Miyambo 7:1-27

  • Mverani malamulo a Mulungu kuti mukhale ndi moyo (1-5)

  • Mnyamata wosadziwa zinthu anakopedwa (6-27)

    • “Ngati ngʼombe yamphongo imene ikupita kukaphedwa” (22)

7  Mwana wanga, usunge mawu angaNdipo uziona kuti malamulo anga ndi amtengo wapatali.+   Usunge malamulo anga kuti upitirize kukhala ndi moyo.+Uteteze malangizo* anga ngati mwana wa diso lako.   Uwamange kuzala zako,Ndipo uwalembe pamtima pako.+   Nzeru uiuze kuti: “Ndiwe mchemwali wanga,” Ndipo kumvetsa zinthu ukutche “mʼbale wanga,”   Kuti zikuteteze kwa mkazi wamakhalidwe oipa,*+Ndiponso kwa mkazi wachiwerewere* wolankhula mawu okopa.+   Ndinayangʼana pansiKuchokera pawindo la nyumba yanga,   Ndipo pamene ndinkayangʼanitsitsa anthu osadziwa zinthu,Ndinazindikira kuti pakati pa achinyamata pali mnyamata wina wopanda nzeru.*+   Iye ankadutsa mumsewu pafupi ndi mphambano,Ndipo ankalowera kunyumba ya mkaziyo   Pa nthawi yamadzulo kuli kachisisira,+Kutatsala pangʼono kuda. 10  Kenako ndinaona mkazi akubwera kudzakumana naye,Atavala ngati hule+ ndipo anali ndi mtima wachinyengo. 11  Ndi wolongolola ndiponso wamakani.+ Ndipo sakhala pakhomo.* 12  Pasanapite nthawi amapezeka kuti ali panja, kenako amapezeka mʼmabwalo a mzinda,Amadikirira anthu pafupi ndi mphambano iliyonse.+ 13  Iye wagwira mnyamatayo nʼkumupatsa kisi.Mʼmaso muli gwaa! akumuuza kuti: 14  “Ndinayenera kupereka nsembe zamgwirizano.+ Lero ndakwaniritsa zimene ndinalonjeza. 15  Nʼchifukwa chake ndabwera kudzakumana nawe,Kudzakufunafuna ndipo ndakupeza. 16  Ndayala zofunda zabwino pabedi panga,Nsalu za ku Iguputo zokongola kwambiri.*+ 17  Ndawaza pabedi panga zonunkhiritsa za mule, aloye ndi sinamoni.+ 18  Bwera tisonyezane chikondi mpaka mʼmawa ndipo chitikwane.Tiye tisangalatsane pochita zachikondi, 19  Chifukwa mwamuna wanga sali panyumba.Iye wachoka, wapita kutali. 20  Wanyamula chikwama cha ndalama,Ndipo adzabwera kunyumba tsiku limene mwezi udzaoneke wathunthu.” 21  Wasocheretsa mnyamatayo pochita zinthu zambiri zomukopa.+ Wamunyengerera ndi mawu okopa. 22  Mwadzidzidzi mnyamatayo akuyamba kulondola mkaziyo, ngati ngʼombe yamphongo imene ikupita kukaphedwa,Ndiponso ngati munthu wopusa amene akuyenera kulangidwa pomuika mʼmatangadza.+ 23  Iye akulondola mkaziyo mpaka muvi utaboola chiwindi chake,Ngati mbalame imene ikuthamangira kumsampha ndipo sakudziwa kuti zichititsa kuti ataye moyo wake.+ 24  Choncho ana anga, ndimvereni.Mvetserani mawu amene ndikukuuzani. 25  Musalole kuti mtima wanu upatukire kunjira zake. Musasochere nʼkuyamba kuyenda mʼnjira zake,+ 26  Chifukwa mkaziyo waphetsa anthu ambiri,+Ndipo amene aphedwa ndi iyeyo ndi osawerengeka.+ 27  Nyumba yake ndi njira yopita ku Manda.*Imatsikira kuzipinda za imfa.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “malamulo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.”
Kapena kuti, “mnyamata wina amene ali ndi zolinga zoipa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo mapazi ake sakhala pakhomo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “zamitundu yosiyanasiyana.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.