Mlaliki 12:1-14

  • Uzikumbukira Mlengi usanakalambe (1-8)

  • Mawu omaliza a wosonkhanitsa anthu (9-14)

    • Mawu a anthu anzeru ali ngati zisonga zobayira ngʼombe (11)

    • Opa Mulungu woona (13)

12  Choncho kumbukira Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako,+ asanafike masiku oipa*+ komanso zisanafike zaka zimene udzanena kuti: “Moyo sukundisangalatsa.”  Uchite zimenezi kuwala kwa dzuwa, mwezi ndi nyenyezi kusanazime+ ndiponso mitambo yamvula isanabwererenso pambuyo poti mvula yagwa.  Pa nthawi imeneyo olondera* nyumba adzayamba kunjenjemera, amuna amphamvu adzapindika, akazi adzasiya kupera ufa chifukwa adzatsala ochepa ndipo akazi oyangʼana pawindo azidzaona mdima.+  Zitseko zotulukira popita mumsewu zidzatsekedwa, phokoso la miyala yoperera ufa lidzayamba kumveka motsika ndipo munthu azidzadzuka ndi kulira kwa mbalame, ndiponso ana onse aakazi azidzaimba nyimbo ndi mawu ofooka.+  Komanso munthu azidzaopa malo okwera ndipo azidzadera nkhawa zinthu zoopsa mumsewu. Mtengo wa amondi udzachita maluwa,+ chiwala chizidzayenda mochita kudzikoka ndipo zakudya sizidzakoma,* chifukwa munthu adzakhala akupita kunyumba yake yokhalitsa+ ndipo olira azidzangoyendayenda mumsewu.+  Uzikumbukira Mlengi wako chingwe chasiliva chisanachotsedwe, mbale yagolide isanaphwanyidwe, mtsuko umene uli pakasupe usanaphwanyike ndiponso wilo lotungira madzi pachitsime lisanathyoke.  Kenako fumbi lidzabwerera kunthaka+ kumene linali, ndipo mzimu* udzabwerera kwa Mulungu woona amene anaupereka.+  Wosonkhanitsa anthu akunena kuti:+ “Nʼzachabechabe!* Zinthu zonse nʼzachabechabe.”+  Kuwonjezera pa kukhala ndi nzeru, wosonkhanitsa anthuyu nthawi zonse ankaphunzitsa anthuwo zimene iye ankadziwa+ ndipo anaganizira mozama komanso anafufuza zinthu mosamala kuti alembe* miyambi yambiri.+ 10  Wosonkhanitsa anthuyu anafufuza mawu osangalatsa+ ndipo analemba mawu olondola a choonadi. 11  Mawu a anthu anzeru ali ngati zisonga zobayira ngʼombe pozitsogolera,+ ndipo mawu awo osankhidwa bwino ali ngati misomali imene aikhomerera kwambiri. Mawuwo aperekedwa ndi mʼbusa mmodzi. 12  Mwana wanga, ponena za zinthu zina kupatula izi, ndikukuchenjeza kuti: Anthu adzapitirizabe kulemba mabuku ambiri ndipo kuwawerenga kwambiri kumangotopetsa munthu.+ 13  Poti zonse zanenedwa, mfundo yaikulu ndi yakuti: Opa Mulungu woona+ ndi kusunga malamulo ake+ chifukwa zimenezi ndi zimene munthu akuyenera kuchita.+ 14  Chifukwa Mulungu woona adzaweruza chilichonse chimene anthu amachita kuphatikizapo chinthu chilichonse chobisika, kuti aone ngati chili chabwino kapena choipa.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “masiku atsoka.”
Kapena kuti, “oyangʼanira.”
Mawu a mʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “zakudya sizidzakoma,” akutanthauza kuti chipatso cha mtundu winawake chimene munthu amadya kuti zakudya ziyambirenso kumukomera, chaphulika.
Kapena kuti, “mphamvu ya moyo.”
Kapena kuti, “Nʼzopanda pake.”
Kapena kuti, “kuti aike mwandondomeko.”