Miyambo 20:1-30

  • Womwa vinyo wambiri amayamba kunyoza (1)

  • Waulesi salima nthawi yozizira (4)

  • Maganizo amumtima mwa munthu ali ngati madzi akuya (5)

  • Chenjezo pa nkhani yolumbira usanaganize bwino (25)

  • Ulemerero wa anyamata ndi mphamvu zawo (29)

20  Munthu amene amamwa vinyo wambiri amayamba kunyoza+ ndipo amene amamwa mowa wambiri amachita zosokoneza.+Aliyense amene amasochera ndi zinthu zimenezi alibe nzeru.+   Kuopsa kwa mfumu kuli ngati kubangula kwa mkango wamphamvu.+Aliyense woputa mkwiyo wake akuika moyo wake pangozi.+   Munthu amalemekezeka akapewa mkangano,+Koma aliyense wopusa amafulumira kuyambitsa mkangano.+   Waulesi salima nthawi yozizira,Choncho iye azidzapemphapempha nthawi yokolola chifukwa adzakhala alibe kanthu.*+   Maganizo amumtima* mwa munthu ali ngati madzi akuya,Koma munthu wozindikira ndi amene amawatunga.   Anthu ambiri amanena kuti ali ndi chikondi chokhulupirika,Koma ndi ndani amene angapeze munthu wokhulupirika?   Munthu wolungama amachita zinthu mokhulupirika.+ Ana ake ndi osangalala.+   Mfumu ikakhala pampando wachifumu kuti iweruze,+Maso ake amazindikira* anthu onse oipa.+   Ndi ndani anganene kuti: “Ndayeretsa mtima wanga.+Ndine woyera ku tchimo langa”?+ 10  Miyala yachinyengo yoyezera komanso miyezo yachinyengo,*Zonsezi nʼzonyansa kwa Yehova.+ 11  Ngakhale mwana* amadziwika ndi zochita zake,Ngati khalidwe lake lili loyera ndiponso labwino.+ 12  Khutu lakumva ndiponso diso loona,Zonsezi anazipanga ndi Yehova.+ 13  Usamakonde tulo chifukwa ungasauke.+ Tsegula maso ako ndipo udzakhala ndi chakudya chambiri.+ 14  Wogula amanena kuti, “chinthu ichi si chabwino, si chabwino chimenechi!”Kenako amachoka ndipo amayamba kudzitama.+ 15  Pali golide komanso miyala yambiri yamtengo wapatali ya korali,*Koma milomo yodziwa zinthu ndi yamtengo wapatali.+ 16  Ngati munthu walonjeza kuti akhala chikole kwa mlendo, umulande chovala chake.+Komanso umulande chikole ngati walonjeza zimenezi kwa mkazi wachilendo.+ 17  Chakudya chimene munthu wachipeza mwachinyengo chimamukomera,Koma pambuyo pake mʼkamwa mwake mumadzaza miyala.+ 18  Anthu akakambirana zolinga zawo zimakwaniritsidwa,*+Ndipo uzitsatira malangizo anzeru pomenya nkhondo yako.+ 19  Wonenera anzake zoipa amayendayenda nʼkumaulula zinsinsi.+Usamagwirizane ndi munthu amene amakonda kunena miseche.* 20  Aliyense amene amatemberera bambo ake komanso mayi ake,Nyale yake idzazimitsidwa kukagwa mdima.+ 21  Munthu akapeza cholowa mwadyera,Pamapeto pake Mulungu sadzamudalitsa.+ 22  Usanene kuti: “Ndidzabwezera choipa.”+ Yembekezera Yehova+ ndipo iye adzakupulumutsa.+ 23  Miyala yachinyengo* yoyezera ndi yonyansa kwa Yehova,Ndipo masikelo achinyengo si abwino. 24  Yehova ndi amene amatsogolera mapazi a munthu.+Ndiye munthu payekha angadziwe bwanji njira yoyenera kuyenda? 25  Umakhala msampha munthu akathamangira kufuula kuti, “Nʼzoyera!”+ Koma pambuyo polonjeza nʼkuyamba kuganiziranso bwino zimene walonjezazo.+ 26  Mfumu yanzeru imazindikira anthu oipa,+Ndipo imawaponda ndi wilo lopunthira mbewu.+ 27  Mpweya wa munthu ndi nyale ya Yehova.Imafufuza zinthu zamkati mwa mtima wake. 28  Kukhulupirika komanso chikondi chokhulupirika zimateteza mfumu.+Mfumuyo ikamasonyeza chikondi chokhulupirika, mpando wake wachifumu umakhazikika.+ 29  Ulemerero wa anyamata ndi mphamvu zawo,+Ndipo ulemerero wa anthu achikulire ndi imvi zawo.+ 30  Mabala obwera chifukwa chopatsidwa chilango amachotsa zoipa,+Ndipo zikwapu zimayeretsa mtima wa munthu.

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “Pa nthawi yokolola adzafunafuna zinthu koma sadzazipeza.”
Kapena kuti, “Zolinga zamumtima.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Malangizo amumtima.”
Kapena kuti, “amapeta.”
Kapena kuti, “Miyala iwiri yosiyana yoyezera ndiponso zinthu ziwiri zosiyana zoyezera.”
Kapena kuti, “mnyamata.”
Kapena kuti, “zimakhazikika.”
Kapena kuti, “amene amakonda kukopa ena ndi milomo yake.”
Kapena kuti, “miyala iwiri yosiyana yoyezera.”