Wolembedwa ndi Mateyu 14:1-36

  • Yohane Mʼbatizi anadulidwa mutu (1-12)

  • Yesu anadyetsa anthu 5,000 (13-21)

  • Yesu anayenda pamadzi (22-33)

  • Anachiritsa anthu ku Genesareti (34-36)

14  Pa nthawiyo Herode, wolamulira chigawo,* anamva za Yesu+  ndipo anauza atumiki ake kuti: “Ameneyu ndi Yohane Mʼbatizi. Anauka kwa akufa ndiye nʼchifukwa chake akuchita ntchito zamphamvu.”+  Herode* anagwira Yohane nʼkumumanga ndipo anamutsekera mʼndende chifukwa cha Herodiya, mkazi wa mchimwene wake Filipo amene Herodeyo anakwatira.+  Anachita zimenezi chifukwa Yohane ankamuuza kuti: “Nʼzosaloleka kuti mutenge mkazi ameneyu kukhala mkazi wanu.”+  Komabe, ngakhale kuti Herode ankafuna kupha Yohane, ankaopa gulu la anthu chifukwa iwo ankakhulupirira kuti anali mneneri.+  Koma tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode+ litafika, mwana wamkazi wa Herodiya anavina pa tsikulo ndipo anasangalatsa kwambiri Herode,+  moti anachita kulumbira polonjeza mtsikanayo kuti adzamupatsa chilichonse chimene angapemphe.  Ndiyeno mtsikanayo, mayi ake atachita kumuuza zoti apemphe ananena kuti: “Mundipatse mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale pompano.”+  Mfumuyo inamva chisoni koma poganizira lumbiro limene inapanga lija komanso anthu amene anali nawo paphwandolo, analamula kuti mutuwo uperekedwe. 10  Choncho anatuma munthu kuti akadule mutu wa Yohane mʼndende. 11  Kenako anabweretsa mutuwo mʼmbale nʼkuupereka kwa mtsikanayo ndipo iye anapita nawo kwa mayi ake. 12  Pambuyo pake ophunzira ake anabwera kudzatenga mtembo wake nʼkukauika mʼmanda. Kenako anapita kukauza Yesu. 13  Yesu atamva zimenezi, anachoka kumeneko pangalawa nʼkupita kumalo kopanda anthu kuti akakhale payekha. Koma gulu la anthu litamva zimenezo, linamutsatira wapansi kuchokera mʼmizinda yawo.+ 14  Yesu atatsika mʼngalawayo anaona gulu lalikulu la anthu ndipo anawamvera chisoni+ nʼkuwachiritsira anthu awo odwala.+ 15  Koma chakumadzulo ophunzira ake anabwera kwa iye nʼkunena kuti: “Kuno nʼkopanda anthu ndipo nthawi yatha, auzeni anthuwa kuti anyamuke, apite mʼmidzimo kuti akagule chakudya choti adye.”+ 16  Koma Yesu anawayankha kuti: “Palibe chifukwa choti apitire. Inuyo muwapatse chakudya.” 17  Iwo anamuuza kuti: “Tilibe chilichonse pano, kupatulapo mitanda 5 ya mkate ndi nsomba ziwiri zokha basi.” 18  Iye anati: “Bweretsani zimenezo kuno.” 19  Kenako analamula gulu la anthulo kuti likhale pansi pa udzu. Ndiyeno anatenga mitanda ya mkate 5 ndi nsomba ziwiri zija nʼkuyangʼana kumwamba ndi kupemphera.+ Atatero ananyemanyema mitanda ya mkate ija nʼkuipereka kwa ophunzirawo ndipo iwo anagawira gulu la anthulo. 20  Choncho onse anadya nʼkukhuta ndipo zimene zinatsala anazitolera moti zinadzaza madengu 12.+ 21  Koma amene anadya anali amuna pafupifupi 5,000 osawerengera akazi ndi ana aangʼono.+ 22  Kenako mwamsanga, Yesu anauza ophunzira ake kuti akwere ngalawa nʼkutsogola kupita kutsidya lina. Koma iye anatsalira nʼcholinga choti auze anthuwo kuti azipita kwawo.+ 23  Atauza anthuwo kuti azipita, anakwera phiri yekhayekha kukapemphera.+ Iye anakhala kumeneko yekhayekha mpaka kunja kunada. 24  Pa nthawiyi nʼkuti ngalawa ija itapita kutali* pakati pa madzi, ndipo inkakankhidwa mwamphamvu ndi mafunde chifukwa ankalimbana ndi mphepo yamphamvu. 25  Koma pa ulonda wa 4* mʼbandakucha, iye anafika kwa ophunzirawo akuyenda pamwamba pa madzi. 26  Ophunzirawo atamuona akuyenda panyanjapo, anachita mantha nʼkunena kuti: “Amenewa ndi masomphenya ndithu!” Ndipo anafuula mwamantha. 27  Koma nthawi yomweyo Yesu anawauza kuti: “Mtima mʼmalo, ndine. Musachite mantha.”+ 28  Ndiyeno Petulo anayankha kuti: “Ambuye, ngati ndinudi ndiuzeni ndiyende pamadzipa ndibwere kuli inuko.” 29  Iye anamuuza kuti: “Bwera!” Choncho Petulo anatsika mʼngalawamo nʼkuyenda pamadzi kupita kumene kunali Yesu. 30  Koma ataona mphepo yamkuntho, anachita mantha. Atayamba kumira anafuula kuti: “Ambuye, ndipulumutseni!” 31  Nthawi yomweyo Yesu anatambasula dzanja lake nʼkumugwira ndipo anamuuza kuti: “Wachikhulupiriro chochepa iwe, nʼchifukwa chiyani wakayikira?”+ 32  Atakwera mʼngalawa, mphepo yamkuntho ija inasiya. 33  Pamenepo amene anali mʼngalawamo anamugwadira nʼkunena kuti: “Ndinudi Mwana wa Mulungu.” 34  Ndipo anawolokera kumtunda ku Genesareti.+ 35  Anthu amʼdera limeneli atamuzindikira, anatumiza uthenga mʼmidzi yonse yapafupi ndipo anamubweretsera anthu onse amene ankadwala. 36  Anthu ankamupempha kuti angogwira ulusi wopota wamʼmphepete mwa malaya ake akunja,+ ndipo anthu onse amene anaugwira anachiriratu.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “bwanamkubwa wa chigawo cha 4 cha dera.”
Ameneyu ndi Herode Antipa. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “masitadiya ambiri.” Sitadiya imodzi inali yofanana ndi mamita 185.
Nthawi imeneyi inkayamba 3 koloko mpaka dzuwa litatuluka cha mʼma 6 koloko mʼmawa.