Miyambo 10:1-32
10 Miyambi ya Solomo.+
Mwana wanzeru amasangalatsa bambo ake,+Koma mwana wopusa amamvetsa chisoni mayi ake.
2 Chuma chimene munthu wapeza chifukwa chochita zoipa chidzakhala chopanda phindu,Koma chilungamo nʼchimene chimapulumutsa munthu ku imfa.+
3 Yehova sadzachititsa kuti munthu wolungama akhale ndi njala,+Koma anthu oipa sadzawapatsa zimene amalakalaka.
4 Munthu waulesi adzakhala wosauka,+Koma wogwira ntchito mwakhama adzalemera.+
5 Mwana wochita zinthu mozindikira amatuta zokolola mʼchilimwe,Koma mwana wochititsa manyazi amakhala ali mʼtulo tofa nato pa nthawi yokolola.+
6 Madalitso amapita pamutu pa munthu wolungama,+Koma pakamwa pa anthu oipa pamabisa zachiwawa.
7 Zabwino zimene munthu wolungama ankachita zikakumbukiridwa* amadalitsidwa,+Koma dzina la anthu oipa lidzawola.+
8 Munthu wanzeru mumtima mwake amamvera malangizo,*+Koma wolankhula mopusa adzapeza mavuto.+
9 Munthu wochita zinthu mokhulupirika adzakhala wotetezeka,+Koma munthu wochita zinthu mwachinyengo adzadziwika.+
10 Munthu amene amatsinzinira ena diso amachititsa ena kumva chisoni,+Ndipo amene amalankhula mopusa adzapeza mavuto.+
11 Pakamwa pa wolungama pamachokera moyo,+Koma pakamwa pa anthu oipa pamabisa zachiwawa.+
12 Chidani nʼchimene chimayambitsa mikangano,Koma chikondi chimaphimba machimo onse.+
13 Nzeru imapezeka pamilomo ya munthu wozindikira,+Koma ndodo amakwapulira msana wa munthu wopanda nzeru.+
14 Anzeru ndi amene amapitiriza kuphunzira zinthu zamtengo wapatali,+Koma pakamwa pa wopusa pamachititsa kuti awonongedwe.+
15 Munthu wolemera amaona kuti chuma chake chili* ngati mzinda wokhala ndi mpanda wolimba.
Koma anthu osauka amavutika chifukwa cha umphawi wawo.+
16 Zochita za wolungama zimabweretsa moyo.Koma zochita za woipa zimabweretsa tchimo.+
17 Amene amamvera malangizo* amathandiza ena kukapeza moyo,*Koma amene amanyalanyaza chidzudzulo amasocheretsa ena.
18 Munthu amene amabisa chidani mumtima mwake amalankhula mabodza,+Ndipo amene amafalitsa mphekesera zoipa ndi wopusa.
19 Mawu akachuluka sipalephera kukhala zolakwika,+Koma amene amalamulira milomo yake amachita zinthu mwanzeru.+
20 Lilime la wolungama lili ngati siliva wabwino kwambiri,+Koma mtima wa woipa ndi wopanda phindu.
21 Milomo ya wolungama imathandiza* anthu ambiri,+Koma zitsiru zimafa chifukwa chopanda nzeru.+
22 Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa munthu,+Ndipo popereka madalitsowa Mulungu sawonjezerapo ululu.*
23 Kwa munthu wopusa, kuchita khalidwe lochititsa manyazi kuli ngati masewera,Koma munthu wozindikira amakhala ndi nzeru.+
24 Chinthu chimene munthu woipa amaopa nʼchimene chidzamuchitikire,Koma anthu olungama adzapatsidwa zimene amalakalaka.+
25 Mphepo yamkuntho ikawomba woipa amawonongedwa,+Koma wolungama ali ngati maziko mpaka kalekale.+
26 Viniga* amachititsa kuti mano ayezimire ndipo utsi umapweteka mʼmaso,Izi nʼzimene munthu waulesi amachita kwa munthu amene wamutuma.*
27 Kuopa Yehova kumatalikitsa moyo,+Koma zaka za anthu oipa zidzafupikitsidwa.+
28 Zimene anthu olungama akuyembekezera zimasangalatsa,*+Koma chiyembekezo cha anthu oipa sichidzakwaniritsidwa.+
29 Njira ya Yehova ndi malo achitetezo kwa munthu wopanda cholakwa,+Koma anthu ochita zoipa amawonongedwa mʼnjira imeneyi.+
30 Wolungama sadzagwetsedwa,+Koma anthu oipa sadzakhalanso padziko lapansi.+
31 Pakamwa pa munthu wolungama pamalankhula* zanzeru,Koma lilime lolankhula zinthu zopotoka lidzadulidwa.
32 Milomo ya munthu wolungama imadziwa zinthu zosangalatsa,Koma pakamwa pa anthu oipa mʼpachinyengo.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Mbiri yake ikakumbukiridwa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “malamulo.”
^ Kapena kuti, “amaona kuti zinthu zake zamtengo wapatali zili.”
^ Mabaibulo ena amati, “akuyenda panjira ya kumoyo.”
^ Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.
^ Kapena kuti, “imatsogolera.”
^ Kapena kuti, “chisoni; mavuto.”
^ “Viniga” ndi chakumwa chowawasira chomwe chinkapangidwa kuchokera ku vinyo wosasa kapena zakumwa zina zoledzeretsa.
^ Kapena kuti, “kwa amene anamulemba ntchito.”
^ Kapena kuti, “Chiyembekezo cha anthu olungama chimasangalatsa.”
^ Kapena kuti, “pamabereka zipatso.”