Miyambo 12:1-28

  • Amene amadana ndi kudzudzulidwa ndi wosaganiza bwino (1)

  • “Mawu a munthu amene amalankhula asanaganize amalasa ngati lupanga” (18)

  • Amene amalimbikitsa mtendere amasangalala (20)

  • Milomo yonama imamunyansa Yehova (22)

  • Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauweramitsa (25)

12  Munthu amene amakonda malangizo* amakondanso kudziwa zinthu,+Koma amene amadana ndi kudzudzulidwa ndi wosaganiza bwino.*+   Yehova amasangalala ndi munthu wabwino,Koma munthu amene amakonza mapulani ochita zinthu zoipa, Mulungu amamuweruza kuti ndi wolakwa.+   Palibe munthu amene angakhale wotetezeka chifukwa chochita zoipa,+Koma anthu olungama sadzazulidwa.   Mkazi wamakhalidwe abwino ndi chisoti cha ulemu kwa mwamuna wake,+Koma mkazi wochita zinthu zochititsa manyazi ali ngati matenda amene amawoletsa mafupa a mwamunayo.+   Maganizo a anthu olungama ndi achilungamo,Koma malangizo a anthu oipa ndi achinyengo.   Mawu a anthu oipa ali ngati msampha wakupha,*+Koma pakamwa pa anthu owongoka mtima pamawapulumutsa.+   Anthu oipa akagonjetsedwa sakhalaponso,Koma nyumba ya anthu olungama idzakhalapobe.+   Munthu amatamandidwa chifukwa cholankhula zinthu zanzeru,+Koma amene ali ndi mtima wopotoka adzanyozedwa.+   Kuli bwino kukhala munthu wamba koma nʼkukhala ndi wantchito,Kusiyana nʼkukhala wodzikuza koma wopanda chakudya.+ 10  Wolungama amasamalira ziweto zake,+Koma munthu woipa amaganiza kuti ndi wachifundo, pamene ali wankhanza. 11  Amene amalima munda wake adzakhala ndi chakudya chokwanira,+Koma amene amafunafuna zinthu zopanda pake ndi wopanda nzeru. 12  Munthu woipa amasirira nyama imene anthu ena oipa agwira,Koma muzu wa anthu olungama umabala zipatso. 13  Munthu woipa amakodwa ndi zolankhula zake zochimwa,+Koma wolungama amapulumuka pamavuto. 14  Munthu amasangalala ndi zinthu zabwino chifukwa cha mawu ake abwino,*+Ndipo ntchito za manja ake zidzamupindulira. 15  Njira ya munthu wopusa imakhala yolondola mʼmaso mwake,+Koma munthu wanzeru amalandira malangizo.*+ 16  Munthu wopusa amasonyeza kuti wakhumudwa nthawi yomweyo,*+Koma munthu wochenjera akachitiridwa chipongwe, amangozinyalanyaza.* 17  Munthu woona mtima akamapereka umboni amalankhula zoona,*Koma mboni yonama imanena zachinyengo. 18  Mawu a munthu amene amalankhula asanaganize amalasa ngati lupanga,Koma lilime la anthu anzeru limachiritsa.+ 19  Milomo imene imalankhula zoona idzakhalapo mpaka kalekale,+Koma lilime labodza lidzangokhalapo kwa kanthawi kochepa.+ 20  Chinyengo chimakhala mumtima mwa anthu okonza chiwembu,Koma amene amalimbikitsa mtendere* amasangalala.+ 21  Palibe chopweteka chimene chidzagwere wolungama,+Koma anthu oipa ndi amene adzakumane ndi mavuto ambiri.+ 22  Yehova amanyansidwa ndi milomo yonama,+Koma anthu amene amachita zinthu mokhulupirika amamusangalatsa. 23  Munthu wochenjera amabisa zimene akudziwa,Koma mtima wa munthu wopusa umangolankhula zinthu zosonyeza kupusa kwake.+ 24  Dzanja la anthu akhama lidzalamulira anthu,+Koma manja aulesi adzagwira ntchito yokakamiza.+ 25  Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauweramitsa,+Koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.+ 26  Wolungama amafufuza malo abwino odyetserako ziweto zake,Koma njira ya anthu oipa imawasocheretsa. 27  Munthu waulesi akamasaka sathamangitsa nyama imene akufuna kupha,+Koma khama ndi chuma chamtengo wapatali cha munthu. 28  Njira yachilungamo imathandiza munthu kuti akhale ndi moyo,+Ndipo mʼnjira yake mulibe imfa.

Mawu a M'munsi

Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga, kapena uphungu.
Kapena kuti, “wopanda nzeru.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “munthu amene amadikirira kuti akhetse magazi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakamwa pake.”
Kapena kuti, “uphungu.”
Kapena kuti, “tsiku lomwelo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amangoziphimba.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “zachilungamo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “alangizi a mtendere.”