Mlaliki 11:1-10

  • Uzigwiritsa ntchito mwayi umene uli nawo mwanzeru (1-8)

    • Ponya mkate wako pamadzi (1)

    • Dzala mbewu zako mʼmawa mpaka madzulo (6)

  • Sangalala moyenera ndi unyamata wako (9, 10)

11  Ponya* mkate wako pamadzi+ chifukwa pakapita masiku ambiri udzaupezanso.+  Pereka gawo la zinthu zimene uli nazo kwa anthu 7 kapena 8+ chifukwa sukudziwa tsoka limene lidzagwe padziko lapansi.  Mitambo ikadzaza madzi, imakhuthulira mvula yochuluka padziko lapansi, ndipo mtengo ukagwera kumʼmwera kapena kumpoto, pamene wagwerapo udzakhala pomwepo.  Munthu amene amayangʼana mphepo sadzadzala mbewu ndipo amene amayangʼana mitambo sadzakolola.+  Iwe sudziwa mmene mzimu umachititsira kuti mafupa a mwana amene ali mʼmimba mwa mayi ake akule.+ Mofanana ndi zimenezi sudziwanso ntchito ya Mulungu woona, amene amachita zinthu zonse.+  Dzala mbewu zako mʼmawa ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo,+ chifukwa sukudziwa zimene zidzachite bwino, kaya izi kapena zinazo, kapenanso ngati zonse zidzachite bwino.  Kuwala nʼkokoma ndipo ndi bwino kuti maso aone dzuwa.  Ngati munthu atakhala ndi moyo zaka zambiri, azisangalala pa zaka zonsezo.+ Koma azikumbukira kuti masiku a mdima akhoza kukhala ambiri. Zonse zimene zikubwera nʼzachabechabe.+  Mnyamata iwe, sangalala pa nthawi imene uli wachinyamata, ndipo mtima wako usangalale masiku a unyamata wako. Uzichita zimene mtima wako ukufuna ndipo uzipita kumene maso ako akukutsogolera. Koma dziwa kuti Mulungu woona adzakuweruza* pa zinthu zonsezi.+ 10  Choncho chotsa zinthu zobweretsa mavuto mumtima mwako ndipo teteza thupi lako ku zinthu zimene zingakuvulaze, chifukwa unyamata ndiponso pachimake pa moyo nʼzachabechabe.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Tumiza.”
Kapena kuti, “adzakuimba mlandu.”