Miyambo 24:1-34

  • Usachitire nsanje anthu oipa (1)

  • Nzeru zimamanga nyumba ya munthu (3)

  • Munthu wolungama angagwe koma adzadzukanso (16)

  • Musamabwezere (29)

  • Kugona kumabweretsa umphawi (33, 34)

24  Usamasirire anthu oipa,Ndipo usamalakelake utakhala pagulu lawo,+   Chifukwa mtima wawo umangoganizira zochita chiwawa,Ndipo milomo yawo imangokhalira kulankhula zobweretsera ena mavuto.   Nzeru zimamanga nyumba ya* munthu,+Ndipo kuzindikira kumachititsa kuti ilimbe kwambiri.   Kudziwa zinthu kumachititsa kuti zipinda za nyumbayo zidzazeNdi zinthu zonse zamtengo wapatali ndiponso zosangalatsa.+   Munthu wanzeru ndi wamphamvu,+Ndipo akakhala wodziwa zinthu amawonjezera mphamvu zake.   Ukamatsatira malangizo anzeru udzatha kumenya nkhondo yako,+Ndipo pakakhala alangizi* ambiri udzapambana.*+   Kwa munthu wopusa nʼzosatheka kupeza nzeru zenizeni.+Ndipo amakhala alibe chilichonse choti anganene pageti la mzinda.   Aliyense wokonzera anzake ziwembuAdzatchedwa katswiri wokonza ziwembu.+   Mapulani a munthu* wopusa amamupangitsa kuti achite tchimo,Ndipo anthu amanyansidwa ndi munthu wonyoza.+ 10  Ukafooka pa nthawi imene ukukumana ndi mavuto,Mphamvu zako zidzachepa. 11  Pulumutsa anthu amene atengedwa kuti akaphedwe,Ndipo amene akuyenda modzandira popita kukaphedwa uwathandize.+ 12  Ukanena kuti: “Ifetu zimenezi sitimazidziwa,” Kodi amene amafufuza mitima sazindikira zimene zili mʼmaganizo mwako?+ Ndithudi, amene amakuyangʼanitsitsa adzadziwaNdipo adzabwezera munthu aliyense mogwirizana ndi zochita zake.+ 13  Mwana wanga, idya uchi chifukwa ndi wabwino.Uchi wochokera pazisa za njuchi umatsekemera. 14  Mofanana ndi zimenezi, dziwa kuti nzeru ndi zabwino kwa iwe.*+ Ukazipeza, udzakhala ndi tsogolo labwinoNdipo chiyembekezo chako sichidzawonongedwa.+ 15  Mofanana ndi munthu woipa, usamabisalire munthu wolungama pafupi ndi nyumba yake kuti umuchitire chiwembu.Usamawononge malo ake okhala. 16  Chifukwa munthu wolungama akhoza kugwa maulendo 7 ndipo adzadzukanso,+Koma anthu oipa adzakumana ndi tsoka ndipo adzagwa.+ 17  Mdani wako akagwa usamasangalale,Ndipo akapunthwa, mtima wako usamakondwere.+ 18  Ukachita zimenezi Yehova adzaona ndipo zidzamuipiraMoti adzachotsa mkwiyo wake pa mdani wakoyo.+ 19  Usamapse mtima chifukwa cha anthu ochita zoipa.Usamasirire anthu oipa, 20  Chifukwa aliyense woipa alibe tsogolo,+Ndipo nyale ya anthu oipa idzazimitsidwa.+ 21  Mwana wanga uziopa Yehova komanso mfumu.+ Ndipo usamakhale pagulu la anthu ofuna kuti zinthu zisinthe,+ 22  Chifukwa tsoka lawo lidzabwera modzidzimutsa.+ Ndipo ndi ndani amene angadziwe za tsoka limene onsewa* adzawabweretsere?+ 23  Mawu awanso ndi a anthu anzeru: Si bwino kukondera poweruza mlandu.+ 24  Aliyense amene amauza munthu woipa kuti, “Ndiwe wolungama,”+ Anthu adzamutemberera ndipo mitundu ya anthu idzaitanira tsoka pa iye. 25  Koma anthu amene amamudzudzula zinthu zidzawayendera bwino.+Adzalandira madalitso a zinthu zabwino.+ 26  Anthu adzakisa milomo ya munthu amene amayankha moona mtima.*+ 27  Konzekera ntchito yako yapanja, ndipo uonetsetse kuti ntchito yonse yatheka mʼmunda wako.Ukatero ukamange nyumba yako.* 28  Usapereke umboni wotsutsana ndi mnzako ngati ulibe umboni weniweni.+ Usapusitse anthu ena ndi milomo yako.+ 29  Usanene kuti: “Ndimuchitira zimene iye wandichitira.Ndimubwezera zimene anandichitira.”+ 30  Ndinadutsa pamunda pa munthu waulesi,+Pamunda wa mpesa wa munthu wopanda nzeru. 31  Ndinaona kuti munali tchire lokhalokha.Zitsamba zoyabwa zinali paliponse mʼmundamo,Komanso mpanda wake wamiyala unali utagumuka.+ 32  Nditaona zimenezi, ndinayamba kuziganizira mumtima mwanga,Ndipo ndinaphunzirapo kuti: 33  Ukapitiriza kugona pangʼono, ukapitiriza katulo pangʼono,Ukapitiriza kupinda manja pangʼono kuti upume, 34  Umphawi wako udzabwera ngati wachifwamba,Ndipo kusauka kwako kudzabwera ngati munthu wokhala ndi zida.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “banja la.”
Kapena kuti, “aphungu.”
Kapena kuti, “zinthu zidzakuyendera bwino; udzapulumuka.”
Kapena kuti, “Ziwembu za munthu.”
Kapena kuti, “nʼzotsekemera kwa iwe.”
Kutanthauza Yehova komanso mfumu.
Mabaibulo ena amati, “Kuyankha mosapita mʼmbali kuli ngati kukisa munthu.”
Kapena kuti, “ukalimbitse banja lako.”