Mlaliki 6:1-12

  • Kukhala ndi zinthu koma osasangalala (1-6)

  • Muzisangalala ndi zinthu zimene muli nazo panopa (7-12)

6  Pali chinthu chinanso chomvetsa chisoni chimene* ndaona padziko lapansi pano ndipo nʼchofala pakati pa anthu:  Mulungu woona amapatsa munthu chuma, katundu ndi ulemerero moti sasowa chilichonse chimene amalakalaka. Komabe Mulungu woona samulola kuti asangalale ndi zinthu zimenezi ngakhale kuti munthu wina angathe kusangalala nazo. Zimenezi nʼzachabechabe komanso tsoka lalikulu.  Ngati munthu atabereka ana 100 nʼkukhala ndi moyo zaka zambirimbiri mpaka kukalamba, koma osasangalala ndi zinthu zabwino zimene ali nazo asanalowe mʼmanda, ndithu mwana amene anabadwa wakufa ali bwino kuposa iyeyu.+  Chifukwa kubadwa kwa mwanayu kunali kopanda phindu. Zinali ngati kuti wafera mumdima ndipo alibe dzina.  Ngakhale kuti mwanayu sanaone dzuwa kapena kudziwa chilichonse, ali bwinobe* kuposa munthu woyamba uja.+  Kodi pali phindu lanji ngati munthu atakhala ndi moyo zaka 1,000 kapena 2,000 koma osasangalala ndi moyo? Kodi si paja anthu onse amapita kumalo amodzi?+  Ntchito yonse imene munthu amagwira mwakhama amagwirira pakamwa pake,+ koma zolakalaka zake sizitha.  Kodi pali ubwino wotani kukhala munthu wanzeru kusiyana ndi kukhala munthu wopusa?+ Kapena kodi pali phindu lanji kuti munthu wosauka amadziwa zimene angachite kuti akhale ndi moyo?*  Ndi bwino kusangalala ndi zinthu zimene maso ako akuona kuposa kulakalaka zinthu zimene sungazipeze.* Izinso nʼzachabechabe ndipo zili ngati kuthamangitsa mphepo. 10  Chilichonse chimene chinakhalapo chinapatsidwa kale dzina ndipo nʼzodziwika kuti munthu ndi ndani. Iye sangathe kutsutsana* ndi amene ali wamphamvu kuposa iyeyo. 11  Mawu akachuluka* zinthu zachabechabe zimachulukanso, ndiye kodi munthu zimamupindulitsa chiyani? 12  Ndi ndani akudziwa zinthu zabwino zimene munthu angachite pa masiku ochepa a moyo wake wachabechabe, umene umakhala ngati mthunzi?+ Chifukwa ndi ndani angauze munthu zimene zidzachitike padziko lapansi pano iyeyo atafa?

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Pali tsoka limene.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “akupumula kwambiri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amadziwa kuyenda pamaso pa anthu amoyo.”
Kapena kuti, “kuposa kulakalaka ndi mtima.”
Kapena kuti, “kudziteteza pa mlandu wotsutsana.”
Mabaibulo ena amati, “Zinthu zikachuluka.”