Wolembedwa ndi Mateyu 4:1-25

  • Mdyerekezi anayesa Yesu (1-11)

  • Yesu anayamba kulalikira ku Galileya (12-17)

  • Anasankha ophunzira oyambirira (18-22)

  • Yesu ankalalikira, kuphunzitsa komanso kuchiritsa (23-25)

4  Kenako mzimu unatsogolera Yesu kuchipululu ndipo kumeneko anayesedwa+ ndi Mdyerekezi.+  Atasala kudya masiku 40 masana ndi usiku, anamva njala.  Ndiyeno Woyesayo+ anabwera nʼkumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, uzani miyalayi kuti isanduke mitanda ya mkate.”  Koma iye anayankha kuti, “Malemba amati: ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu alionse ochokera mʼkamwa mwa Yehova.’”*+  Kenako Mdyerekezi anamutenga nʼkupita naye mumzinda woyera,+ ndipo anamukweza pamwamba pa khoma la mpanda wa kachisi*+  nʼkumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu mudziponye pansi, paja Malemba amati: ‘Iye adzalamula angelo ake zokhudza inu,’ komanso amati, ‘Adzakunyamulani mʼmanja mwawo, kuti phazi lanu lisawombe mwala.’”+  Koma Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amanenanso kuti: ‘Yehova* Mulungu wanu musamamuyese.’”+  Kenako Mdyerekezi anamutenganso nʼkupita naye paphiri lalitali kwambiri ndipo anamuonetsa maufumu onse apadziko ndi ulemerero wawo.+  Ndiyeno anamuuza kuti: “Ndikupatsani zinthu zonsezi ngati mutagwada pansi kamodzi kokha nʼkundilambira.” 10  Koma Yesu anamuyankha kuti: “Choka Satana! Chifukwa Malemba amati, ‘Yehova* Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira+ ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.’”+ 11  Kenako Mdyerekezi uja anamusiya+ ndipo kunabwera angelo nʼkuyamba kumutumikira.+ 12  Tsopano Yesu atamva kuti Yohane amutsekera mundende,+ anachoka kumeneko nʼkupita ku Galileya.+ 13  Kenako atachoka ku Nazareti, anafika ku Kaperenao+ nʼkupeza malo okhala mʼmbali mwa nyanja mʼzigawo za Zebuloni ndi Nafitali, 14  kuti mawu amene Mulungu ananena kudzera mwa mneneri Yesaya akwaniritsidwe. Iye ananena kuti: 15  “Anthu amene akukhala mʼdziko la Zebuloni ndi dziko la Nafitali, mʼmbali mwa msewu wakunyanja kutsidya lina la Yorodano, ku Galileya kumene kunkakhala anthu a mitundu ina, 16  anthu amene ankakhala mumdima anaona kuwala kwakukulu, ndipo anthu amene ankakhala mʼdera lamthunzi wa imfa, kuwala+ kunawaunikira.”+ 17  Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikira kuti: “Lapani, chifukwa Ufumu wakumwamba wayandikira.”+ 18  Pamene ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya,* Yesu anaona amuna awiri apachibale akuponya ukonde wophera nsomba mʼnyanja. Iwo anali asodzi ndipo mayina awo anali Simoni wotchedwa Petulo+ ndi Andireya.+ 19  Iye anawauza kuti: “Nditsatireni ndipo ndikusandutsani asodzi a anthu.”+ 20  Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde awo nʼkumutsatira.+ 21  Atadutsa pamenepo, anaona amuna enanso awiri apachibale, Yakobo mwana wa Zebedayo ndi mchimwene wake Yohane.+ Iwo anali mʼngalawa limodzi ndi bambo awo, a Zebedayo, akusoka maukonde awo, ndipo anawaitana.+ 22  Nthawi yomweyo anasiya ngalawa ija ndi bambo awo nʼkumutsatira. 23  Atatero, anayendayenda mʼGalileya+ yense ndipo ankaphunzitsa mʼmasunagoge+ mwawo, ankalalikira uthenga wabwino wa Ufumu komanso ankachiritsa matenda amtundu uliwonse amene anthu ankadwala.+ 24  Choncho mbiri yake inafalikira mu Siriya monse. Anthu anamubweretsera onse amene ankadwala matenda osiyanasiyana komanso amene ankamva kupweteka mʼthupi,+ ogwidwa ndi ziwanda,+ akhunyu+ komanso anthu akufa ziwalo ndipo iye anawachiritsa. 25  Choncho anthu ambirimbiri ochokera ku Galileya, ku Dekapoli,* ku Yerusalemu, ku Yudeya komanso kutsidya lina la Yorodano, anamutsatira.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “anamukweza pamalo okwera kwambiri a kachisi.”
MʼBaibulo, “nyanja ya Galileya” imatchulidwanso ndi mayina akuti, nyanja ya Kinereti, nyanja ya Genesarete komanso nyanja ya Tiberiyo.
Kapena kuti, “Chigawo cha Mizinda 10.”