Wolembedwa ndi Mateyu 21:1-46

  • Yesu analowa mumzinda mwaulemerero (1-11)

  • Yesu anayeretsa kachisi (12-17)

  • Anatemberera mtengo wa mkuyu (18-22)

  • Anakayikira ulamuliro wa Yesu (23-27)

  • Fanizo la ana awiri aamuna (28-32)

  • Fanizo la alimi amene anapha anthu (33-46)

    • Mwala wofunika kwambiri wapakona unakanidwa (42)

21  Atayandikira ku Yerusalemu nʼkufika ku Betefage paphiri la Maolivi, Yesu anatuma ophunzira awiri.+  Iye anawauza kuti: “Pitani mʼmudzi umene mukuuonawo. Kumeneko mukapeza bulu atamumangirira limodzi ndi mwana wake wamphongo. Mukawamasule nʼkuwabweretsa kwa ine.  Ngati wina atakufunsani chilichonse, mukanene kuti, ‘Ambuye akuwafuna.’ Ndipo nthawi yomweyo akawatumiza kuno.”  Izi zinachitikadi kuti zimene Mulungu ananena kudzera mwa mneneri zikwaniritsidwe, zakuti:  “Uzani mwana wamkazi wa Ziyoni* kuti: ‘Taona! Mfumu yako ikubwera kwa iwe.+ Ndi yofatsa+ ndipo yakwera bulu, yakwera mwana wamphongo wa bulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.’”+  Choncho ophunzirawo ananyamuka nʼkukachita zimene Yesu anawauza.+  Iwo anabweretsa bulu uja limodzi ndi mwana wake wamphongo. Kenako anayala malaya awo akunja pa abuluwo ndipo iye anakwera pamwana wa buluyo.+  Anthu ambiri amene anali pamenepo anayala malaya awo akunja mumsewu+ ndipo ena ankadula nthambi za mitengo nʼkuziyala mumsewu.  Komanso gulu la anthu limene linali patsogolo pake ndi mʼmbuyo mwake linkafuula kuti: “Mʼpulumutseni Mwana wa Davide!+ Wodalitsidwa ndi amene akubwera mʼdzina la Yehova!*+ Mʼpulumutseni kumwambamwambako!”+ 10  Atalowa mu Yerusalemu, mzinda wonse unagwedezeka ndipo ena ankafunsa kuti: “Kodi ameneyu ndi ndani?” 11  Gulu la anthulo linkayankha kuti: “Ameneyu ndi mneneri Yesu,+ wochokera ku Nazareti, ku Galileya!” 12  Kenako Yesu analowa mʼkachisi nʼkuthamangitsa anthu onse amene ankagulitsa ndi kugula zinthu mʼkachisimo, ndipo anagubuduza matebulo a anthu amene ankasintha ndalama komanso mabenchi a anthu amene ankagulitsa nkhunda.+ 13  Iye anawauza kuti: “Malemba amati, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo,’+ koma inu mukuisandutsa phanga la achifwamba.”+ 14  Kenako anthu amene anali ndi vuto losaona komanso olumala anabwera kwa iye mʼkachisimo ndipo anawachiritsa. 15  Ansembe aakulu ndi alembi ataona zodabwitsa zimene anachitazo komanso anyamata amene ankafuula mʼkachisimo kuti, “Mʼpulumutseni Mwana wa Davide!”+ anakwiya kwambiri+ 16  ndipo anamufunsa kuti: “Kodi ukumva zimene anthu akunenazi?” Yesu anayankha kuti: “Inde. Kodi simunawerenge zimenezi kuti, ‘Mwachititsa kuti mʼkamwa mwa ana ndi mwa makanda mutuluke mawu otamandaʼ?”+ 17  Kenako iye anawasiya nʼkutuluka mumzindawo kupita ku Betaniya ndipo anagona kumeneko.+ 18  Akubwerera kumzinda uja mʼmawa kwambiri, anamva njala.+ 19  Kenako anaona mtengo wamkuyu mʼmbali mwa msewu ndipo atapita pomwepo, sanapezemo chilichonse koma masamba okhaokha.+ Choncho anauza mtengowo kuti: “Kuyambira lero sudzaberekanso chipatso chilichonse.”+ Ndipo mkuyuwo unafota nthawi yomweyo. 20  Ophunzira aja ataona zimenezi, anadabwa nʼkunena kuti: “Zatheka bwanji kuti mkuyuwu ufote nthawi yomweyi?”+ 21  Poyankha Yesu anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, ngati mutakhala ndi chikhulupiriro ndipo simukukayikira, mudzatha kuchita zimene ndachitira mkuyu umenewu. Komanso kuposa pamenepa, mudzatha kuuza phiri ili kuti, ‘Nyamuka pano ukadziponye mʼnyanja,’ ndipo zidzachitikadi.+ 22  Zinthu zonse zimene mudzapemphe mʼmapemphero anu, mudzalandira ngati muli ndi chikhulupiriro.”+ 23  Yesu atalowa mʼkachisi nʼkumaphunzitsa, ansembe aakulu ndiponso akulu anabwera kwa iye nʼkumufunsa kuti: “Kodi muli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi? Ndipo ndi ndani amene anakupatsani ulamuliro umenewu?”