Mlaliki 9:1-18

  • Anthu onse mapeto awo ndi ofanana (1-3)

  • Uzisangalala ndi moyo ngakhale kuti udzafa (4-12)

    • Akufa sadziwa chilichonse (5)

    • Ku Manda kulibe kugwira ntchito (10)

    • Nthawi yatsoka komanso zinthu zosayembekezereka (11)

  • Si nthawi zonse pamene anthu amayamikira munthu wanzeru (13-18)

9  Choncho ndinaganizira zinthu zonsezi mumtima mwanga ndipo ndinaona kuti anthu olungama, anthu anzeru limodzi ndi ntchito zawo ali mʼmanja mwa Mulungu woona.+ Anthu sakudziwa za chikondi kapena chidani chimene chinalipo iwo asanakhalepo.  Anthu onse mapeto awo ndi ofanana,+ munthu wolungama komanso munthu woipa,+ munthu wabwino ndi woyera komanso munthu wodetsedwa, munthu amene amapereka nsembe komanso amene sapereka nsembe. Munthu wabwino nʼchimodzimodzi ndi munthu wochimwa. Munthu amene amachita lumbiro nʼchimodzimodzi ndi amene amaganiza kaye asanachite lumbiro.  Chinthu chomvetsa chisoni chimene chimachitika padziko lapansi pano ndi ichi: Chifukwa chakuti mapeto a anthu onse ndi ofanana,+ mitima ya anthu ndi yodzaza ndi zoipa. Mumtima mwawo mumakhala misala pa nthawi imene ali ndi moyo ndipo kenako amafa.  Aliyense amene ali pakati pa anthu amoyo ali ndi chiyembekezo, chifukwa galu wamoyo ali bwino kuposa mkango wakufa.+  Chifukwa amoyo amadziwa kuti adzafa,+ koma akufa sadziwa chilichonse+ komanso salandira mphoto iliyonse,* chifukwa zonse zimene anthu akanawakumbukira nazo zimaiwalika.+  Komanso chikondi chawo, chidani chawo ndi nsanje yawo zatha kale, ndipo alibenso gawo lililonse pa zimene zikuchitika padziko lapansi pano.+  Pita ukadye chakudya chako mokondwera ndipo ukamwe vinyo wako ndi mtima wosangalala,+ chifukwa Mulungu woona wasangalala kale ndi ntchito zako.+  Nthawi zonse zovala zako zizikhala zoyera* ndipo usamalephere kudzola mafuta kumutu kwako.+  Sangalala ndi moyo limodzi ndi mkazi wako amene umamukonda+ masiku onse a moyo wako wachabechabe, amene Mulungu wakupatsa padziko lapansi pano. Usangalale masiku ako onse achabechabe, chifukwa imeneyi ndi mphoto imene* ukuyenera kulandira pa moyo wako komanso pa ntchito yovuta imene ukuigwira mwakhama padziko lapansi pano.+ 10  Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse, chifukwa ku Manda*+ kumene ukupitako kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu kapena nzeru. 11  Ndaonanso chinthu china padziko lapansi pano kuti si nthawi zonse pamene anthu othamanga kwambiri amapambana pampikisano komanso pamene amphamvu amapambana pankhondo.+ Si nthawi zonse pamene anthu ochenjera amapeza chakudya, ndiponso si nthawi zonse pamene anthu anzeru amakhala ndi chuma.+ Komanso anthu odziwa zinthu, si nthawi zonse pamene zinthu zimawayendera bwino,+ chifukwa nthawi yatsoka komanso zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo. 12  Chifukwa munthu sadziwa nthawi imene tsoka lingamugwere.+ Mofanana ndi nsomba zimene zimagwidwa mu ukonde wakupha, komanso mbalame zimene zimagwidwa mumsampha, ana a anthu nawonso amakodwa pa nthawi yatsoka, tsokalo likawagwera mwadzidzidzi. 13  Padziko lapansi pano ndinaonaponso zinthu izi zokhudza nzeru ndipo ndinagoma nazo: 14  Panali mzinda winawake waungʼono ndipo munali amuna ochepa. Kenako kunabwera mfumu yamphamvu ndipo inazungulira mzindawo nʼkuunjika milu ikuluikulu yadothi yoti imenyerepo nkhondo. 15  Mumzindawo munali munthu wosauka koma wanzeru ndipo anapulumutsa mzindawo chifukwa cha nzeru zakezo. Koma palibe aliyense amene anakumbukira munthu wosaukayo.+ 16  Choncho ndinaganiza kuti: ‘Nzeru nʼzabwino kuposa mphamvu,+ koma anthu amanyoza nzeru za munthu wosauka ndipo samvera mawu ake.’+ 17  Ndi bwino kumvera mawu odekha a munthu wanzeru kusiyana ndi mawu ofuula a munthu amene akulamulira pakati pa anthu opusa. 18  Nzeru nʼzabwino kuposa zida zankhondo, koma wochimwa mmodzi yekha akhoza kuwononga zabwino zochuluka.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “malipiro aliwonse.”
Zimenezi ndi zovala zowala zosonyeza kuti munthu akusangalala osati zovala za pamaliro.
Kapena kuti, “limeneli ndi gawo limene.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.