Wolembedwa ndi Mateyu 15:1-39

  • Anadzudzula miyambo ya makolo (1-9)

  • Zodetsa zimachokera mumtima (10-20)

  • Chikhulupiriro cholimba cha mayi wa ku Foinike (21-28)

  • Yesu anachiritsa matenda ambiri (29-31)

  • Yesu anadyetsa anthu 4,000 (32-39)

15  Kenako Afarisi ndi alembi+ ochokera ku Yerusalemu anapita kwa Yesu nʼkumufunsa kuti:  “Nʼchifukwa chiyani ophunzira anu amaphwanya miyambo ya makolo? Mwachitsanzo, sasamba mʼmanja* akafuna kudya chakudya.”+  Koma iye anawayankha kuti: “Nʼchifukwa chiyani inuyo mumaphwanya malamulo a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu?+  Mwachitsanzo, Mulungu ananena kuti, ‘Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu.’+ Komanso anati, ‘Aliyense wolankhula mawu achipongwe kwa bambo ake kapena mayi ake aziphedwa.’+  Koma inu mumanena kuti, ‘Aliyense wouza bambo ake kapena mayi ake kuti: “Chilichonse chimene ndili nacho, chimene ndikanakuthandizani nacho ndi mphatso yoti ndipereke kwa Mulungu,”+  sakuyenera kuthandiza bambo ake.’ Choncho mwachititsa kuti mawu a Mulungu akhale opanda pake chifukwa cha miyambo yanu.+  Anthu achinyengo inu! Yesaya analosera zolondola zokhudza inu pamene anati:+  ‘Anthu awa amandilemekeza ndi milomo yokha, koma mitima yawo aiika kutali ndi ine.  Chilichonse chomwe amachita pondilambira ndi chopanda pake, chifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu ngati kuti ndi malamulo a Mulungu.’”+ 10  Atanena zimenezi, anaitana gulu la anthu kuti liyandikire ndipo anawauza kuti: “Mvetserani ndipo muzindikire tanthauzo lake:+ 11  Chimene chimalowa mʼkamwa mwa munthu si chimene chimamuipitsa, koma chimene chimatuluka mʼkamwa mwake nʼchimene chimamuipitsa.”+ 12  Ndiyeno ophunzira ake anabwera nʼkumufunsa kuti: “Kodi mukudziwa kuti Afarisi akhumudwa ndi zimene mwanena zija?”+ 13  Koma iye anayankha kuti: “Mbewu iliyonse imene sinadzalidwe ndi Atate wanga wakumwamba idzazulidwa. 14  Asiyeni amenewo. Iwo ndi atsogoleri akhungu. Choncho ngati munthu wakhungu akutsogolera wakhungu mnzake, onse awiri adzagwera mʼdzenje.”+ 15  Ndiyeno Petulo anamupempha kuti: “Timasulireni fanizo lija.” 16  Yesu anawafunsa kuti: “Kodi inunso simunamvetse?+ 17  Kodi simukudziwa kuti chilichonse chimene chalowa mʼkamwa chimadutsa mʼmimba ndipo chimakatayidwa kuchimbudzi? 18  Koma chilichonse chimene chimatuluka pakamwa chimachokera mumtima ndipo zinthu zimenezo ndi zimene zimaipitsa munthu.+ 19  Mwachitsanzo, mumtima mumachokera maganizo oipa awa:+ maganizo a kupha anthu, a chigololo, a chiwerewere,* a kuba, maumboni onama komanso kunyoza Mulungu. 20  Zimenezi ndi zinthu zimene zimaipitsa munthu, koma kudya chakudya osasamba mʼmanja* sikuipitsa munthu.” 21  Yesu atachoka kumeneko anapita mʼzigawo za Turo ndi Sidoni.+ 22  Ndiyeno kunabwera mayi wina wa ku Foinike kuchokera mʼzigawo zimenezo ndipo anafuula kuti: “Ndichitireni chifundo Ambuye, Mwana wa Davide. Mwana wanga wamkazi anagwidwa ndi chiwanda chimene chikumuzunza mwankhanza.”+ 23  Koma iye sanamuyankhe chilichonse. Choncho ophunzira ake anabwera nʼkumuuza kuti: “Muuzeni kuti azipita, chifukwa akupitirizabe kufuula mʼmbuyo mwathumu.” 24  Iye anayankha kuti: “Ine sananditumize kwa wina aliyense koma kwa nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli.”+ 25  Koma mayi uja anabwera pafupi nʼkumugwadira ndipo ananena kuti: “Ambuye, ndithandizeni!” 26  Iye anamuyankha kuti: “Si bwino kutenga chakudya cha ana nʼkuponyera tiagalu.” 27  Mayiyo ananena kuti: “Inde Ambuye, komatu tiagalu timadya nyenyeswa zimene zikugwa patebulo la ambuye awo.”+ 28  Ndiyeno Yesu anamuyankha kuti: “Mayi iwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu. Zimene ukufuna zichitike kwa iwe.” Ndipo nthawi yomweyo mwana wake anachira. 29  Yesu atachoka kumeneko, anapita kufupi ndi nyanja ya Galileya+ ndipo anakwera phiri nʼkukakhala pansi mʼphirimo. 30  Kenako anthu ochuluka anabwera kwa iye. Anabwera ndi anthu olumala, othyoka ziwalo, a vuto losaona, a vuto losalankhula, ndi ena ambiri osiyanasiyana. Anthuwo anawakhazika pamapazi ake ndipo iye anawachiritsa.+ 31  Choncho gulu la anthulo linadabwa kuona anthu osalankhula akulankhula, olumala akuyenda ndiponso anthu osaona akuona ndipo anatamanda Mulungu wa Isiraeli.+ 32  Koma Yesu anaitana ophunzira ake nʼkuwauza kuti: “Gulu la anthuli likundimvetsa chisoni,+ chifukwa anthuwa akhala ndi ine kwa masiku atatu ndipo alibe chakudya. Sindikufuna kuwauza kuti azipita ndi njala* chifukwa angalenguke panjira.”+ 33  Koma ophunzirawo anamuuza kuti: “Kumalo kopanda anthu ngati kuno chakudya chokwanira gulu lonseli tichipeza kuti?”+ 34  Ndiyeno Yesu anawafunsa kuti: “Muli ndi mitanda ingati ya mkate?” Iwo anayankha kuti: “Tili nayo 7 ndi tinsomba towerengeka.” 35  Choncho atauza anthuwo kuti akhale pansi, 36  anatenga mitanda 7 ya mkate ija ndi nsomba zija. Atayamika, anainyemanyema nʼkuyamba kupereka kwa ophunzirawo ndipo iwo anagawira gulu la anthulo.+ 37  Anthu onsewo anadya nʼkukhuta, moti zotsala zimene anatolera zinadzaza madengu akuluakulu 7.+ 38  Koma amene anadya anali amuna 4,000, osawerengera akazi ndi ana aangʼono. 39  Pambuyo pake, atauza anthuwo kuti azipita kwawo, iye anakwera ngalawa nʼkufika mʼchigawo cha Magadani.+

Mawu a M'munsi

Izi sizikutanthauza kuti ankadya chakudya ndi mʼmanja mwakuda koma kuti sankatsatira miyambo ya Chiyuda yosambira mʼmanja.
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Izi sizikutanthauza kuti ankadya chakudya ndi mʼmanja mwakuda koma kuti sankatsatira miyambo ya Chiyuda yosambira mʼmanja.
Kapena kuti, “azipita asanadye.”