Miyambo 31:1-31
31 Mawu a Mfumu Lemueli, uwu ndi uthenga wamphamvu umene mayi ake anamupatsa pomulangiza:+
2 Kodi ndikuuze chiyani mwana wanga?Kodi ndikuuze mawu otani iwe mwana wochokera mʼmimba mwanga?Kodi ndikuuze mawu otani iwe mwana wa malonjezo anga?+
3 Usamapereke mphamvu zako kwa akazi,+Kapena kutsatira njira zimene zimachititsa kuti mafumu awonongedwe.+
4 Nʼkosayenera kuti mafumu azimwa vinyo,Nʼkosayenera kuti mafumu azichita zimenezi, iwe Lemueli,Kapena kuti olamulira azinena kuti: “Kodi chakumwa changa chili kuti?”+
5 Chifukwa angamwe nʼkuiwala malamuloNdiponso kupondereza ufulu wa anthu onyozeka.
6 Pereka mowa kwa anthu amene akuwonongedwa+Komanso vinyo kwa anthu amene ali ndi nkhawa.*+
7 Asiyeni amwe kuti aiwale umphawi wawo,Ndipo asakumbukirenso mavuto awo.
8 Lankhula poteteza anthu amene sangathe kudziteteza okha.Teteza ufulu wa anthu onse amene akuwonongedwa.+
9 Lankhula ndipo uweruze mwachilungamo.Teteza ufulu wa anthu onyozeka komanso osauka.*+
א [Aleph]
10 Kodi ndi ndani amene angapeze mkazi wamakhalidwe abwino?*+
Ndi wamtengo wapatali kuposa miyala ya korali.*
ב [Beth]
11 Mwamuna wake amamudalira ndi mtima wonse,Ndipo mwamunayo amapeza chilichonse chimene akufunikira.
ג [Gimel]
12 Masiku onse a moyo wake,Mkaziyo amachitira mwamuna wakeyo zinthu zabwino osati zoipa.
ד [Daleth]
13 Amatenga ulusi ndi nsalu,Ndipo amasangalala kugwira ntchito ndi manja ake.+
ה [He]
14 Iye ali ngati sitima zapamadzi za munthu wamalonda,+Amabweretsa chakudya chake kuchokera kutali.
ו [Waw]
15 Amadzukanso kudakali usiku,Nʼkupereka chakudya kwa banja lakeNdipo atsikana ake antchito amawapatsa gawo lawo.+
ז [Zayin]
16 Amaganizira zogula munda ndipo amauguladi.Amalima munda wa mpesa chifukwa cha khama lake.*
ח [Heth]
17 Amakonzekera kugwira ntchito yovuta,*+Ndipo amalimbitsa manja ake.
ט [Teth]
18 Amaonetsetsa kuti akupeza phindu pa malonda ake.Nyale yake simazima usiku.
י [Yod]
19 Manja ake amagwira ndodo yokulungako ulusi,Ndipo zala zake zimagwira ndodo yopotera chingwe.+
כ [Kaph]
20 Amatambasula dzanja lake nʼkuthandiza munthu wonyozeka,Ndipo amatambasula manja ake kuti athandize wosauka.+
ל [Lamed]
21 Kukamazizira, iye sadera nkhawa za banja lakeChifukwa anthu onse a mʼbanja lake amavala zovala zotentha.*
מ [Mem]
22 Iye amapanga yekha zoyala pabedi.
Zovala zake zimakhala za nsalu zabwino ndiponso za ubweya wa nkhosa wapepo.
נ [Nun]
23 Mwamuna wake amadziwika bwino pamageti a mzinda,+Pamene amakhala pamodzi ndi akulu amʼdzikolo.
ס [Samekh]
24 Iye amapanga zovala* nʼkuzigulitsa,Ndipo amapanga malamba nʼkuwapereka kwa amalonda.
ע [Ayin]
25 Iye amavala mphamvu ndi ulemerero ngati chovala,Ndipo sada nkhawa akamaganizira zamʼtsogolo.
פ [Pe]
26 Amatsegula pakamwa pake mwanzeru,+Ndipo lamulo la kukoma mtima lili* palilime lake.
צ [Tsade]
27 Iye amayangʼanira ntchito zapabanja pake,Ndipo sadya chakudya cha ulesi.+
ק [Qoph]
28 Ana ake amaimirira nʼkumutchula kuti ndi wosangalala.Mwamuna wake amaimirira nʼkumutamanda kuti:
ר [Resh]
29 “Pali akazi ambiri amakhalidwe abwino,*Koma iweyo umaposa onsewo.”
ש [Shin]
30 Munthu akhoza kuoneka ngati wabwino koma zisali choncho ndipo kukongola sikungachedwe kutha,*+Koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.+
ת [Taw]
31 Mʼpatseni mphoto chifukwa cha zimene amachita,*+Ndipo ntchito zake zimutamande mʼmageti a mzinda.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “amene mtima wawo ukuwawa.”
^ Kapena kuti, “Teteza anthu onyozeka komanso osauka pa mlandu wawo.”
^ Kapena kuti, “wabwino kwambiri.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “pogwiritsa ntchito ndalama zimene wapeza.” Mʼchilankhulo choyambirira, “pogwiritsa ntchito zipatso za manja ake.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Amamangirira mphamvu mchiuno mwake.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “zovala ziwiri.”
^ Kapena kuti, “zovala zamkati.”
^ Kapena kuti, “Malangizo achikondi ali; Lamulo la chikondi chokhulupirika lili.”
^ Kapena kuti, “abwino kwambiri.”
^ Kapena kuti, “kukhoza kukhala kopanda phindu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mupatseni kuchokera pa zipatso za manja ake.”