Mika 5:1-15

  • Wolamulira amene adzakhale wamphamvu padziko lonse (1-6)

    • Wolamulira adzachokera ku Betelehemu (2)

  • Anthu otsala adzakhala ngati mame komanso mkango (7-9)

  • Dziko lidzayeretsedwa (10-15)

5  “Iwe mzinda umene waukiridwa,Tsopano ukudzichekacheka.Adani atizungulira kuti atiukire.+ Iwo amenya woweruza wa Isiraeli patsaya ndi ndodo.+   Iwe Betelehemu Efurata,+Mzinda waungʼono kwambiri moti sungawerengedwe ngati umodzi mwa mizinda ya fuko la Yuda,Mwa iwe mudzatuluka munthu amene ndidzamusankhe kuti akhale wolamulira mu Isiraeli.+Munthu ameneyu wakhala alipo kuyambira kalekale, wakhala alipo kuyambira masiku akale.   Choncho Mulungu adzawasiya Aisiraeli,Mpaka pamene mkazi amene adzabereke, atabereka. Ndipo abale ake onse a munthuyo adzabwerera kwa Aisiraeli.   Iye adzaimirira nʼkuyamba kuweta nkhosa mothandizidwa ndi mphamvu za Yehova,+Ndiponso mʼdzina lalikulu la Yehova Mulungu wake. Anthu azidzakhala motetezeka,+Ndipo mphamvu zake zidzafika mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+   Iye adzabweretsa mtendere.+ Asuri akadzalowa mʼdziko lathu, akadzaponda nsanja zathu zolimba,+Tidzawatumizira abusa 7, inde atsogoleri* 8 a anthu kuti akathane nawo.   Atsogoleriwo adzalanga dziko la Asuri ndi lupanga,+Komanso dziko la Nimurodi+ mʼnjira zake zonse zolowera mʼdzikolo. Wolamulirayo adzatipulumutsa kwa Asuri,+Asuriwo akadzangofika mʼdziko lathu nʼkuponda nthaka yathu.   Mbadwa zotsala za Yakobo zidzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu,Ngati mame ochokera kwa Yehova.Komanso ngati mvula yowaza imene ikugwa pazomera,Yomwe sidalira munthuKapena kuyembekezera ana a anthu.   Mbadwa zotsala za Yakobo zidzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu.Zidzakhala pakati pa anthu ambiri.Ngati mkango pakati pa nyama zakutchire.Komanso ngati mkango wamphamvu pakati pa magulu ankhosa,Umene umadutsa pakati pa nkhosazo nʼkuzimbwandira ndiponso kuzikhadzulaNdipo palibe wozipulumutsa.   Dzanja lanu lidzakhala pamwamba pa adani anu,Ndipo adani anu onse adzaphedwa.” 10  Yehova wanena kuti, “Pa tsiku limenelo,Ndidzapha mahatchi* anu ndipo magaleta anu ndidzawawononga. 11  Ndidzagwetsa mizinda yamʼdziko lanu.Ndipo ndidzagumula malo anu onse okhala ndi mipanda yolimba kwambiri. 12  Ndidzathetsa zamatsenga zonse zimene mukuchita,Ndipo pakati panu sipadzapezekanso wochita zamatsenga.+ 13  Ndidzagwetsa zifaniziro zogoba ndi zipilala zopatulika zimene muli nazo,Ndipo simudzagwadiranso ntchito za manja anu.+ 14  Ndidzazula mizati* yanu yopatulika,+Nʼkuwononga mizinda yanu. 15  Ndidzabwezera mokwiya ndiponso mwaukaliAnthu a mitundu imene sinandimvere.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “akalonga.”
Ena amati “mahosi.”