Mika 7:1-20
7 Tsoka kwa ine, chifukwa ndili ngati munthu amene,Nthawi yokolola zipatso zamʼchilimwe* itatha,Komanso nthawi yokunkha mʼmunda umene akololamo mphesa itatha,Sanapeze mphesa zoti adye.Komanso nkhuyu zoyambirira zimene akulakalaka.
2 Anthu okhulupirika atha padziko lapansi.Pakati pa anthu palibe munthu wachilungamo.+
Onse amabisalira anzawo kuti akhetse magazi.+
Aliyense amasaka mʼbale wake ndi ukonde.
3 Manja awo amachita zoipa ndipo amazichita bwino kwambiri.+Kalonga amalamula kuti amupatse mphatso,Woweruza amauza anthu kuti amupatse chiphuphu.+Munthu wotchuka amauza anthu zimene akulakalaka,+Ndipo onsewa amakonzera limodzi chiwembu.
4 Munthu amene iwo amati ndi wabwino kwambiri, ali ngati minga,Ndipo munthu amene amati ndi wachilungamo kwambiri, ndi woipa kuposa mpanda wa mitengo yaminga.
Tsiku limene alonda awo ananena komanso limene adzaweruzidwe lidzafika ndithu.+
Pa tsikulo iwo adzathedwa nzeru.+
5 Musamakhulupirire anzanu.Musamadalire mnzanu wapamtima.+
Muzisamala ndi zimene mumauza amene mumagona naye pafupi.
6 Chifukwa mwana wamwamuna akunyoza bambo ake.Mwana wamkazi akutsutsana ndi mayi ake,+Ndipo mkazi wokwatiwa akutsutsana ndi apongozi ake aakazi.+Adani ake a munthu ndi anthu a mʼbanja lake.+
7 Koma ine ndidzayembekezera Yehova.+
Ndidzayembekezera moleza mtima Mulungu wa chipulumutso changa.+
Mulungu wanga adzandimvera.+
8 Iwe mdani* wanga, usasangalale chifukwa cha zimene zandichitikira.
Ngakhale kuti ndagwa, ndidzadzuka.Ngakhale kuti ndili mumdima, Yehova adzakhala kuwala kwanga.
9 Ndidzapirira mkwiyo wa Yehova,Chifukwa ndamuchimwira.+Ndidzaupirira mpaka ataweruza mlandu wanga nʼkundichitira chilungamo.
Iye adzandipititsa pamalo owala,Ndipo ndidzaona chilungamo chake.
10 Mdani wanga adzaonanso zimenezi,Ndipo manyazi adzagwira amene ankandinena kuti:
“Yehova Mulungu wako ali kuti?”+
Maso anga adzamuyangʼana.
Iye adzapondedwapondedwa ngati matope amumsewu.
11 Lidzakhala tsiku lomanga mpanda wako wamiyala.Pa tsiku limenelo malire adzakulitsidwa.*
12 Pa tsiku limenelo anthu adzabwera kwa iwe,Ochokera kudziko la Asuri ndi kumizinda ya ku Iguputo.Ochokera ku Iguputo mpaka ku Mtsinje.*Komanso ochokera kunyanja ina mpaka kunyanja ina ndiponso kuphiri lina mpaka kuphiri linanso.+
13 Dzikoli lidzakhala bwinja chifukwa cha anthu okhala mmenemo,Chifukwa cha zimene achita.*
14 Weta anthu ako ndi ndodo yako, gulu la nkhosa zomwe ndi cholowa chako,+Zimene zinkakhala zokhazokha mʼnkhalango komanso pakati pa mitengo ya zipatso.
Uzilole zikadyere ku Basana ndi ku Giliyadi+ ngati mmene zinkachitira kale.
15 “Ndidzakusonyezani zinthu zodabwitsa,Ngati mmene ndinachitira nthawi imene munkachokera ku Iguputo.+
16 Anthu a mitundu ina adzaona zodabwitsazo ndipo adzachita manyazi ngakhale kuti ndi amphamvu.+
Iwo adzagwira pakamwa,Ndipo makutu awo adzagontha.
17 Adzanyambita fumbi ngati njoka.+Ngati nyama zokwawa, adzatuluka akunjenjemera mʼmalo awo obisalamo.
Adzabwera kwa Yehova Mulungu akuchita mantha,Ndipo adzayamba kukuopani.”+
18 Kodi pali Mulungu winanso wofanana ndi inu,Amene amakhululukira zolakwa ndi machimo+ a anthu ake otsala omwe ndi cholowa chake?+
Inu simudzakhalabe wokwiya mpaka kalekale,Chifukwa mumakonda chikondi chokhulupirika.+
19 Inu mudzatichitiranso chifundo+ ndipo mudzagonjetsa* zolakwa zathu.
Machimo athu onse mudzawaponya mʼnyanja pamalo ozama.+
20 Yakobo mudzamusonyeza kukhulupirika.Abulahamu mudzamusonyeza chikondi chokhulupirika,Ngati mmene munalumbirira kwa makolo athu kalekale.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu akuti “zipatso za mʼchilimwe” makamaka amatanthauza nkhuyu ndipo nthawi zina amatanthauza zipatso za kanjedza.
^ Mawu a Chiheberi amene amasuliridwa kuti “mdani,” amanena za munthu wamkazi.
^ Mabaibulo ena amati, “Pa tsiku limenelo lamulo lidzakhala kutali.”
^ Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Chifukwa cha chipatso cha ntchito zawo.”
^ Kapena kuti, “mudzapondaponda.”