Miyambo 19:1-29
19 Ndi bwino kukhala wosauka nʼkumachita zinthu mokhulupirika+Kusiyana nʼkukhala munthu wopusa nʼkumalankhula mabodza.+
2 Munthu wosadziwa zinthu si wabwino,+Ndipo amene amachita zinthu mopupuluma* akuchimwa.
3 Kupusa kwa munthu nʼkumene kumapotoza njira yake,Ndipo mtima wake umakwiyira Yehova.
4 Chuma chimachititsa kuti munthu akhale ndi anzake ambiri,Koma munthu wosauka amasiyidwa ngakhale ndi mnzake weniweni.+
5 Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,+Ndipo amene amalankhula zabodza zokhazokha sadzathawa chilango.+
6 Anthu ambiri amafuna kukondedwa ndi munthu wolemekezeka,*Ndipo aliyense ndi bwenzi la munthu wopereka mphatso.
7 Abale ake onse a munthu wosauka amadana naye,+Kuwonjezera pamenepo anzake amamupewa,+
Iye amawachonderera kuti amuthandize, koma palibe amene amamuyankha.
8 Munthu amene wapeza nzeru amakonda moyo wake.+
Amene amaona kuti kukhala wozindikira nʼkofunika kwambiri zinthu zidzamuyendera bwino.+
9 Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,Ndipo amene amalankhula zabodza zokhazokha adzawonongedwa.+
10 Nʼzosayenera kuti munthu wopusa azikhala moyo wawofuwofu.Chimodzimodzinso kuti munthu wantchito alamulire anthu audindo!+
11 Kuzindikira kumachititsa kuti munthu abweze mkwiyo wake,+Ndipo kunyalanyaza cholakwa kumamʼchititsa kukhala wokongola.+
12 Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango wamphamvu,+Koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pazomera.
13 Mwana wopusa amabweretsa mavuto kwa bambo ake,+Ndipo mkazi wolongolola* ali ngati denga limene silisiya kudontha.+
14 Nyumba komanso chuma ndi cholowa chochokera kwa makolo,Koma mkazi wanzeru amachokera kwa Yehova.+
15 Ulesi umabweretsa tulo tofa nato,Ndipo munthu waulesi adzakhala ndi njala.+
16 Amene amasunga lamulo amasunga moyo wake.+Amene amachita zinthu mosasamala adzafa.+
17 Amene amakomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova,+Ndipo adzamʼbwezera* zimene anachitazo.+
18 Langa mwana wako padakali chiyembekezo,+Ndipo usakhale ndi mlandu wochititsa* kuti afe.+
19 Munthu wosachedwa kupsa mtima ayenera kulipira,Chifukwa ukayesa kumʼpulumutsa, uzichita zimenezi kawirikawiri.+
20 Mvera uphungu ndipo utsatire malangizo*+Kuti udzakhale wanzeru mʼtsogolo.+
21 Munthu amakhala ndi mapulani ambiri mumtima mwake,Koma zolinga za Yehova nʼzimene zidzakwaniritsidwe.+
22 Chinthu chosiririka mwa munthu ndi chikondi chake chokhulupirika,+Ndipo ndi bwino kukhala wosauka kusiyana nʼkukhala munthu wonama.
23 Kuopa Yehova kumathandiza munthu kuti apeze moyo.+Munthu amene amachita zimenezi amagona tulo tokoma ndipo zoipa sizimugwera.+
24 Munthu waulesi amapisa dzanja lake mʼmbale ya chakudya,Koma nʼkulephera kulibweretsa pakamwa.+
25 Menya munthu wonyoza+ kuti wosadziwa zinthu achenjere,+Ndipo dzudzula munthu womvetsa zinthu kuti awonjezere zimene akudziwa.+
26 Munthu amene amazunza bambo ake ndiponso kuthamangitsa mayi ake,Ndi mwana wochititsa manyazi ndi wonyozetsa.+
27 Mwana wanga ukasiya kumvera malangizo,Udzasochera nʼkusiya kutsatira mawu anzeru.
28 Mboni yopanda pake imanyoza chilungamo,+Munthu woipa amasangalala kuchita zoipa ngati mmene amasangalalira ndi chakudya.+
29 Zilango amazisungira anthu onyoza,+Ndipo zikwapu ndi zokwapulira msana wa anthu opusa.+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amayenda mofulumira ndi mapazi ake.”
^ Kapena kuti, “wowolowa manja.”
^ Kapena kuti, “wokonda kudandaula.”
^ Kapena kuti, “adzamʼpatsa mphoto pa.”
^ Kapena kuti, “Ndipo usalakelake.”
^ Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.