Miyambo 26:1-28

  • Zimene anthu aulesi amachita (13-16)

  • Usamalowerere mkangano wa anthu ena (17)

  • Kupewa nthabwala zopusitsa ena (18, 19)

  • Ngati palibe nkhuni moto umazima (20, 21)

  • Mawu a munthu wonenera ena zoipa ali ngati chakudya chokoma (22)

26  Sinowo sayenera kugwa mʼchilimwe ndiponso mvula siyenera kugwa pa nthawi yokolola,Chimodzimodzinso munthu wopusa, iye sayenera kulemekezedwa.+   Mbalame imakhala ndi chifukwa chothawira ndiponso namzeze amakhala ndi chifukwa choulukira.Nalonso temberero silibwera popanda chifukwa chenicheni.*   Chikwapu nʼchokwapulira hatchi, zingwe nʼzomangira pakamwa pa bulu,+Ndipo ndodo ndi yokwapulira msana wa anthu opusa.+   Usayankhe aliyense wopusa mogwirizana ndi uchitsiru wake,Kuti iweyo usafanane naye.   Ukamayankha munthu wopusa uziganizira uchitsiru wake,Kuti asaganize kuti ndi wanzeru.+   Munthu amene amasiya ntchito yake mʼmanja mwa munthu wopusaAli ngati munthu amene wapundula mapazi ake nʼkudzivulaza yekha.*   Mwambi wamʼkamwa mwa anthu opusa+Uli ngati miyendo* ya munthu wolumala amene akuyenda motsimphina.   Kupereka ulemerero kwa munthu wopusa,+Kuli ngati kumanga mwala pagulaye.*   Mwambi wamʼkamwa mwa anthu opusaUli ngati chitsamba chaminga chimene chili mʼmanja mwa munthu woledzera. 10  Wolemba ntchito munthu wopusa kapena anthu ongodutsa mʼnjira,Ali ngati woponya muvi ndi uta amene amangolasa mwachisawawa nʼkuvulaza anthu. 11  Wopusa amabwereza zochita zake zopusa+Mofanana ndi galu amene amabwerera kumasanzi ake. 12  Kodi waona munthu amene amaganiza kuti ndi wanzeru?+ Munthu wopusa ali ndi chiyembekezo chachikulu kuposa iyeyo. 13  Waulesi amanena kuti: “Mumsewu muli mkango wamphamvu,Mʼbwalo la mzinda mukuyendayenda mkango.”+ 14  Mofanana ndi chitseko chimene chimangozungulira pamene anachimangirira,Waulesi nayenso amangotembenukatembenuka pabedi pake.+ 15  Munthu waulesi amapisa dzanja lake mʼmbale ya chakudya,Koma amalephera kulibweretsa pakamwa pake chifukwa chotopa kwambiri.+ 16  Munthu waulesi amaganiza kuti ndi wanzeru kwambiriKuposa anthu 7 amene ayankha zanzeru. 17  Munthu wongodutsa amene amakwiya chifukwa cha mkangano* womwe si wake,+Ali ngati munthu wogwira makutu a galu. 18  Munthu wamisala amene akuponya mivi yoyaka moto komanso mivi yakupha, 19  Akufanana ndi munthu amene amapusitsa mnzake nʼkunena kuti, “Inetu ndimangochita zocheza.”+ 20  Ngati palibe nkhuni moto umazima,Ndipo ngati palibe munthu wonenera anzake zoipa, mikangano imatha.+ 21  Makala komanso nkhuni zimachititsa kuti moto uziyaka,Mofanana ndi zimenezi munthu wokonda kuyambana ndi anthu amakolezera mikangano.+ 22  Mawu a munthu wonenera ena zoipa ali ngati chakudya chokoma,*Akachimeza chimalowa mʼmimba.+ 23  Mawu achikondi ochokera pakamwa pa munthu wa mtima woipa,+Ali ngati siliva wokutira phale. 24  Munthu amene amadana ndi ena amabisa chidanicho ndi milomo yake,Koma mumtima mwake mumakhala chinyengo. 25  Ngakhale azilankhula mawu okoma, usamukhulupirire,Chifukwa mumtima mwake muli zinthu 7 zonyansa.* 26  Ngakhale chidani chake chitaphimbika ndi chinyengo,Zoipa zake zidzaululika mumpingo. 27  Amene akukumba dzenje adzagweramo yekha,Ndipo amene akugubuduza mwala udzabwerera kwa iye nʼkumupsinja.+ 28  Lilime lonama limadana ndi amene lamʼpweteka,Ndipo pakamwa polankhula mwachiphamaso pamabweretsa chiwonongeko.+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “Ndi mmenenso limachitira temberero lopanda chifukwa, silichitika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ali ngati munthu amene amamwa chiwawa.”
Kapena kuti, “miyendo yalendelende.”
Gulaye ndi chipangizo choponyera miyala chimene amachita kupukusa ndi dzanja.
Mabaibulo ena amati, “amene amalowerera mkangano.”
Kapena kuti, “ngati zinthu zofunika kuzimeza msangamsanga.”
Kapena kuti, “Chifukwa mtima wake ndi wonyansa kwambiri.”