Miyambo 29:1-27

  • Mwana womulekerera amachititsa manyazi (15)

  • Ngati anthu sakutsogoleredwa amachita zinthu motayirira (18)

  • Munthu wosachedwa kukwiya amayambitsa mkangano (22)

  • Munthu wodzichepetsa adzapeza ulemerero (23)

  • Kuopa anthu ndi msampha (25)

29  Munthu amene amaumitsa khosi lake* pambuyo podzudzulidwa mobwerezabwereza+Adzathyoledwa mwadzidzidzi ndipo sadzachira.+   Olungama akachuluka, anthu amasangalala,Koma munthu woipa akamalamulira, anthu amabuula.+   Munthu amene amakonda nzeru amasangalatsa bambo ake,+Koma woyenda ndi mahule amawononga chuma chake.+   Mfumu ikamachita zinthu zachilungamo dziko limalimba,+Koma munthu wokonda ziphuphu amaligwetsa.   Munthu amene amayamikira mnzake mwachiphamasoAkuyalira ukonde mapazi ake.+   Tchimo la munthu woipa limamutchera msampha,+Koma munthu wolungama amafuula mokondwera ndipo amasangalala.+   Wolungama amafunitsitsa kuti anthu osauka aziweruzidwa mwachilungamo,+Koma woipa safuna kuchita zimenezi.+   Anthu odzitama ali ngati anthu amene amayatsa tauni,+Koma anthu anzeru amaletsa mkwiyo.+   Munthu wanzeru akayamba kukangana ndi chitsiru,Pamangokhala phokoso ndi kunyozana, ndipo munthu wanzeruyo sapindula chilichonse.+ 10  Anthu okonda kukhetsa magazi amadana ndi munthu aliyense wosalakwa,+Ndipo amafuna kuchotsa moyo wa anthu owongoka mtima.* 11  Munthu wopusa amatulutsa mkwiyo wake wonse,+Koma wanzeru amakhala wodekha ndipo amalamulira mkwiyo wake.+ 12  Wolamulira akamamvera mabodza,Antchito ake onse adzakhala oipa.+ 13  Munthu wosauka komanso munthu wopondereza ena ndi ofanana* pa chinthu chimodzi ichi: Yehova amachititsa kuti maso a onsewa aziona kuwala.* 14  Mfumu ikamaweruza anthu osauka mwachilungamo,+Idzapitiriza kulamulira mpaka kalekale.+ 15  Chikwapu* komanso kudzudzula nʼzimene zimapereka nzeru,+Koma mwana womulekerera amachititsa manyazi mayi ake. 16  Oipa akachuluka, machimo amachuluka,Koma olungama adzaona oipawo akugwa.+ 17  Langa mwana wako ndipo adzakupatsa mpumuloKomanso adzakusangalatsa kwambiri.+ 18  Ngati anthu sakutsogoleredwa ndi Mulungu, amachita zinthu motayirira,+Koma osangalala ndi amene amatsatira chilamulo.+ 19  Wantchito safuna kusintha ndi mawu okha,Chifukwa ngakhale atamvetsa mawuwo, safuna kuwatsatira.+ 20  Kodi waona munthu amene amafulumira kulankhula asanaganize?+ Munthu wopusa ali ndi chiyembekezo chachikulu kuposa munthu ameneyu.+ 21  Ngati munthu akusasatitsa kapolo wake kuyambira ali mwana,Mʼtsogolo adzakhala wosayamika. 22  Munthu wosachedwa kukwiya amayambitsa mkangano.+Aliyense amene sachedwa kupsa mtima amakhala ndi machimo ambiri.+ 23  Kudzikuza kwa munthu kudzamutsitsa,+Koma amene ali ndi mtima wodzichepetsa adzapeza ulemerero.+ 24  Amene amathandiza munthu wakuba amadzibweretsera mavuto. Iye angamve kuitana kuti akapereke umboni,* koma osakanena chilichonse.+ 25  Kuopa anthu ndi msampha,*+Koma amene amakhulupirira Yehova adzatetezedwa.+ 26  Anthu ambiri amafunitsitsa kuonana ndi wolamulira,*Koma kwa Yehova nʼkumene munthu amapeza chilungamo.+ 27  Munthu wopanda chilungamo ndi wonyansa kwa anthu olungama,+Koma munthu amene amachita zabwino ndi wonyansa kwa munthu woipa.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “amene safuna kusintha.”
Mabaibulo ena amati, “Koma anthu owongoka mtima amasamalira moyo wa anthu opanda cholakwawo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amakumana pamodzi.”
Kutanthauza kuti amawapatsa moyo.
Kapena kuti, “Chilango.”
Kapena kuti, “lumbiro limene linalinso ndi mawu otemberera.”
Kapena kuti, “kumatchera msampha.”
Mabaibulo ena amati, “amafunitsitsa kuti wolamulira awakomere mtima.”