Miyambo 25:1-28
25 Miyambi ina ya Solomo+ imene atumiki a Hezekiya+ mfumu ya Yuda anakopera ndi iyi:
2 Kusunga chinsinsi ndi ulemerero wa Mulungu,+Ndipo ulemerero wa mafumu ndi kufufuza bwino nkhani.
3 Nʼzosatheka kufufuza kutalika kwa kumwamba komanso kuzama kwa dziko lapansi,Nʼchimodzimodzinso mitima ya mafumu.
4 Yengani siliva nʼkuchotsa zonse zosafunika,Ndipo yense adzatuluka woyengeka bwino.+
5 Chotsani woipa pamaso pa mfumu,Ndipo mpando wake wachifumu udzakhazikika chifukwa cha chilungamo.+
6 Usadzilemekeze wekha pamaso pa mfumu,+Ndipo usakhale pakati pa anthu olemekezeka,+
7 Chifukwa ndi bwino kuti mfumuyo ikuuze kuti, “Bwera udzakhale apa,”
Kusiyana nʼkuti ikuchititse manyazi pamaso pa munthu wolemekezeka.+
8 Usamafulumire kupititsa mlandu kukhoti,Chifukwa udzachita chiyani mnzako akadzapereka umboni wosonyeza kuti iweyo ndi wolakwa?+
9 Thetsa nkhaniyo pokambirana ndi mnzakoyo,+Koma usaulule nkhani zachinsinsi zimene unauzidwa,*+
10 Kuti amene akumvetsera asakuchititse manyaziKomanso kuti usafalitse nkhani yoipa* imene sungathe kuithetsa kuti isapitirize kufalikira.
11 Mawu olankhulidwa pa nthawi yoyenera+Ali ngati zipatso za maapozi agolide mʼmbale zasiliva.
12 Munthu wanzeru akamadzudzula munthu wa khutu lomvetsera+Amakhala ngati ndolo yagolide ndiponso ngati chokongoletsera chagolide woyenga bwino.
13 Nthumwi yokhulupirika kwa anthu amene aitumaIli ngati kuzizira kwa sinowo* pa tsiku lokolola,Chifukwa imatsitsimula moyo wa abwana ake.+
14 Munthu wodzitama kuti apereka mphatso koma nʼkulephera kupereka,+Ali ngati mitambo komanso mphepo yosabweretsa mvula.
15 Chifukwa cha kuleza mtima munthu angathe kunyengerera munthu waudindo,Ndipo mawu okoma akhoza* kuthyola fupa.+
16 Ukapeza uchi udye umene ungakukwane,Chifukwa ukadya wambiri ungathe kuusanza.+
17 Phazi lako lisamapitepite kunyumba kwa mnzako,Kuti angatope nawe nʼkuyamba kudana nawe.
18 Munthu wopereka umboni wabodza pa mlandu wa mnzake+Ali ngati chibonga chakunkhondo, lupanga, komanso muvi wakuthwa.
19 Kukhulupirira munthu wosadalirika* pa nthawi yamavutoKuli ngati dzino lothyoka komanso phazi lotsimphina.
20 Amene amaimbira nyimbo munthu amene ali ndi chisoni mumtima mwake+Ali ngati munthu amene amavula chovala pa tsiku lozizira,Komanso ngati viniga* amene wathiridwa musoda
21 Ngati mdani wako* ali ndi njala, umʼpatse chakudya.Ngati ali ndi ludzu, umʼpatse madzi akumwa,+
22 Ukachita zimenezi ndiye kuti ukumuunjikira makala amoto pamutu pake,*+Ndipo Yehova adzakupatsa mphoto.
23 Mphepo yakumpoto imabweretsa mvula yambiriNdipo lilime lonena miseche limachititsa kuti anthu akhale ndi nkhope zolusa.+
24 Ndi bwino kukhala pakona ya denga la nyumbaKusiyana ndi kukhala mʼnyumba limodzi ndi mkazi wolongolola.*+
25 Nkhani yabwino yochokera kudziko lakutali+Ili ngati madzi ozizira kwa munthu wotopa.
26 Munthu wolungama amene amagonja* nʼkuchita zofuna za munthu woipaAmakhala ngati kasupe wamatope komanso chitsime chimene chawonongedwa.
27 Si bwino kudya uchi wambiri,+Komanso si bwino kuti munthu adzifunire yekha ulemerero.+
28 Munthu wosaugwira mtima+Ali ngati mzinda umene mpanda wake wagumulidwa.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “usaulule zinsinsi za ena.”
^ Kapena kuti, “mphekesera zoipa.”
^ Kapena kuti, “chipale chofewa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “lilime lofewa likhoza.”
^ Mabaibulo ena amati, “munthu amene amachita zachinyengo.”
^ “Viniga” ndi chakumwa chowawasira chomwe chinkapangidwa kuchokera ku vinyo wosasa kapena zakumwa zina zoledzeretsa.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “munthu amene amadana nawe.”
^ Kutanthauza kufewetsa mtima wake komanso kumuchititsa kuti azichita zinthu zabwino.
^ Kapena kuti, “wokonda kudandaula.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amanjenjemera pamaso pa munthu woipa.”