Mika 2:1-13

  • Tsoka kwa opondereza anzawo (1-11)

  • Aisiraeli anagwirizanitsidwa (12, 13)

    • Mʼdziko mudzadzaza phokoso la anthu (12)

2  “Tsoka kwa anthu amene amakonza chiwembu,Amene akagona pabedi pawo, amaganizira kuti achite zoipa. Ndipo mʼmawa kukacha, amazichitadi.Chifukwa ali ndi mphamvu zochitira zimenezo.+  2  Iwo amalakalaka minda ya anthu ena ndipo amaitenga.+Amalakalakanso nyumba za anthu ena nʼkuzitenga.Amatenga mwachinyengo nyumba ya munthu,+Ndipo amatenganso cholowa cha munthu.  3  Choncho Yehova wanena kuti: ‘Ndikukonza zobweretsa tsoka+ pa banja ili, tsoka limene simudzatha kulithawa.+ Anthu inu simudzayendanso modzikuza+ chifukwa idzakhala nthawi ya tsoka.+  4  Pa tsikulo anthu adzanena mwambi wokhudza anthu inu.Ndipo adzaimba nyimbo yokulirirani.+ Adzanena kuti: “Ife ndiye tatha basi!+ Wachititsa kuti cholowa cha anthu amtundu wathu chiperekedwe kwa anthu ena. Talandidwa cholowa chathu.+ Iye wapereka minda yathu kwa anthu osakhulupirika.”  5  Choncho simudzapezeka aliyense woyeza malo ndi chingwe,Amene azidzagawa malo mumpingo wa Yehova.  6  Amanena kuti: “Siyani kulalikira!Musalalikirenso zokhudza zinthu zimenezi.Sitidzachititsidwa manyazi.”  7  Inu a mʼnyumba ya Yakobo, kodi mukunena kuti: “Kodi mzimu wa Yehova sukuleza mtima? Kodi zochita zake ndi zimenezi?” Kodi mawu anga sapindulitsa anthu owongoka mtima?  8  Posachedwapa anthu anga enieni andiukira ngati mdani wanga. Anthu amene akuyenda molimba mtima, ngati anthu obwera kuchokera kunkhondo,Mumawavula mkanjo wawo wokongola kwambiri umene avala pamwamba pa zovala zawo.  9  Inu mwathamangitsa akazi amtundu wanga mʼnyumba zawo zabwino kwambiri.Mwalanda ana awo zinthu zabwino zimene ndinawadalitsa nazo ndipo simudzazibwezanso mpaka kalekale. 10  Nyamukani muzipita, chifukwa malowa si opumulirako. Popeza dzikoli ndi lodetsedwa+ liwonongedwa, ndipo liwonongedwa koopsa.+ 11  Munthu akatsatira zinthu zopanda pake ndi zachinyengo nʼkunena bodza lakuti: “Ndidzakulalikirani zokhudza vinyo ndi chakumwa choledzeretsa,” Adzangokhala mlaliki wa anthu awa.+ 12  Ndithu ndidzasonkhanitsa mbadwa zonse za Yakobo.Ndidzasonkhanitsa Aisiraeli otsala.+ Ndidzawabweretsa pamalo amodzi ngati gulu la nkhosa mʼkhola,Komanso ngati gulu la ziweto pamalo amsipu.+Kumeneko kudzakhala phokoso la anthu.’+ 13  Wogumula mpanda adzawatsogolera.Iwo adzakulitsa pogumulidwapo nʼkudutsa pageti.+ Mfumu yawo idzakhala patsogolo pawoNdipo Yehova adzawatsogolera.”+

Mawu a M'munsi