+ 24  Yesu anawayankha kuti: “Inenso ndikufunsani chinthu chimodzi. Mukandiyankha chinthu chimenecho, inenso ndikuuzani amene anandipatsa ulamuliro umene ndimachitira zimenezi: 25  Kodi ubatizo umene Yohane ankachita unachokera kuti? Kumwamba kapena kwa anthu?” Koma iwo anayamba kukambirana kuti: “Tikanena kuti, ‘Unachokera kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga nʼchifukwa chiyani simunamukhulupirire?’+ 26  Komanso sitinganene kuti, ‘Unachokera kwa anthu,’ chifukwa tikuopa gulu la anthuli, popeza onsewa amakhulupirira kuti Yohane anali mneneri.” 27  Choncho iwo anayankha Yesu kuti: “Sitikudziwa.” Nayenso anawauza kuti: “Inenso sindikuuzani amene anandipatsa ulamuliro umene ndimachitira zimenezi. 28  Kodi mukuganiza bwanji? Munthu wina anali ndi ana awiri. Ndipo anapita kwa mwana woyamba nʼkumuuza kuti, ‘Mwana wanga, lero upite kukagwira ntchito mʼmunda wa mpesa.’ 29  Iye anayankha kuti, ‘Sindipita,’ koma kenako anasintha maganizo nʼkupita. 30  Kenako anapita kwa mwana wachiwiri nʼkumuuzanso chimodzimodzi. Iye anayankha kuti, ‘Ndipita bambo,’ koma sanapite. 31  Ndi ndani mwa ana awiriwa amene anachita zimene bambo ake ankafuna?” Iwo anayankha kuti: “Woyambayo.” Yesu anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani kuti okhometsa msonkho ndiponso mahule akukusiyani mʼmbuyo nʼkukalowa mu Ufumu wa Mulungu. 32  Chifukwa Yohane anabwera kwa inu kudzakuphunzitsani njira yachilungamo, koma inu simunamukhulupirire. Koma okhometsa msonkho ndi mahule anamukhulupirira.+ Ngakhale kuti inu munaona zimenezi, simunasinthe maganizo anu nʼkuyamba kumukhulupirira. 33  Mvetserani fanizo lina: Panali munthu wina yemwe analima munda wa mpesa+ nʼkumanga mpanda kuzungulira mundawo. Komanso anakumba dzenje loponderamo mphesa nʼkumanga nsanja.+ Atatero anausiya mʼmanja mwa alimi nʼkupita kudziko lina.+ 34  Nyengo ya zipatso itafika, anatumiza akapolo ake kwa alimiwo kuti akatenge zipatso zake. 35  Koma alimiwo anagwira akapolo ake aja ndipo mmodzi anamumenya, wina anamupha, wina anamugenda ndi miyala.+ 36  Anatumizanso akapolo ena ambiri kuposa oyamba aja, koma amenewanso anawachitira zomwezo.+ 37  Pamapeto pake anawatumizira mwana wake, nʼkunena kuti, ‘Mwana wanga yekhayu akamulemekeza.’ 38  Alimiwo ataona mwanayo anayamba kukambirana kuti, ‘Eyaa! uyu ndi amene adzalandire cholowa.+ Bwerani, tiyeni timuphe nʼkutenga cholowa chakecho!’ 39  Choncho anamugwira nʼkumutulutsa mʼmunda wa mpesawo ndipo anamumupha.+ 40  Ndiye kodi mwiniwake wa munda wa mpesa uja akadzabwera, adzachita nawo chiyani alimiwo?” 41  Iwo anayankha kuti: “Chifukwa chakuti ndi oipa, adzawawononga koopsa ndipo munda wa mpesawo adzaupereka kwa alimi ena, amene angamupatse zipatso mʼnyengo yake.” 42  Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Paja Malemba amanena kuti, ‘Mwala umene omanga nyumba anaukana wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.*+ Umenewu wachokera kwa Yehova* ndipo ndi wodabwitsa mʼmaso mwathu.+ Kodi simunawerenge zimeneziʼ? 43  Nʼchifukwa chake ndikukuuzani kuti, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu nʼkuperekedwa ku mtundu wobereka zipatso zake. 44  Komanso munthu amene adzagwere pamwala umenewu adzaphwanyika.+ Ndipo aliyense amene mwalawo udzamugwere, adzanyenyeka.”+ 45  Ansembe aakulu ndi Afarisi atamva mafanizo akewa, anazindikira kuti akunena za iwowo.+ 46  Komabe ngakhale kuti ankafuna kumugwira,* ankaopa gulu la anthu chifukwa anthuwo ankakhulupirira kuti iye ndi mneneri.+

Mawu a M'munsi

Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mutu wa kona.”
Kapena kuti, “kumumanga.”