Miyambo 28:1-28

  • Pemphero la munthu wosamvera ndi lonyansa (9)

  • Munthu woulula machimo ake amachitiridwa chifundo (13)

  • Amene amafuna kulemera mofulumira sadzalephera kukhala wolakwa (20)

  • Kudzudzula munthu kuli bwino kuposa kuyamikira mwachinyengo (23)

  • Munthu amene amapereka zinthu sadzasowa kanthu (27)

28  Anthu oipa amathawa popanda wowathamangitsa,Koma olungama amakhala olimba mtima ngati mkango.*+   Anthu okhala mʼdziko akamachimwa,* dzikolo limasintha akalonga pafupipafupi,+Koma kalonga akamathandizidwa ndi munthu wozindikira komanso wodziwa zinthu, amakhala nthawi yaitali.+   Munthu wosauka amene amabera mwachinyengo anthu onyozeka,+Ali ngati mvula imene imakokolola chakudya chonse.   Anthu amene asiya chilamulo amatamanda munthu woipa,Koma amene amasunga chilamulo amakwiyira anthu amene asiya chilamulowo.+   Anthu oipa sangamvetse chilungamo,Koma amene akufunafuna Yehova angathe kumvetsa chilichonse.+   Munthu wosauka amene amachita zinthu mokhulupirika,Ali bwino kuposa munthu wolemera amene amachita zachinyengo.+   Mwana womvetsa zinthu amatsatira malamulo,Koma amene amakonda kucheza ndi anthu osusuka amachititsa manyazi bambo ake.+   Munthu amene amachulukitsa chuma chake polandira chiwongoladzanja+ ndi katapira,Chuma chakecho chidzapita kwa munthu amene amakomera mtima anthu osauka.+   Munthu amene amakana kumvera chilamulo,Ngakhale pemphero lake limakhala lonyansa.+ 10  Munthu amene amasocheretsa anthu owongoka mtima kuti azichita zinthu zoipa, adzagwera mʼdzenje lake lomwe,+Koma anthu osalakwa adzalandira zinthu zabwino.+ 11  Munthu wolemera amadziona ngati wanzeru,+Koma munthu wosauka amene ndi wozindikira amamufufuza nʼkudziwa zoona zake.+ 12  Anthu olungama zinthu zikamawayendera bwino, anthu amasangalala kwambiri,*Koma anthu oipa akayamba kulamulira, anthu amabisala.+ 13  Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino,+Koma amene amawaulula nʼkuwasiya adzachitiridwa chifundo.+ 14  Wosangalala ndi munthu amene nthawi zonse amasamala zochita zake,*Koma amene amaumitsa mtima wake adzakumana ndi tsoka.+ 15  Mtsogoleri woipa amene akulamulira anthu onyozeka+Ali ngati mkango wobangula komanso chimbalangondo chimene chakonzekera kugwira nyama. 16  Mtsogoleri wosazindikira amagwiritsa ntchito mphamvu zake molakwika,+Koma amene amadana ndi kupeza phindu mwachinyengo adzatalikitsa moyo wake.+ 17  Munthu amene ali ndi mlandu wa magazi chifukwa chopha munthu, adzakhala wothawathawa mpaka kumanda.*+ Aliyense asamuthandize. 18  Amene amayenda mosalakwitsa kanthu adzapulumutsidwa,+Koma amene njira zake ndi zokhotakhota adzagwa mwadzidzidzi.+ 19  Munthu amene amalima munda wake adzakhala ndi chakudya chambiri,Koma amene akutanganidwa ndi zinthu zopanda phindu adzakhala pa umphawi waukulu.+ 20  Munthu wokhulupirika adzalandira madalitso ambiri,+Koma amene akufuna kulemera mofulumira, sadzapitiriza kukhala wosalakwa.+ 21  Si bwino kukondera.+Koma munthu akhoza kuchita zinthu zolakwika pofuna kupeza kachidutswa ka chakudya. 22  Munthu wadyera amayesetsa kuti apeze chuma,Osadziwa kuti umphawi udzamugwira. 23  Amene amadzudzula munthu,+ pambuyo pake adzakondedwa kwambiri+Kuposa munthu amene amayamikira mnzake mwachiphamaso. 24  Wobera bambo ake ndi mayi ake nʼkumanena kuti, “Si kulakwa,”+ Amakhala ngati mnzake wa munthu wobweretsa chiwonongeko.+ 25  Munthu wadyera amayambitsa mikangano,Koma aliyense amene amadalira Yehova zinthu zidzamuyendera bwino.*+ 26  Aliyense amene amadalira mtima wake ndi wopusa,+Koma amene amachita zinthu mwanzeru adzapulumuka.+ 27  Aliyense amene amapereka zinthu zake kwa anthu osauka sadzasowa kanthu,+Koma amene amatseka maso ake kuti asaone osaukawo adzalandira matemberero ambiri. 28  Munthu woipa akayamba kulamulira, munthu amabisala,Koma oipawo akatha anthu olungama amachuluka.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mkango wamphamvu.”
Kapena kuti, “akamachita zinthu zoukira.”
Kapena kuti, “pamakhala ulemerero wochuluka.”
Kapena kuti, “amene sachita mantha.”
Kapena kuti, “mʼdzenje.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzanenepa.”