Miyambo 3:1-35

  • Kukhala wanzeru komanso kudalira Yehova (1-12)

    • Kulemekeza Yehova pogwiritsa ntchito zinthu zamtengo wapatali (9)

  • Nzeru zimathandiza munthu kuti azisangalala (13-18)

  • Nzeru zimateteza (19-26)

  • Kuchitira ena zinthu zabwino (27-35)

    • Kuthandiza ena ngati tingathe (27)

3  Mwana wanga, usaiwale zimene ndimakuphunzitsa,*Ndipo mtima wako uzisunga malamulo anga.   Ukamachita zimenezi, udzakhala ndi masiku ochulukaKomanso moyo wazaka zambiri ndi mtendere.+   Usalole kuti chikondi chokhulupirika komanso kukhulupirika* zichoke mwa iwe.+ Uzimange mʼkhosi mwakoNdi kuzilemba pamtima pako.+   Ukachita zimenezi, Mulungu ndi anthu+Adzakukomera mtima ndipo adzakuona kuti ndiwe wozindikira.   Uzikhulupirira Yehova+ ndi mtima wako wonse,Ndipo usamadalire* luso lako lomvetsa zinthu.+   Uzimukumbukira mʼnjira zako zonse,+Ndipo iye adzawongola njira zako.+   Usamadzione kuti ndiwe wanzeru.+ Uziopa Yehova ndi kupatuka pa choipa.   Zimenezi zidzachiritsa thupi lako*Ndi kutsitsimutsa mafupa ako.   Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali+Ndiponso ndi zipatso zako zonse zoyambirira.*+ 10  Ukatero nyumba zako zosungiramo zinthu zidzadzaza kwambiri,+Ndipo zoponderamo mphesa zako zidzasefukira ndi vinyo watsopano. 11  Mwana wanga, usakane malangizo* a Yehova+Ndipo usanyansidwe ndi kudzudzula kwake,+ 12  Chifukwa Yehova amadzudzula munthu amene amamukonda,+Ngati mmene bambo amadzudzulira mwana amene amasangalala naye.+ 13  Wosangalala ndi munthu amene amapeza nzeru,+Ndiponso munthu amene amaphunzira zinthu zimene zingamuthandize kukhala wozindikira. 14  Chifukwa kupeza nzeru nʼkwabwino kuposa kupeza siliva,Ndipo kukhala nazo monga phindu nʼkwabwino kuposa kukhala ndi golide.+ 15  Nʼzamtengo wapatali kuposa miyala ya korali,*Palibe chimene umalakalaka chimene chingafanane nazo. 16  Mʼdzanja lake lamanja muli moyo wautali.Mʼdzanja lake lamanzere muli chuma ndi ulemerero. 17  Kuyenda mʼnjira zake kumasangalatsa,Ndipo kuyenda mʼmisewu yake kumabweretsa mtendere.+ 18  Munthu akagwiritsitsa nzeru, zidzakhala ngati mtengo wa moyo kwa iye,Ndipo anthu amene amazigwiritsitsa adzatchedwa osangalala.+ 19  Yehova anayala maziko a dziko lapansi mwanzeru.+ Anakhazikitsa kumwamba mozindikira.+ 20  Chifukwa chakuti iye amadziwa zinthu, anagawa madzi akuyaNdipo kumwamba kwa mitambo kunagwetsa mame.+ 21  Mwana wanga, zimenezi* zisachoke pamaso pako. Uteteze nzeru zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino. 22  Zidzakupatsa moyoKomanso zidzakhala zokongoletsera mʼkhosi mwako. 23  Ukatero udzayenda panjira yako popanda chokuopseza,Ndipo phazi lako silidzapunthwa.*+ 24  Ukagona sudzaopa chilichonse.+Udzagona ndithu, ndipo tulo tako tidzakhala tokoma.+ 25  Sudzaopa zoopsa zilizonse zadzidzidzi,+Kapena mphepo yamkuntho imene ikubwera pa oipa.+ 26  Chifukwa uzidzadalira kwambiri Yehova,+Ndipo adzateteza phazi lako kuti lisakodwe.+ 27  Usalephere kuchitira zabwino anthu amene ukuyenera kuwachitira* zabwinozo,+Ngati ungathe kuwathandiza.*+ 28  Mnzako usamuuze kuti, “Pita, ukabwerenso mawa ndipo ndidzakupatsa,” Ngati ungathe kumupatsa nthawi yomweyo. 29  Usakonze zochitira mnzako zoipa+Pamene iye akuona kuti akukhala nawe mwamtendere. 30  Usakangane ndi munthu popanda chifukwa+Ngati sanakuchitire choipa chilichonse.+ 31  Usasirire munthu wachiwawa+Kapena kusankha kuyenda mʼnjira yake iliyonse, 32  Chifukwa Yehova amanyansidwa ndi munthu wachiphamaso,+Koma anthu owongoka mtima amakhala nawo pa ubwenzi wolimba.+ 33  Yehova amatemberera banja la munthu woipa,+Koma iye amadalitsa nyumba ya munthu wolungama.+ 34  Onyoza, iye amawanyoza,+Koma ofatsa amawakomera mtima.+ 35  Anzeru adzalandira ulemu,Koma opusa amalemekeza zinthu zimene zidzawachititse manyazi.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “usaiwale malamulo anga.”
Kapena kuti, “choonadi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “usatsamire.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mchombo wako.”
Kapena kuti, “Ndiponso ndi zinthu zabwino kwambiri pa zokolola zako.”
Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.
Zikuoneka kuti akutanthauza makhalidwe a Mulungu amene atchulidwa mʼmavesi amʼmbuyomu.
Kapena kuti, “silidzawomba chilichonse.”
Kapena kuti, “Ngati dzanja lako lingathe kuchita zimenezo.”
Kapena kuti, “amene akufunikira.”