Miyambo 5:1-23
5 Mwana wanga, tchera makutu ako ku mawu anga anzeru.
Mvetsera mosamala zimene ndikukuphunzitsa zokhudza kukhala wozindikira,+
2 Kuti uteteze luso lako loganiza bwino,Ndiponso kuti milomo yako iteteze kudziwa zinthu.+
3 Chifukwa milomo ya mkazi wamakhalidwe oipa* imakha uchi ngati chisa cha njuchi,+Ndipo mʼkamwa mwake ndi mosalala kuposa mafuta.+
4 Koma pamapeto pake amawawa kwambiri ngati chitsamba chowawa.+Ndipo amakhala wakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.+
5 Mapazi ake amatsikira ku imfa.
Miyendo yake imalowera ku Manda.*
6 Iye saganizira zimene zingamuthandize kukapeza moyo.
Amangoyendayenda, osadziwa kumene akulowera.
7 Tsopano mwana wanga,* ndimvere,Ndipo usapatuke pa zimene ndikukuuza.
8 Ukhale kutali kwambiri ndi iye.Usayandikire pakhomo la nyumba yake,+
9 Kuti usapereke ulemu wako kwa anthu ena+Komanso kuti usakumane ndi mavuto mʼzaka zotsala za moyo wako.*+
10 Ndiponso kuti alendo asakuwonongere zinthu zako,*+Komanso kuti zinthu zimene unazipeza movutikira zisapite kunyumba ya mlendo.
11 Ukapanda kumvera, udzabuula kumapeto kwa moyo wako,Mphamvu zako zikadzatha komanso ukadzawonda kwambiri.+
12 Ndipo udzanena kuti: “Ndinkadana ndi malangizo* ine!
Ndipo mtima wanga sunkamvera, ena akandidzudzula.
13 Sindinamvere mawu a alangizi anga,Kapena kutchera khutu kwa aphunzitsi anga.
14 Ndangotsala pangʼono kutheratuPakati pa mpingo wonse.”*+
15 Imwa madzi ochokera mʼchitsime chako,Komanso madzi oyenderera kuchokera pakasupe wako.+
16 Kodi akasupe ako amwazike panja?Ndipo kodi mitsinje yako ya madzi imwazike mʼmabwalo amumzinda?+
17 Zimenezi zikhale zako zokhaosati uzigawana ndi anthu achilendo.+
18 Kasupe wako akhale wodalitsidwa,*Ndipo uzisangalala ndi mkazi amene unamukwatira udakali wachinyamata.+
19 Iye akhale ngati mbawala yaikazi yachikondi komanso ngati kamwana ka mbuzi zamʼmapiri kokongola.+
Mabere ake azikukhutiritsa* nthawi zonse.
Chikondi chake chizikusangalatsa kwambiri nthawi zonse.+
20 Ndiye mwana wanga, kodi pali chifukwa chilichonse choti uzisangalalira ndi mkazi wamakhalidwe oipa,*Kapena choti uzikumbatirira chifuwa cha mkazi wachiwerewere?*+
21 Chifukwa maso a Yehova amaona chilichonse chimene munthu akuchita,Ndipo iye amafufuza njira zake zonse.+
22 Woipa amakodwa ndi zolakwa zake zomwe,Ndipo adzamangidwa ndi zingwe za tchimo lake lomwe.+
23 Iye adzafa chifukwa chosamvera malangizo,Ndipo adzasochera chifukwa cha kuchuluka kwa uchitsiru wake.
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ana anga.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “kuti usapereke zaka zako ku zinthu zankhanza.”
^ Kapena kuti, “mphamvu zako.”
^ Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Pakati pa msonkhano komanso mpingo.”
^ Kapena kuti, “Pamene umatunga madzi ako pakhale podalitsidwa.”
^ Kapena kuti, “azikusangalatsa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.”