Miyambo 30:1-33
30 Uwu ndi uthenga wamphamvu womwe Aguri mwana wa Yake analankhula ndi Itiyeli komanso Ukali.
2 Ine sindidziwa zambiri poyerekeza ndi anthu ena onse,+Ndipo sinditha kumvetsa zinthu ngati mmene anthu ena amachitira.
3 Ine sindinaphunzire zinthu zanzeru,Ndipo sindidziwa zinthu zimene Woyera Koposa amadziwa.
4 Ndi ndani amene anakwerapo kumwamba kenako nʼkutsika?+
Ndi ndani amene anasonkhanitsapo mphepo mʼmanja mwake?
Ndi ndani amene anamangapo madzi pachovala chake?+
Ndi ndani amene anaika malire a dziko lapansi?+
Dzina lake ndi ndani, nanga mwana wake dzina lake ndi ndani? Ndiuzeni ngati mukudziwa.
5 Mawu onse a Mulungu ndi oyengeka.+
Iye ndi chishango kwa onse amene amathawira kwa iye.+
6 Usawonjezere kanthu pa mawu ake+Kuti angakudzudzule,Nʼkuoneka kuti ndiwe wabodza.
7 Ndikukupemphani zinthu ziwiri.
Mundipatse zinthu zimenezi ndisanafe.
8 Zinthu zabodza komanso mawu onama muziike kutali ndi ine.+
Musandipatse umphawi kapena chuma.
Mungondipatsa chakudya chokwanira,+
9 Kuti ndisakhute kwambiri nʼkukukanani kuti: “Kodi Yehova ndi ndani?”+
Ndiponso kuti ndisasauke nʼkukaba ndi kuchititsa kuti dzina la Mulungu wanga linyozedwe.
10 Usanenere wantchito zoipa kwa bwana wake,Kuti angakutemberere ndipo ungapezeke wolakwa.+
11 Pali mʼbadwo umene umatemberera bambo awoKomanso umene sudalitsa mayi awo.+
12 Pali mʼbadwo umene umadziona kuti ndi woyera+Koma sunayeretsedwe ku zonyansa zake.*
13 Pali mʼbadwo umene maso ake ndi onyadaNdiponso umene maso ake amayangʼana modzikweza.+
14 Pali mʼbadwo umene mano ake ndi malupangaNdiponso umene nsagwada zake ndi mipeni yophera nyama.Mʼbadwowo umapondereza anthu ovutika apadziko lapansiKomanso osauka pakati pa anthu.+
15 Misundu* ili ndi ana aakazi awiri amene amafuula kuti, “Tipatseni! Tipatseni!”
Pali zinthu zitatu zimene sizikhutaNdiponso zinthu 4 zimene sizinena kuti, “Ndakhuta!” Zinthu zake ndi izi:
16 Manda,*+ mimba yosabereka,Nthaka yopanda madziKomanso moto umene sunena kuti, “Ndakhuta!”
17 Munthu amene amanyoza bambo ake ndiponso amene samvera mayi ake,+Akhwangwala akuchigwa* adzakolowola diso lakeNdipo ana a chiwombankhanga adzalidya.+
18 Pali zinthu zitatu zimene nʼzodabwitsa kwambiri kwa ine,Ndiponso zinthu 4 zimene sindizimvetsa. Zinthu zake ndi izi:
19 Njira ya chiwombankhanga mumlengalenga,Njira ya njoka pamwala,Njira ya sitima pakatikati pa nyanja,Ndiponso njira ya mwamuna ndi mtsikana.
20 Zimene mkazi wachigololo amachita ndi izi:
Iye amadya nʼkupukuta pakamwa pakeKenako amanena kuti, “Sindinachite cholakwa chilichonse.”+
21 Pali zinthu zitatu zimene zimagwedeza dziko lapansiNdiponso zinthu 4 zimene dziko lapansi silitha kuzipirira. Zinthu zake ndi izi:
22 Kapolo akamalamulira monga mfumu,+Munthu wopusa akamadya kwambiri,
23 Mkazi amene amadedwa* akakwatiwa,Komanso mtsikana wantchito akatenga malo a abwana ake aakazi.+
24 Pali zinthu 4 zomwe zili mʼgulu la zinthu zingʼonozingʼono kwambiri padziko lapansiKoma ndi zanzeru mwachibadwa.* Zinthu zake ndi izi:+
25 Nyerere si zamphamvu,Koma zimasonkhanitsa chakudya chawo mʼchilimwe.+
26 Mbira+ si nyama zamphamvuKoma zimamanga nyumba zawo pathanthwe.+
27 Dzombe+ lilibe mfumuKoma limauluka lonse litagawikana mʼmagulumagulu.+
28 Nalimata+ amagwira zinthu ndi mapazi akeNdipo amalowa mʼnyumba yachifumu.
29 Pali zinthu zitatu zimene zimayenda mochititsa chidwiNdiponso zinthu 4 zimene zimasangalatsa zikamayenda. Zinthu zake ndi izi:
30 Mkango umene ndi wamphamvu kwambiri panyama zonse zakutchireNdiponso umene suopa chilichonse nʼkubwerera mʼmbuyo,+
31 Galu wosaka kapena mbuzi yamphongo,Ndiponso mfumu imene ili limodzi ndi asilikali ake.
32 Ngati wachita zinthu zopusa nʼkudzikweza,+Kapena ngati ukufuna kuchita zimenezo,Gwira pakamwa pako.+
33 Chifukwa mkaka ukaukhutchumula umatulutsa mafuta,Mphuno ukaifinya imatulutsa magazi,Ndipo kukolezera mkwiyo kumayambitsa mkangano.+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ku ndowe zake.”
^ “Msundu” ndi mtundu wa nyongolotsi zimene zimakhala mʼmadzi ndipo zimaluma anthu kapena zinyama nʼkumayamwa magazi.
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “akukhwawa.”
^ Kapena kuti, “sakondedwa.”
^ Kapena kuti, “ndi zanzeru kwambiri.”