koma udzatsikira ku Manda,*+ chifukwa ntchito zamphamvu zimene zinachitika mwa iwe zikanachitika ku Sodomu, mzindawo ukanakhala ulipobe mpaka lero. 24  Koma ndikukuuzani kuti chilango cha Kaperenao chidzakhala chopweteka kwambiri kuposa cha Sodomu pa Tsiku la Chiweruzo.”+ 25  Pa nthawi imeneyo Yesu ananena kuti: “Ndikukutamandani inu Atate pamaso pa onse, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa anthu anzeru ndi ozindikira mwawabisira zinthu zimenezi ndipo mwaziulula kwa ana angʼono.+ 26  Inde Atate, chifukwa inu munavomereza kuti zimenezi zichitike. 27  Atate wanga wapereka zinthu zonse kwa ine+ ndipo palibe amene akumudziwa bwino Mwana koma Atate okha.+ Komanso palibe amene akuwadziwa bwino Atate koma Mwana yekha ndi aliyense amene Mwanayo wafuna kumuululira za Atatewo.+ 28  Bwerani kwa ine inu nonse amene mukugwira ntchito yotopetsa ndi olemedwa ndipo ndidzakutsitsimulani. 29  Senzani goli langa ndipo lolani kuti ndikuphunzitseni, chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa+ ndipo mudzatsitsimulidwa. 30  Chifukwa goli langa ndi losavuta kunyamula ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mwa onse amene anabadwa kwa akazi.”
Kapena kuti, “imaonekera kuti ndi yeniyeni.”
Kapena kuti, “chifukwa cha zotsatira zake.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu ena.