Mlaliki 4:1-16

  • Kuponderezedwa nʼkoipa kuposa imfa (1-3)

  • Kuona ntchito moyenera (4-6)

  • Ubwino wokhala ndi mnzako (7-12)

    • Awiri amaposa mmodzi (9)

  • Moyo wa wolamulira ungathe kukhala wachabechabe (13-16)

4  Ine ndinaganiziranso zinthu zonse zimene anthu amachita akamapondereza anzawo padziko lapansi pano. Ndinaona anthu oponderezedwa akugwetsa misozi, koma panalibe aliyense woti awatonthoze.+ Anthu oponderezawo anali ndi mphamvu, moti panalibe aliyense woti atonthoze anthu oponderezedwawo.  Ndinazindikira kuti anthu amene anafa kale ali bwino kuposa anthu amene ali ndi moyo.+  Koma amene ali bwino kwambiri kuposa onsewa ndi amene sanabadwe,+ amene sanaone zinthu zoipa zimene zikuchitika padziko lapansi pano.+  Ndaona kuti anthu akamagwira ntchito mopikisana, amaigwira mwakhama ndiponso mwaluso kwambiri.+ Izinso nʼzachabechabe ndipo zili ngati kuthamangitsa mphepo.  Wopusa amapinda manja ake osagwira ntchito ndipo amadzibweretsera mavuto.*+  Ndi bwino kupuma pangʼono* kusiyana nʼkugwira ntchito mwakhama* ndi kuthamangitsa mphepo.+  Ndinaganiziranso zinthu zina zachabechabe zimene zimachitika padziko lapansi pano:  Pali munthu amene ali yekhayekha, wopanda mnzake. Alibe mwana kapena mchimwene wake, koma amangokhalira kugwira ntchito mwakhama. Maso ake sakhutira ndi chuma.+ Koma kodi amadzifunsa kuti, “Ndikamagwira ntchito mwakhama komanso kudzimana zinthu zabwino, kodi ndikufuna kuti zinthu zimenezi adzasangalale nazo ndani?”+ Izinso nʼzachabechabe ndipo ndi ntchito yobweretsa nkhawa.+  Awiri amaposa mmodzi+ chifukwa amapeza mphoto yabwino* pa ntchito yawo imene amaigwira mwakhama. 10  Chifukwa ngati mmodzi wa iwo atagwa, winayo akhoza kuthandiza mnzakeyo kuti adzuke. Koma kodi chingachitike nʼchiyani kwa munthu amene wagwa koma palibe woti amuthandize kuti adzuke? 11  Komanso anthu awiri akagona pamodzi amamva kutentha. Koma kodi mmodzi yekha angamve bwanji kutentha? 12  Munthu akhoza kugonjetsa munthu mmodzi koma anthu awiri akhoza kulimbana naye. Ndipo chingwe chopotedwa ndi zingwe zitatu sichingaduke msanga.* 13  Mwana wosauka koma wanzeru ali bwino kuposa mfumu yokalamba koma yopusa,+ imene sionanso kufunika komvera chenjezo.+ 14  Chifukwa mwanayo amatuluka mʼndende nʼkukhala mfumu+ ngakhale kuti anabadwa ali wosauka mu ufumuwo.+ 15  Ndinaganizira za anthu onse amoyo amene amayenda padziko lapansi pano komanso za mmene zimakhalira ndi wachinyamata amene amalowa mʼmalo mwa mfumu. 16  Ngakhale kuti anthu amene ali kumbali yake ndi ambiri, anthu obwera pambuyo pake sadzasangalala naye.+ Izinso nʼzachabechabe ndipo zili ngati kuthamangitsa mphepo.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo amadya mnofu wake womwe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kupuma kodzaza dzanja limodzi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ntchito yovuta yodzaza manja awiri.”
Kapena kuti, “phindu lalikulu.”
Kapena kuti, “mosavuta.”